Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezara 1-2

Koresi Athandiza Ayuda Kubwerera Kwawo

Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.

Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti,

“ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda. Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu. Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”

Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu. Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija. Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake. Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.

Chiwerengerochi chinali motere:

Mabeseni agolide30
mabeseni asiliva1,000
a zopereka29
10 timiphika tagolide230
timiphika tasiliva410
ziwiya zina1,000.

11 Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.

Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera

Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).

Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:

Zidzukulu za Parosi2,172
zidzukulu za Sefatiya372
zidzukulu za Ara775
zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu)2,812
zidzukulu za Elamu1,254
zidzukulu za Zatu945
zidzukulu za Zakai760
10 zidzukulu za Bani642
11 zidzukulu za Bebai623
12 zidzukulu za Azigadi1,222
13 zidzukulu za Adonikamu666
14 zidzukulu za Bigivai2,056
15 zidzukulu za Adini454
16 zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98
17 zidzukulu za Bezayi323
18 zidzukulu za Yora112
19 zidzukulu za Hasumu223
20 zidzukulu za Gibari95.
21 Anthu a ku Betelehemu123
22 Anthu aamuna a ku Netofa56
23 Anthu aamuna a ku Anatoti128
24 Anthu aamuna a ku Azimaveti42
25 Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti743
26 Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba621
27 Anthu aamuna a ku Mikimasi122
28 Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai223
29 Anthu aamuna a ku Nebo52
30 Anthu aamuna a ku Magaibisi156
31 Anthu aamuna a ku Elamu wina1,254
32 Anthu aamuna a ku Harimu320
33 Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono725
34 Anthu aamuna a ku Yeriko345
35 Anthu aamuna a ku Sena3,630.

36 Ansembe anali awa:

Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa)973
37 Zidzukulu za Imeri1,052
38 Zidzukulu za Pasuri1,247
39 Zidzukulu za Harimu1,017.

40 Alevi anali awa:

Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya)74.

41 Anthu oyimba nyimbo anali awa:

Zidzukulu za Asafu128.

42 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai139.

43 Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
44 zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
45 zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
46 zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
47 zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
48 zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
49 zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
50 zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
51 zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
52 zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
53 zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
54 zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.

55 Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:

Zidzukulu za
Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
56 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
57 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,
zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
58 Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali392.

59 Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:

60 Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali652.

61 Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:

Zidzukulu za
Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)

62 Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63 Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.

64 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65 kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66 Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67 ngamira 435 ndi abulu 6,720.

68 Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69 Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.

70 Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.

Yohane 19:23-42

23 Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.

24 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge.”

Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati,

“Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo
    ndi kuchita maere pa zovala zangazo.”

Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.

25 Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. 26 Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, “Amayi nayu mwana wanu.” 27 Anawuzanso wophunzirayo kuti, “Nawa amayi ako.” Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.

Imfa ya Yesu

28 Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, “Ine ndili ndi ludzu.” 29 Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu. 30 Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.

31 Popeza linali Tsiku Lokonzekera ndipo tsiku linalo linali Sabata lapadera; Ayuda sanafune kuti mitembo ikhale pa mtanda pa Sabata, iwo anapempha Pilato kuti akathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo. 32 Chifukwa chake asilikali anabwera ndi kuthyola miyendo ya munthu oyamba amene anapachikidwa ndi Yesu ndipo kenaka ya winayo. 33 Koma atafika pa Yesu ndi kupeza kuti anali atamwalira kale, iwo sanathyole miyendo yake. 34 Mʼmalo mwake, mmodzi wa asilikaliwo anamubaya Yesu ndi mkondo mʼnthiti, ndipo nthawi yomweyo munatuluka magazi ndi madzi. 35 Munthu amene anaona izi wapereka umboni ndipo umboni wake ndi woona. Iye akudziwa kuti akunena choonadi kuti inunso mukhulupirire. 36 Zinthu izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe: “Palibe limodzi la mafupa limene lidzathyoledwa,” 37 ndi monga lemba linanso linena, “Iwo adzayangʼana Iye amene iwo anamubaya.”

Yesu Ayikidwa Mʼmanda

38 Kenaka, Yosefe wa ku Arimateyu anakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Tsono Yosefe anali wophunzira wa Yesu koma mobisa chifukwa iye ankaopa Ayuda. Atalandira chilolezo kwa Pilato, anakatsitsa mtembo wa Yesu. 39 Nekodimo, munthu amene poyamba pake anabwera kwa Yesu usiku, anatenga mafuta osakaniza ndi mure ndi aloe wolemera pafupifupi makilogalamu 32. 40 Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu nawukulunga pamodzi ndi zonunkhiritsa mu nsalu za mtundu woyera monga mwa mwambo wa maliro wa Ayuda. 41 Pamalo pamene anapachikidwa Yesu panali munda ndipo mʼmundamo munali manda atsopano mʼmene munali simunayikidwemo aliyense. 42 Chifukwa linali Tsiku la Ayuda Lokonzekera ndi kuti mandawo anali pafupipo, iwo anayika Yesu mʼmenemo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.