Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Nehemiya 4-7

Adani a Nehemiya pa Ntchito Yake

Sanibalati atamva kuti tikumanganso khoma anapsa mtima nayamba kuseka ndi kunyogodola Ayuda kwambiri. Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, “Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?”

Tobiya wa ku Amoni, amene anali naye anati, “Chimene akumangacho ngati nkhandwe itakwerapo, itha kugwetsa khoma lawolo!”

Tsono ndinayamba kupemphera kuti, “Timvereni, Inu Mulungu wathu, mmene akutinyozera. Mulole kuti mawu awo onyoza awabwerere, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo. Musawakhululukire mphulupulu zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu popeza aputa ukali wanu pamaso pa anthu omanga khoma.”

Choncho ife tinamangabe khomalo kufikira lonse litafika theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu anagwira ntchitoyo ndi mtima wawo wonse.

Koma pamene Sanibalati, Tobiya, Aarabu, Aamoni ndi anthu a ku Asidodi anamva kuti ntchito yokonzanso makoma a Yerusalemu ikupitirirabe ndipo kuti mipata ikutsekedwa, anapsa mtima kwambiri. Tsono onse anapangana za chiwembu kuti abwere ndi kudzathira nkhondo anthu a ku Yerusalemu ndi kuyambitsa mapokoso pakati pawo. Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinayika alonda otiteteza kwa adaniwo usiku ndi usana.

10 Pa nthawi yomweyi anthu a ku Yuda anati, “Mphamvu za anthu onyamula zinyalala zikutha ndipo pali zinyalala zambiri. Choncho ife sititha kumanga khomali.”

11 Adani athunso anati, “Iwo asanadziwe izi, kapena kutiona, tidzakhala tili pakati pawo ndipo tidzawapha ndi kuyimitsa ntchitoyo.”

12 Ndipo Ayuda amene ankhala pafupi ndi adani athuwo anabwera kakhumi konse kuchokera konse kumene ankakhala kudzatiwuza kuti tibwereko ku ntchito.

13 Choncho kumbuyo kwa khoma, cha mʼmunsi mwake komanso malo amene anali asanathe ndinayikamo anthu mʼmabanja atatenga malupanga, mikondo ndi mauta awo. 14 Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”

15 Adani athu atamva kuti ife tadziwa za chiwembu chawo, anadziwanso kuti Yehova walepheretsa zimene ankafuna kutichita. Choncho tinabwerera aliyense ku ntchito yake yomanga khoma.

16 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo mwake, theka la antchito anga linkagwira ntchito, pamene theka linalo limatenga mikondo, zishango, mauta ndi kuvala malaya azitsulo. Akuluakulu ankalimbikitsa Ayuda onse 17 amene ankamanga khoma. Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, dzanja linali atanyamula chida chankhondo. 18 Mʼmisiri aliyense ankamangirira lupanga lake mʼchiwuno mwake akamagwira ntchito. Koma munthu woyimba lipenga anali pambali panga nthawi zonse.

19 Ndipo ine ndinati kwa anthu olemekezeka ndi anthu ena onse, “Ntchitoyi ndi yayikulu ndipo ili padera lalikulu ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma. 20 Tsono kulikonse kumene muliko, mukamva kulira kwa lipenga bwerani mudzasonkhane kumene kuli ine kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”

21 Choncho enafe tinapitiriza kugwira ntchito, pamene theka lina linkanyamula mikondo kuyambira mʼbandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka. 22 Pa nthawi imeneyo ndinawuzanso anthuwo kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone mu Yerusalemu kuti tikhale ndi otilondera usiku ndi kuti masana tizigwira ntchito.” 23 Choncho ine, anzanga, antchito anga, ndi anthu otiteteza amene ankanditsata panalibe ndi mmodzi yemwe anavula zovala zake pogona. Aliyense anasunga chida chake chankhondo pambali pake.

Nehemiya Ateteza Anthu Aumphawi

Tsono anthu ena ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzawo. Ena ankanena kuti, “Ife ndi ana athu aamuna ndi aakazi, tilipo ochuluka kwambiri. Choncho tikufuna tirigu kuti tidye ndi kukhala ndi moyo.”

Panali ena amene ankanena kuti, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu ya mphesa ndi nyumba zathu ngati chikole kuti tipeze tirigu chifukwa njala yakula.”

