Old/New Testament
Lamulo la Mfumu Dariyo
6 Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale. 2 Ndipo ku Ekibatana, likulu la dera la Mediya, kunapezeka mpukutu mmene munalembedwa kuti,
Chikumbutso:
3 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu.
Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27. 4 Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu. 5 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo.
6 Tsopano Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu muchokeko kumeneko. 7 Ntchito yomanga Nyumba ya Mulunguyi muyileke. Mulekeni bwanamkubwa wa Ayuda ndiponso akuluakulu a Ayuda kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake.
8 Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo:
Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate. 9 Ndipo zonse zofunikira monga, ana angʼombe, nkhosa zazimuna, ana ankhosa aamuna zoperekera nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba, ndi tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta monga mmene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziwapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku ndipo musamalephere kutero. 10 Zikatero ndiye kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu wakumwamba ndi kupempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.
11 Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala. 12 Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko.
Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.
Kutsiriza ndi Kupereka Nyumba ya Mulungu
13 Tsono potsata zomwe analamula mfumu Dariyo, Tatenai bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzawo anatsatira mosamala kwambiri zimene mfumu Dariyo analamula. 14 Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya. 15 Anatsiriza kumanga Nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara mʼchaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariyo.
16 Choncho Aisraeli, ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, anachita chikondwerero chopereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe. 17 Poporeka Nyumba ya Mulunguyi, anthu anapereka nsembe za ngʼombe zazimuna 100, nkhosa zazimuna 200, ana ankhosa aamuna 400. Anaperekanso mbuzi zazimuna 12 ngati nsembe yopepesera machimo a anthu onse, potsata chiwerengero cha mafuko a Israeli. 18 Ndipo anakhazikitsa ansembe ndi Alevi pa ntchito zawo zotumikira Mulungu mu Yerusalemu monga zinalembedwera mʼbuku la Mose.
Paska
19 Pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba, obwera ku ukapolo aja anachita chikondwerero cha Paska. 20 Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa ndipo onsewo anali oyeretsedwa. Alevi anapha mwana wankhosa wa Paska kuphera onse amene anatuluka ku ukapolo, ansembe anzawo ndi iwo eni. 21 Nkhosa ya Paskayo anayidya ndi Aisraeli onse amene anatuluka ku ukapolo, wina aliyense amene anaphatikana nawo atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja a mʼdzikomo kuti apembedze Yehova Mulungu wa Israeli. 22 Choncho pa masiku asanu ndi awiri anasangalala pa chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa Yehova anawadzaza ndi chimwemwe. Iye anatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya motero kuti iyo inakomera mtima Aisraeli ndi kuwathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israeli.
Ezara Abwera ku Yerusalemu
7 Zitatha izi, Aritasasita ali mfumu ya ku Perisiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu abambo ake anali Seraya mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya, 2 mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi, 3 mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Merayoti, 4 mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki, 5 mwana wa Abisuwa, mwana wa Finehasi, mwana wa Eliezara, mwana wa Aaroni mkulu wa ansembe uja. 6 Ezara ameneyu anabwera kuchokera ku Babuloni. Iyeyu anali wophunzira kwambiri za malamulo a Mose, amene Yehova Mulungu wa Israeli anapereka. Mfumu inamupatsa chilichonse chimene anapempha pakuti dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye. 7 Tsono mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wa Aritasasita, Ezara pamodzi ndi Aisraeli ena, kuphatikizapo ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda, ndi anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ananyamuka kubwerera ku Yerusalemu.
8 Ezara anafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu. 9 Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye. 10 Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.
Kalata ya Aritasasita Yopita kwa Ezara
11 Iyi ndi kalata imene mfumu Aritasasita anapereka kwa wansembe Ezara, mlembi wa malamulo, munthu wophunzira kwambiri zokhudza malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli.
12 Ndine Aritasasita, mfumu ya mafumu.
Ndikulembera iwe Ezara wansembe ndi mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba.
Malonje.
13 Tsopano ndikulamula kuti Mwisraeli aliyense, wansembe kapena Mlevi wokhala mʼdziko langa, amene akufuna kupita ku Yerusalemu ndi iwe, apite. 14 Ine mfumu pamodzi ndi alangizi anga asanu ndi awiri tikukutumani kuti mukafufuze za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu kuti mukaone mmene anthu akutsatira malamulo a Mulungu wanu, amene anawapereka kwa inu. 15 Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi alangizi anga tapereka mwa ufulu kwa Mulungu wa Israeli, amene amakhala ku Yerusalemu. 16 Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu. 17 Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
18 Ndalama zotsala mudzagwiritse ntchito zimene inuyo ndi abale anu zikakukomerani malingana nʼkufuna kwa Mulungu wanu. 19 Ziwiya zonse zimene akupatsani kuti mukatumikire nazo mʼNyumba ya Mulungu wanu, kaziperekeni kwa Mulungu ku Yerusalemu. 20 Ndipo chilichonse chimene chingafunike mʼNyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze mpata wopereka, ndalama zake zogulira zidzachokere mʼthumba la chuma cha mfumu.
