Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezara 9-10

Pemphero la Ezara pa za Kukwatirana ndi a Mitundu Ina

Zitachitika izi, atsogoleri anabwera kwa ine nati, “Aisraeli, kuphatikizanso ansembe ndi Alevi, sanadzipatule ku makhalidwe onyansa a anthu a mitundu ina amene ayandikana nafe: Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aigupto ndi Aamori. Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.”

Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa. Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.

Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga ndipo ndinapemphera kuti,

“Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo. Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu.

“Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu. Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu.

10 “Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, kodi tinganene chiyani titachita zoyipa zonsezi? Ife taphwanya malamulo anu 11 amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa. 12 Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’

13 “Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke, 14 kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka? 15 Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”

Anthu Avomereza Tchimo Lawo

10 Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri. Ndipo Sekaniya, mwana wa Yehieli, wa fuko la Elamu, anawuza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mayiko akunowa. Koma ngakhale zili chomwechi, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraeli. Tsopano tiyeni tichite naye pangano Mulungu wathu, kuti tichotse akazi onsewa ndi ana awo, potsata malangizo a inu mbuye wanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Lolani kuti zichitike motsatira malamulo. Tsono dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu. Ife tikuthandizani. Limbani mtima ndipo gwirani ntchitoyi.”

Choncho Ezara anayimirira ndipo analumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraeli onse, kuti adzachitedi monga Sekaniya ananenera. Tsono onse analumbira. Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.

Tsono anthu analengeza mʼdziko lonse la Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Yerusalemu kwa onse ochokera ku ukapolo aja kuti asonkhane ku Yerusalemu. Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.

Choncho anthu onse a mʼdziko la Yuda ndi a mʼdziko la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onse anakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu akunjenjemera chifukwa cha mvula yambiri imene inagwa. 10 Ndipo wansembe Ezara anayimirira nawuza anthuwo kuti, “Inu mwachimwa pomakwatira akazi achikunja ndi kumawonjezera pa tchimo la Aisraeli. 11 Tsopano lapani kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu ndi kuchita zimene akufuna. Dzipatuleni kwa anthu a mayiko enawa ndi kwa akazi achikunjawa.”

12 Gulu lonse la anthu linayankha ndi mawu ofuwula kuti, “Nʼzoona! Tichita monga mwaneneramu. 13 Koma pano pali anthu ambiri ndiponso mvula ikugwa kwambiri, choncho sitingakayime panja. Ndiponso ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena awiri, chifukwa tachimwa kwambiri pa zimene tachitazi. 14 Tsono mulole kuti atsogoleri athu ayimirire mʼmalo mwa anthu onse. Aliyense wa mʼmizinda yathu amene anakwatira mkazi wachikunja abwere pa nthawi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akuluakulu ndi oweruza a mzindawo. Choncho mkwiyo wa Mulungu wathu udzatichoka.” 15 Koma Yonatani yekha mwana wa Asaheli ndi Yahazieli mwana wa Tikiva ndiwo anatsutsapo pa zimenezi. Tsono Mesulamu ndi Mlevi Sebetai anawayikira kumbuyo.

16 Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja anachita zimene zimafunika. Ndipo wansembe Ezara anasankha amuna amene anali atsogoleri a mabanja potsata mafuko awo ndipo onsewo analembedwa mayina awo. Tsiku loyamba la mwezi wa khumi anayambapo kuyifufuza nkhani imeneyi. 17 Ndipo pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba anali atathana nawo anthu amene anakwatira akazi achilendo aja.

Okwatira Akazi Achilendo

18 Nawu mʼndandanda wa ansembe amene anakwatira akazi achikunja:

Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali awa: Maaseiya, Eliezara, Yaribu ndi Gedaliya. 19 Iwo anatsimikiza zochotsa akazi awo ndipo chifukwa cha kulakwa kwawo aliyense anapereka nkhosa yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.

20 Pa banja la Imeri panali awa:

Hanani ndi Zebadiya.

21 Pa banja la Harimu panali awa:

Maseya, Eliya, Semaya, Yehieli ndi Uziya.

22 Pa banja la Pasuri panali awa:

Eliyoenai, Maseya, Ismaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa.

23 Pakati pa Alevi panali:

Yozabadi, Simei, Kelaya (ndiye kuti, Kelita). Petaya, Yuda ndi Eliezara.

24 Pakati pa oyimba nyimbo panali

Eliyasibu.

Ochokera kwa alonda a zipata:

Salumu, Telemu ndi Uri.

25 Ochokera pakati pa Aisraeli ena:

a fuko la Parosi anali

Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, ndi Benaya.

26 A fuko la Elamu anali

Mataniya, Zekariya, Yehieli, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.

27 A fuko la Zatu anali

Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza.

28 A fuko la Bebai anali

Yehohanani, Hananiya, Zabayi ndi Atilayi.

29 A fuko la Bani anali

Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubu, Seali ndi Yeremoti.

30 A fuko la Pahati-Mowabu anali

Adina, Kelali, Benaya, Maseya, Mataniya, Bezaleli, Binuyi ndi Manase.

31 A fuko la Harimu anali

Eliezara, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni, 32 Benjamini, Maluki ndi Semariya.

33 A fuko la Hasumu anali

Mataneyi, Matata, Zabadi, Elifeleti, Yeremayi, Manase ndi Simei.

34 A fuko la Bani anali

Madai, Amramu, Uweli, 35 Benaya, Bediya, Keluhi, 36 Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37 Mataniya, Matenayi ndi Yasu.

38 A fuko la Binuyi anali

Simei, 39 Selemiya, Natani, Adaya, 40 Makinadebayi, Sasai, Sarai, 41 Azaleli, Selemiya, Semariya, 42 Salumu, Amariya ndi Yosefe.

43 A fuko la Nebo anali

Yeiyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya.

44 Onsewa anakwatira akazi achilendo. Tsono anawasudzula akaziwo ndi kuwatumiza kwawo pamodzi ndi ana awo.

Machitidwe a Atumwi 1

Lonjezo la Mzimu Woyera

Mʼbuku langa loyamba, ndinakulembera iwe Teofilo zonse zimene Yesu anayamba kuchita ndi kuphunzitsa, mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha. Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi. Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani. Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”

Yesu Akwera Kumwamba

Atumwi atasonkhana pamodzi, iwo anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi nthawi ino mubwezeretsa ufumu kwa Israeli?”

Yesu anawawuza kuti, “Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo. Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo.

10 Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo. 11 Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”

Matiyasi Alowa Mʼmalo mwa Yudasi Isikarioti

12 Pamenepo atumwi anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri la Olivi, mtunda wosakwana kilomita kuchokera mu mzindamo. 13 Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo. 14 Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

15 Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120). 16 Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu. 17 Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”

18 (Yudasi anagula munda ndi ndalama zimene anazipeza pochita zoyipa zija; kumeneko, iye anagwa chamutu, naphulika pakati ndipo matumbo ake wonse anakhuthuka. 19 Aliyense mu Yerusalemu anamva zimenezi, kotero anatcha mundawo mʼchiyankhulo chawo kuti Akeledama, kutanthauza, Munda wa Magazi).

20 Petro anati, “Pakuti kwalembedwa mʼbuku la Masalimo kuti,

“Nyumba yake isanduke bwinja,
    ndipo pasakhale wogonamo.

Ndiponso,

“Wina atenge ntchito yake yautsogoleri.

21 Chifukwa chake ndi kofunika kusankha mmodzi wa anthu amene akhala nafe nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankayenda nafe, 22 kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”

23 Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi. 24 Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa 25 kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.” 26 Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.