Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 10-12

Aisraeli Awukira Rehobowamu

10 Rehobowamu anapita ku Sekemu, pakuti Aisraeli onse anapita kumeneko kuti akamulonge ufumu. Yeroboamu mwana wa Nebati atamva zimenezi (Iye anali ku Igupto, kumene anapita pothawa mfumu Solomoni) anabwerako kuchokera ku Igupto. Kotero anthu anakayitana Yeroboamu ndipo iye ndi Aisraeli onse anapita kwa Rehobowamu ndi kumuwuza kuti, “Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma tsopano mutipeputsire ntchito yolemetsayi ndi goli lolemerali limene analiyika pa ife ndipo ifeyo tidzakutumikirani.”

Rehobowamu anayankha kuti, “Mukabwerenso pakapita masiku atatu.” Choncho anthuwo anachoka.

Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?”

Iwo anayankha kuti, “Ngati inu muwakomera mtima anthu awa ndi kuwasangalatsa ndiponso kuwayankha mawu abwino, iwo adzakutumikirani nthawi zonse.”

Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira. Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ndi otani? Kodi tiwayankhe chiyani anthu amene akunena kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anayika pa ife?’ ”

10 Anyamata amene anakula pamodzi naye anamuyankha kuti, “Anthu amene anena kwa inu kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma inu mupeputse goli lathu,’ muwawuze kuti, ‘Chala changa chachingʼono ndi chachikulu kuposa chiwuno cha abambo anga. 11 Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’ ”

12 Tsiku lachitatu Yeroboamu ndi anthu onse anabwerera kwa Rehobowamu monga ananenera mfumu kuti, “Mukabwerenso kwa ine pakapita masiku atatu.” 13 Mfumu inawayankha mwankhanza, pokana malangizo a akuluakulu aja. 14 Iye anatsatira malangizo a anyamata ndipo anati, “Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.” 15 Kotero mfumu sinamvere anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Mulungu, kukwaniritsa mawu amene Yehova ananena kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.

16 Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kuwamvera, iwo anayankha mfumu kuti,

“Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide,
    gawo lanji mwa mwana wa Yese?
Inu Aisraeli! Pitani kwanu.
    Iwe Davide! Yangʼana banja lako.”

Kotero Aisraeli onse anapita kwawo. 17 Koma Rehobowamu anakhala akulamulirabe Aisraeli amene amakhala mʼmizinda ya Yuda.

18 Mfumu Rehobowamu inatuma Hadoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli anamugenda miyala ndi kumupha. Koma mfumu Rehobowamu anakwera galeta lake ndi kuthawira ku Yerusalemu. 19 Motero Israeli wakhala akuwukira banja la Davide mpaka lero lino.

11 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu anasonkhanitsa asilikali 180,000 a fuko la Yuda ndi Benjamini kuti akachite nkhondo ndi Israeli, kuti abwezeretse ufumu kwa Rehobowamu.

Koma Yehova anayankhula ndi munthu wa Mulungu Semaya kuti, “Kawuze Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Aisraeli onse ali mu Yuda ndi Benjamini kuti, ‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu. Pitani kwanu, aliyense wa inu, pakuti izi ndikuchita ndine.’ ” Choncho anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera osapita kukamenyana ndi Yeroboamu.

Rehobowamu Akhwimitsa Chitetezo cha Yuda

Rehobowamu amakhala mu Yerusalemu ndipo anamanga mizinda ya chitetezo iyi mu Yuda: Betelehemu, Etamu, Tekowa, Beti Zuri, Soko, Adulamu, Gati, Maresa, Zifi, Adoraimu, Lakisi, Azeka, 10 Zora, Ayaloni ndi Hebroni. Iyi ndiye inali mizinda yotetezedwa ya Yuda ndi Benjamini. 11 Iye anakhwimitsa chitetezo cha mizindayi ndipo anayikamo atsogoleri a ankhondo, pamodzi ndi chakudya, mafuta a olivi ndi vinyo. 12 Mʼmizinda yonse anayikamo zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndipo anachititsa kuti mizindayo ikhale yamphamvu. Choncho iye amalamulira Yuda ndi Benjamini.

13 Ansembe ndi Alevi a mʼmadera onse a Israeli anakhala mbali ya Rehobowamu. 14 Alevi anasiya malo awo owetera ziweto ndi katundu wawo, ndi kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu chifukwa Yeroboamu ndi ana ake anawakana kukhala ansembe a Yehova. 15 Ndipo iye anasankha ansembe akeake a pa malo opatulika ndi a mafano a mbuzi ndi mwana wangʼombe amene anapanga. 16 Anthu ochokera fuko lililonse la Israeli amene anatsimikiza mitima yawo kufunafuna Yehova Mulungu wa Israeli, ankapitabe ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. 17 Iwo analimbikitsa ufumu wa Yuda, ndipo anathandiza Rehobowamu mwana wa Solomoni kwa zaka zitatu. Pa nthawi imeneyi iye amatsatira zochita za Davide ndi Solomoni.