21 Tsopano Ine, mfumu Aritasasita, ndikulamula asungichuma onse a dera la Patsidya pa Yufurate kuti, chilichonse chimene wansembe Ezara, mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba adzapempha kwa inu, mupatseni mwa msanga. 22 Ngakhale atafunika makilogalamu 3,400 asiliva, makilogalamu 10,000 a tirigu, malita 2,000 a vinyo, malita 2,000 a mafuta ndi mchere wochuluka motani, zonsezi mupereke monga zingafunikire. 23 Chimene Mulungu Wakumwamba walamula, chichitike mosamalitsa ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba kuopa kuti mkwiyo wa Mulungu ungayakire mfumu, dziko lake ndi ana ake. 24 Tikukudziwitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kukhometsa msonkho uliwonse anthu awa: ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda kapena aliyense wogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.
25 Ndipo iwe, Ezara, monga mwa nzeru za Mulungu wako zimene uli nazo, usankhe oyendetsa zinthu ndi oweruza kuti azilamulira anthu onse okhala ku dera la Patsidya pa Yufurate, onse amene amadziwa malamulo a Mulungu wako. Ndipo uphunzitse aliyense amene sawadziwa. 26 Ndipo amene sadzamvera lamulo la Mulungu wako ndi lamulo la mfumu alangidwe kolimba kapena aphedwe kapena achotsedwe mʼdzikolo, kapena katundu wake alandidwe, kapena aponyedwe mʼndende.
27 Ezara anati atamandike Yehova, Mulungu wa makolo athu, amene wayika ichi mu mtima wa mfumu kuti alemekeze Nyumba ya Yehova ya ku Yerusalemu mʼnjira imeneyi. 28 Ameneyonso waonetsa chikondi chake chosasinthika kwa ine pamaso pa mfumu, alangizi ake ndi nduna zake zamphamvu kuti andikomere mtima. Choncho ndinalimba mtima popeza Yehova, Mulungu wanga anali nane, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Israeli kuti apite nane pamodzi.
Mʼndandanda wa Akuluakulu a Mabanja Amene Anabwera ndi Ezara
8 Nawa mayina a atsogoleri a mabanja amene anabwera nane kuchokera ku Babuloni nthawi ya ulamuliro wa mfumu Aritasasita:
2 Geresomu wa fuko la Finehasi;
Danieli wa fuko la Itamara;
Hatusi 3 mwana wa Sekaniya wa fuko la Davide;
Zekariya wa fuko la Parosi. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwa anthu ena 150;
4 Elihunai mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahati-Mowabu. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu ena 400.
5 Sekaniya, mwana wa Yahazieli wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwanso anthu 300.
6 Ebedi, mwana wa Yonatani wa fuko la Adini. Pamodzi naye analembedwanso anthu ena makumi asanu.
7 Yesaiya, mwana wa Ataliya wa fuko la Elamu. Pamodzi naye panali anthu ena 70.
8 Zebadiya, mwana wa Mikayeli wa fuko la Sefatiya. Pamodzi naye panalinso anthu 80.
9 Obadiya, mwana wa Yehieli wa fuko la Yowabu. Pamodzi naye panalinso anthu 218.
10 Selomiti mwana wa Yosifiya wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu 160.
11 Zekariya, mwana wa Bebai wa fuko la Babai. Pamodzi naye analembedwanso anthu 28.
12 Yohanani, mwana wa Hakatani wa fuko la Azigadi. Pamodzi naye panalinso anthu 110.
13 Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene anabwera pambuyo pake mayina awo anali Elifeleti, Yeiyeli ndi Semaya. Pamodzi ndi iwowa panalinso anthu 60.
14 Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri. Pamodzi ndi iwowa panali anthu 70.
Kubwerera ku Yerusalemu
15 Anthu onse ndinawasonkhanitsa ku mtsinje umene umapita mpaka ku Ahava, ndipo kumeneko tinagona mʼmisasa masiku atatu. Nditayangʼana pakati pa anthu ndi ansembe, ndinapeza kuti panalibe Alevi. 16 Choncho ndinayitana atsogoleri awa: Eliezara, Arieli, Semaiya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi awiri, Yoyaribu ndi Elinatani, 17 ndipo ndinawatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ine ndinawawuza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu. 18 Chifukwa cha kutikomera mtima kwa Mulungu wathu, Ido anatitumizira munthu wanzeru, Serabiya, wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israeli, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi abale ake, anthu 18. 19 Anatitumiziranso Hasabiya ndi Yesaiya wa fuko la Merari pamodzi ndi abale ake ndi adzukulu ake, anthu makumi awiri. 20 Panalinso anthu ena 220 mwa anthu ogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amene Davide ndi nduna zake anawasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onsewa analembedwa potsata mayina awo.
