Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 19-20

19 Yehosafati, mfumu ya Yuda itabwerera mwamtendere ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu. Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”

Yehosafati Asankha Oweruza

Yehosafati anakakhala ku Yerusalemu, ndipo amayenda pakati pa anthu kuchokera ku Beeriseba mpaka ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anawatembenuzira kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. Iye anasankha oweruza mʼdzikomo, mu mzinda uliwonse wotetezedwa wa Yuda. Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo. Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.”

Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu. Iye anawalamula kuti, “Inu mutumikire mokhulupirika ndi mtima wanu wonse moopa Yehova. 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.

11 “Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”

Yehosafati Agonjetsa Mowabu ndi Amoni

20 Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati.

Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi). Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova.

Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano ndipo anati:

“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’

10 “Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11 Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12 Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.”

13 Anthu onse a Yuda, pamodzi ndi akazi awo ndi ana ndi makanda, anayima chilili pamaso pa Yehova.

14 Ndipo Mzimu wa Yehova unabwera pa Yahazieli mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyeli, mwana wa Mataniya Mlevi, chidzukulu cha Asafu, atayimirira mu msonkhano.

15 Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 16 Mawa mupite mukamenyane nawo. Adzakhala akubwera mokweza kudzera Njira ya Zizi, ndipo mukawapeza kumapeto kwa chigwa cha ku chipululu cha Yeruweli. 17 Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”

18 Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova. 19 Kenaka Alevi ena ochokera ku mabanja a Kohati ndi Kora anayimirira ndipo anatamanda Yehova Mulungu wa Israeli ndi mawu ofuwula kwambiri.

20 Mmamawa, ananyamuka kupita ku chipululu cha Tekowa. Akunyamuka, Yehosafati anayimirira ndipo anati, “Tandimverani ine anthu a Yuda ndi Yerusalemu! Khalani ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzatchinjirizidwa, khalani ndi chikhulupiriro mwa aneneri ake ndipo mudzapambana.” 21 Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti:

“Yamikani Yehova
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.”

22 Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa. 23 Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana.

24 Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge. 26 Tsiku lachinayi anasonkhana ku chigwa cha Beraka kumene anatamanda Yehova. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero.

27 Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo. 28 Iwo analowa mu Yerusalemu ndipo anapita ku Nyumba ya Mulungu akuyimba azeze, apangwe ndi malipenga.

29 Kuopsa kwa Mulungu kunali pa maufumu onse a mayiko amene anamva mmene Yehova anamenyera adani a Aisraeli. 30 Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse.

Kutha kwa Ufumu wa Yehosafati

31 Choncho Yehosafati analamulira Yuda. Iye anali wa zaka 35 pamene anakhala mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 25. Dzina la amayi ake linali Azuba mwana wa Sili. 32 Iye ankayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanapatuke pa zimenezi pakuti anachita zolungama pamaso pa Yehova. 33 Komabe malo opembedzerapo mafano sanachotsedwe ndipo anthu sanaperekebe mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo.

34 Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.

35 Zitapita izi, Yehosafati mfumu ya Yuda inachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Israeli, amene anachita zoyipa kwambiri. 36 Iye anagwirizana ndi Ahaziya kuti apange sitima zapamadzi zochitira malonda. Atazipanga zimenezi ku Ezioni-Geberi, 37 Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.

Yohane 13:21-38

Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake

21 Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”

22 Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. 23 Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake. 24 Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”

25 Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”

26 Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni. 27 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.

Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” 28 Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. 29 Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. 30 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku.

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31 Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32 Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.

33 “Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.

34 “Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35 Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”

36 Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?”

Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”

37 Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”

38 Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.