Banja la Rehobowamu

18 Rehobowamu anakwatira Mahalati, amene abambo ake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo amayi ake anali Abihaili, mwana wa Eliabu, mwana wa Yese. 19 Mkaziyo anamubereka ana aamuna awa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu. 20 Kenaka anakwatira Maaka, mwana wamkazi wa Abisalomu, amene anamubereka Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti. 21 Rehobowamu ankamukonda Maaka mwana wa Abisalomu kuposa aliyense mwa akazi ake ndi azikazi. Iye anali ndi akazi 18, azikazi 60, ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60.

22 Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri pa abale ake, ndi cholinga choti adzakhale mfumu. 23 Iye anachita mwanzeru, pomwaza ena mwa ana ake ku madera onse a Yuda ndi Benjamini, ndi ku mizinda yonse yotetezedwa. Iye anawapatsa zinthu zambiri ndiponso anawafunira akazi ambiri.

Sisaki Athira Nkhondo Dziko la Yuda

12 Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova. Chifukwa anakhala osakhulupirika pamaso pa Yehova, Sisaki mfumu ya dziko la Igupto inathira nkhondo Yerusalemu mʼchaka chachisanu cha mfumu Rehobowamu. Sisakiyo anabwera ndi magaleta 1,200 ndi anthu okwera akavalo 60,000 ndiponso asilikali osawerengeka ochokera ku Libiya, Suki ndi Kusi amene anabwera naye kuchokera ku Igupto. Iye analanda mizinda yotetezedwa ya Yuda ndipo anafika mpaka ku Yerusalemu.

Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’ ”

Atsogoleri a Israeli pamodzi ndi mfumu anadzichepetsa nati, “Yehova ndi wolungama.”

Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki. Komabe iwo adzakhala pansi pa ulamuliro wake, kuti aphunzire kudziwa kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a mayiko ena.”

Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga. 10 Ndipo mfumu inapereka zishango zamkuwa kwa oyangʼanira mʼmalo mwake ndipo iwo anazipereka kwa oyangʼanira alonda amene amayangʼanira pa chipata cha nyumba yaufumu. 11 Nthawi ina iliyonse imene mfumu ikupita ku Nyumba ya Yehova, alonda amapita nayo atanyamula zishango, ndipo kenaka amakazibwezera ku chipinda cha alonda.

12 Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda.

13 Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni. 14 Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova.

15 Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 16 Rehobowamu anamwalira, ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Ndipo mwana wake Abiya analowa ufumu mʼmalo wake.

Yohane 11:30-57

30 Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.

32 Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”

33 Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. 34 Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”

Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”

35 Yesu analira.

36 Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”

37 Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”

Yesu Aukitsa Lazaro

38 Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. 39 Yesu anati, “Chotsani mwala.”

Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”

40 Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”

41 Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. 42 Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”

43 Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” 44 Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.

Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”

Ayuda Apangana za Kupha Yesu

45 Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kudzamuchereza Mariya ndi kuona zimene Yesu anachita anamukhulupirira Iye. 46 Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawawuza zimene Yesu anachita. 47 Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu olamulira.

Iwo anafunsa kuti, “Kodi ife tikuchita chiyani? Pano pali munthu uyu akuchita zizindikiro zodabwitsa zambiri. 48 Ngati ife timuleka kuti apitirize chotere, aliyense adzamukhulupirira Iye, ndipo kenaka Aroma adzabwera ndi kudzatenga malo athu pamodzi ndi dziko lathu.”

49 Kenaka mmodzi wa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anayankhula kuti, “Inu simukudziwa kanthu kalikonse! 50 Inu simukuzindikira kuti kuli bwino kwa inu kuti munthu mmodzi afe mʼmalo mwa anthu kusiyana ndi kuti mtundu wonse uwonongeke.”

51 Iye sananene izi mwa iye yekha, koma monga mkulu wa ansembe chaka chimenecho ananenera kuti Yesu anayanera kufera mtundu wa Ayuda, 52 ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi. 53 Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe.

54 Chifukwa cha ichi Yesu sanayendenso moonekera pakati pa Ayuda. Mʼmalo mwake Iye anapita ku chigawo cha kufupi ndi chipululu, ku mudzi wa Efereimu, kumene Iye anakhalako ndi ophunzira ake.

55 Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike. 56 Iwo anapitiriza kumufunafuna Yesu, ndipo pamene ankayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi ukuganiza chiyani? Kodi Iye sabwera konse kuphwando?” 57 Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.