21 Ku mtsinje wa Ahava, ndinalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kupempha kuti atiyendetse bwino ife ndi ana athu, ndi kuteteza katundu wathu yense. 22 Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.” 23 Choncho tinasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze ndipo Iye anamva pemphero lathu.
24 Tsono ndinasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi awiri awa, Serebiya, Hasabiya ndi abale awo khumi 25 ndipo ndinawayezera siliva ndi golide, ndiponso ziwiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi alangizi ake, nduna zake ndi Aisraeli onse amene anali kumeneko anazipereka. 26 Nditayeza zonse, ndinapereka mʼmanja mwawo, matani 22 asiliva, ziwiya zasiliva zolemera makilogalamu 70, ndiponso makilogalamu 3,400 a golide, 27 mbale zagolide makumi awiri zolemera makilogalamu asanu ndi atatu ndi theka ndiponso ziwiya ziwiri zamkuwa wosalala, wonyezimira bwino ngati golide wamtengowapatali.
28 Kenaka ndinawawuza kuti, “Inu ndi opatulika a Yehova, ndiponso mphatso zonsezi ndi zopatulika. Siliva ndi golideyu ndi zopereka zaufulu kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu. 29 Muzisamale bwino mpaka mutaziyeza pamaso pa atsogoleri a ansembe ndi Alevi ndi akulu a mabanja a Israeli mʼzipinda za mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu.” 30 Choncho ansembe ndi Alevi analandira zonse zoyezedwa zija, siliva, golide pamodzi ndi ziwiya kuti apite nazo ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.
31 Pa tsiku la khumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, tinachoka ku mtsinje wa Ahava kupita ku Yerusalemu. Ndipo Mulungu wathu anali nafe, ndipo anatiteteza kwa adani athu makamaka otibisalira pa njira. 32 Tinafika ku Yerusalemu, komwe tinapumula masiku atatu.
33 Pa tsiku la chinayi lake, mʼNyumba ya Mulungu wathu, tinayeza siliva ndi golide ndi ziwiya zija nʼkuzipereka mʼmanja mwa Meremoti mwana wa wansembe Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eliezara mwana wa Finehasi ndiponso Alevi awa: Yozabadi mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binuyi. 34 Zonsezi anaziwerenga ndi kuziyeza ndipo analemba kulemera kwa chinthu chilichonse.
35 Pamenepo anthu amene anatengedwa ukapolo aja anabwerera, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israeli: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, kuperekera Aisraeli onse, nkhosa zazimuna 96, ana ankhosa 77, ndiponso mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri ngati nsembe yopepesera machimo. Zonsezi zinali nsembe yopsereza zopereka kwa Yehova. 36 Iwo anaperekanso chidziwitso cha mfumu chija kwa akuluakulu a mfumu ndi kwa akazembe a mʼdera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwo anathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya
21 Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: 2 Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. 3 Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
4 Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.
5 Yesu anawafunsa iwo kuti, “Anzanga, kodi muli nsomba?”
Iwo anayankha kuti, “Ayi.”
6 Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.
7 Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. 8 Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. 9 Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.
10 Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.”
11 Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike. 12 Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye. 13 Yesu anabwera, natenga buledi ndikuwapatsa iwo, ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsomba. 14 Aka kanali tsopano kachitatu Yesu akuonekera kwa ophunzira ake Iye ataukitsidwa kwa akufa.
Yesu Abwezeretsa Petro
15 Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?”
Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.”
16 Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”
Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”
17 Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”
Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga. 18 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.” 19 Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”
20 Petro anatembenuka ndi kuona kuti ophunzira amene Yesu amamukonda amawatsatira iwo. (Uyu ndi amene anatsamira pachifuwa cha Yesu pa chakudya chamadzulo ndipo iye anati, “Ambuye, kodi ndi ndani amene adzakuperekani Inu?” 21 Petro atamuona iye, anafunsa kuti, “Ambuye, nanga uyu?”
22 Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.” 23 Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”
24 Uyu ndi wophunzira amene akuchitira umboni ndipo ndi amene analemba. Ife tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
25 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anachita. Zikanalembedwa zonsezi, ndikhulupirira dziko lonse lapansi likanasowa malo osungirako mabuku onse amene akanalembedwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.