Panalinso ena amene ankanena kuti, “ife tinachita kukongola ndalama zoti tipereke msonkho wa minda ndi mitengo yathu ya mphesa kwa mfumu. Ngakhale kuti ndife amodzi ndi abale athuwa, ndipo ngakhalenso ana athu ndi ofanana ndi ana awo, ife tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo. Ena mwa ana athu aakazi atengedwa kale ukapolo. Ife tilibe mphamvu yochitapo kanthu popeza anthu ena anatenga kale minda yathu ndi mitengo yathu ya mphesa.”

Nditamva madandawulo awo ndi zimene amanenazi ndinapsa mtima kwambiri. Nditalingalira bwino ndinatsimikiza zoti ndichitepo kanthu ndipo kenaka ndinawadzudzula anthu olemekezeka ndi akuluakuluwo. Ndinawawuza kuti, “Zoona ndithu inu nʼkumalipiritsana chiwongoladzanja chachikulu anthu apachibale nokhanokha!” Choncho ndinayitanitsa msonkhano waukulu kuti ndiwazenge mlandu ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene.

Kotero ndinapitiriza kunena kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi inu simungakhale ndi moyo woopa Mulungu wathu kuti tipewe kunyoza kwa adani athu, anthu a mitunda inayi? 10 Ine ndi abale anga ndiponso antchito anga tikuwakongozanso anthuwa ndalama ndi tirigu. Ndipo tiyeni tilekeretu zolandira chiwongoladzanja! 11 Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.”

12 Iwo anayankha kuti, “Ife tidzawabwezera zimenezi popanda kupemphapo kanthu kalikonse kwa iwo. Tidzachita monga mwanena.”

Pambuyo pake ndinayitanitsa ansembe ndipo pamaso pawo ndinawalumbiritsa atsogoleriwo ndi akuluakuluwo kuti adzachitadi zomwe analonjezazo. 13 Ndipo inenso ndinakutumula chovala changa ndi kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu wosasunga malonjezano ake. Amulande nyumba yake ndi katundu wake ndi kumusandutsa mʼmphawi!”

Apo msonkhano wonse unati, “Ameni” natamanda Yehova. Ndipo anthu aja anachita monga analonjezera.

14 Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. 15 Koma abwanamkubwa akale ankasautsa anthu. Iwo ankalanda anthu chakudya ndi vinyo ndi kuwalipiritsanso masekeli asiliva makumi anayi. Ngakhalenso antchito awo amavutitsa anthu kwambiri. Koma ine sindinachite zimenezo chifukwa ndimaopa Mulungu. 16 Ndiponso ndinadzipereka kugwira ntchito yomanga khoma la mzinda wa Yerusalemu popanda ngakhale kugulapo munda. Antchito anganso anasonkhana komweko kuti agwire ntchito ndipo sitinafunenso malo ena.

17 Kuwonjezera apa, ndinkadyetsa Ayuda, akuluakulu kuphatikizanso anthu amene ankabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ya anthu otizungulira okwanira 150. 18 Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu.

19 Kuti zinthu zindiyendere bwino, kumbukirani Yehova Mulungu wanga pa zonse zimene ndachitira anthu awa.

Adani Apitiriza Kutsutsa ndi Kuopseza Nehemiya

Pamenepo Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndi adani athu anamva kuti ndatsiriza ntchito yomanganso khoma ndi kuti palibe mpata umene watsala ngakhale kuti pa nthawi imeneyi ndinali ndisanayike zitseko pa zipata. Sanibalati ndi Gesemu, ananditumizira uthenga uwu: “Bwerani tidzakumane pa mudzi wina ku chigwa cha Ono.”

Koma iwo anakonzekera kuti akandichite chiwembu kumeneko. Choncho ine ndinatuma amithenga ndi yankho ili: “Ine ndikugwira ntchito yayikulu kuno ndipo sindingathe kubwera kumeneko. Kodi ntchito iyime pofuna kuti ndibwere kumeneko?” Ananditumizira uthenga umodzimodzi omwewu kanayi ndipo ndinawayankha chimodzimodzi.

Tsono kachisanu, Sanibalati anatumiza wantchito wake ndi kalata yosamata. Mu kalatamo munali mawu akuti,

“Pali mphekesera pakati pa mitundu ya anthu, ndiponso Gesemu akunena zomwezo kuti inu ndi Ayuda onse mufuna kuwukira boma. Nʼchifukwa chake mukumanga khoma. Mphekeserazo zikutinso inu mukufuna kudzakhala mfumu yawo. Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.”

Ine ndinatumiza yankho ili: “Pa zimene mukunenazo, palibe chimene chinachitikapo. Inu mukungozipeka mʼmutu mwanu.”

Apa adani athu onsewa ankangofuna kutiopseza. Iwo ankaganiza kuti “Tichita mantha ndi kuleka kugwira ntchito.”

Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu ndilimbitseni mtima.”

10 Tsiku lina ndinapita ku nyumba ya Semaya mwana wa Delaya mwana wa Mehatabeli. Tsono anandiwuza kuti, “Tiyeni tikakumanire ku Nyumba ya Mulungu. Tikabisale mʼmenemo ndi kutseka zitseko chifukwa akubwera kudzakuphani. Ndithu usiku uno akubwera kudzakuphani.”

11 Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!” 12 Ndinazindikira kuti Mulungu sanamutume koma kuti anayankhula mawu oloserawa motsutsana nane chifukwa Tobiya ndi Sanibalati anamulemba ntchitoyi. 13 Iye analembedwa ntchitoyi ndi cholinga choti ine ndichite mantha, ndithawe. Ndikanatero ndiye kuti ndikanachimwira Yehova ndiponso iwowo akanandiyipitsira mbiri yanga ndi kumandinyoza.

14 Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobiya ndi Sanibalati chifukwa cha zimene achita. Kumbukiraninso mneneri wamkazi Nowadiya ndi aneneri amene akhala akufuna kundiopseza.”

Kutsiriza kwa Khoma

15 Ndipo khoma linatsirizidwa kumanga pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli. Linamangidwa pa masiku okwana 52. 16 Adani athu onse atamva izi, mitundu yonse ya anthu yozungulira inachita mantha ndi kuchita manyazi. Iwo anazindikira kuti ntchitoyo inachitika ndi thandizo la Mulungu wathu.

17 Komanso masiku amenewo anthu olemekezeka a ku Yuda ankalemberana naye makalata ambiri ndi Tobiyayo, 18 pakuti anthu ambiri a ku Yuda anali atalumbira kale kuti adzagwira naye ntchito popeza anali mkamwini wa Sekaniya mwana wa Ara, ndipo mwana wake Yehohanani anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya. 19 Kuwonjezera apo, anthu ankasimba za ntchito zake zabwino ine ndili pomwepo ndipo anakamuwululira mawu anga. Choncho Tobiyayo ankatumiza makalata ondiopseza.

Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

Zidzukulu za Parosi2,172
Zidzukulu za Sefatiya372
10 Zidzukulu za Ara652
11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)2,818
12 Zidzukulu za Elamu1,254
13 Zidzukulu za Zatu845
14 Zidzukulu za Zakai760
15 Zidzukulu za Binuyi648
16 Zidzukulu za Bebai628
17 Zidzukulu za Azigadi2,322
18 Zidzukulu za Adonikamu667
19 Zidzukulu za Abigivai2,067
20 Zidzukulu za Adini655
21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98
22 Zidzukulu za Hasumu328
23 Zidzukulu za Bezayi324
24 Zidzukulu za Harifu112
25 Zidzukulu za Gibiyoni95.
26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa188
27 Anthu a ku Anatoti128
28 Anthu a ku Beti-Azimaveti42
29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti743
30 Anthu a ku Rama ndi Geba621
31 Anthu a ku Mikimasi122
32 Anthu a ku Beteli ndi Ai123
33 Anthu a ku Nebo winayo52
34 Ana a Elamu wina1,254
35 Zidzukulu za Harimu320
36 Zidzukulu za Yeriko345
37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono721
38 Zidzukulu za Senaya3,930.

39 Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa)973
40 Zidzukulu za Imeri1,052
41 Zidzukulu za Pasi-Huri1,247
42 Zidzukulu za Harimu1,017.

43 Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya74.

44 Anthu oyimba:

Zidzukulu za Asafu148.

45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai138.

46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni
48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,
49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,
50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,
51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,
52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,
53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema
56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

57 Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za
Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida
58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu
zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.
60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo392.

61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

62 Zidzukulu za
Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda642.

63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za

Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Machitidwe a Atumwi 2:22-47

22 “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. 23 Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. 24 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa. 25 Pakuti Davide ananena za Iye kuti,

“ ‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse.
    Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja,
    Ine sindidzagwedezeka.
26 Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera;
    thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
27 Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda,
    kapena kulekerera Woyerayo kuti awole.
28 Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo;
    Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’

29 “Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino. 30 Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu. 31 Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. 32 Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi. 33 Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi. 34 Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti,

“ ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti:
    Khala kudzanja langa lamanja
35 mpaka nditasandutsa adani ako
    kukhala chopondapo mapazi ako.’

36 “Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”

37 Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”

38 Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39 Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”

40 Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.” 41 Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.

Kuyanjana kwa Okhulupirira

42 Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera. 43 Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. 44 Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. 45 Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. 46 Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona. 47 Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.