Old/New Testament
Abweretsanso Bokosi la Chipangano
13 Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100. 2 Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe. 3 Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.” 4 Gulu lonse linavomereza izi, pakuti anthu onse anaona kuti kunali kofunika kutero.
5 Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu. 6 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake.
7 Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo. 8 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
9 Atafika pa malo opunthira tirigu ku Kidoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire bokosilo, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. 10 Yehova anapsera mtima Uza ndipo anamukantha chifukwa chogwira bokosilo. Choncho iyeyo anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.
11 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.
12 Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Mulungu ndipo anafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu lingafike bwanji kwathu?” 13 Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 14 Ndipo Bokosi la Mulungu linakhala mʼbanja la Obedi-Edomu mʼnyumba mwake kwa miyezi itatu ndipo Yehova anadalitsa nyumba yake ndi chilichonse chimene anali nacho.
Nyumba ya Davide ndi Banja Lake
14 Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu. 2 Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza kwambiri ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.
3 Davide anakwatira akazi ena ambiri ku Yerusalemu ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. 4 Mayina a ana amene anaberekera ku Yerusalemu anali awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, 5 Ibihari, Elisua, Elipeleti, 6 Noga, Nefegi, Yafiya, 7 Elisama, Beeliada ndi Elifeleti.
Davide Agonjetsa Afilisti
8 Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya dziko lonse la Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anapita kukakumana nawo. 9 Ndipo Afilisti anabwera ndi kulanda zinthu mʼChigwa cha Refaimu. 10 Davide anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?”
Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka mʼmanja mwako.”
11 Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Mulungu waphwanya adani anga ine ndikuona.” Motero anawatcha malowa Baala Perazimu. 12 Afilisti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide analamulira kuti itenthedwe ndi moto.
13 Nthawi inanso Afilisti anadzalanda katundu mu Chigwamo. 14 Choncho Davide anafunsa Mulungu ndipo Mulunguyo anayankha kuti, “Usapite molunjika, koma uzungulire kumbuyo kwawo. Ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. 15 Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukapite kukamenyana nawo, chifukwa izi zikasonyeza kuti Mulungu ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” 16 Kotero Davide anachita zimene Mulungu anamulamulira ndipo anakantha ankhondo a Afilisti njira yonse kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.
17 Choncho mbiri ya Davide inafalikira dziko lonse, ndipo Yehova anachititsa kuti mayiko ena azimuopa.
Bokosi la Chipangano Alibweretsa ku Yerusalemu
15 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti. 2 Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.”
3 Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse mu Yerusalemu kuti abweretse Bokosi la Yehova ku malo amene analikonzera. 4 Iye anayitanitsa pamodzi zidzukulu za Aaroni ndi Alevi:
5 kuchokera ku banja la Kohati,
mtsogoleri Urieli ndi abale ake 120.
6 Kuchokera ku banja la Merari,
mtsogoleri Asaya ndi abale ake 220;
7 kuchokera ku banja la Geresomu,
mtsogoleri Yoweli ndi abale ake 130;
8 kuchokera ku banja la Elizafani,
mtsogoleri Semaya ndi abale ake 200;
9 kuchokera ku banja la Hebroni,
mtsogoleri Elieli ndi abale ake 80;
10 kuchokera ku banja la Uzieli,
mtsogoleri Aminadabu ndi abale ake 112.
11 Kenaka Davide anayitanitsa ansembe Zadoki ndi Abiatara, ndi Alevi awa, Urieli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu. 12 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu atsogoleri a mabanja a Alevi ndipo inu ndi abale anu Alevi mudziyeretse nokha ndi kubweretsa Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli ku malo amene ine ndalikonzera. 13 Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.” 14 Kotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa ndi cholinga chakuti akatenge Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli. 15 Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova.
16 Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga.
17 Kotero Alevi anasankha Hemani mwana wa Yoweli; ndipo mwa abale ake anasankha Asafu mwana wa Berekiya; ndipo mwa ana a Merari, abale awo, anasankha Etani mwana wa Kusaya; 18 ndipo pamodzi ndi iwowa abale awo otsatana nawo: Zekariya, Yaazieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli, alonda a pa chipata.
19 Anthu oyimba aja Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo ankayimba ziwaya za malipenga zamkuwa; 20 Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Maaseya ndi Benaya ankayimba azeze a liwu lokwera; 21 ndipo Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu, Yeiyeli ndi Azaziya ankayimba apangwe a liwu lotsika. 22 Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi anali woyangʼanira mayimbidwe; uwu ndiye unali udindo wake pakuti anali waluso pa zimenezi.
23 Berekiya ndi Elikana anali olondera pa khomo la bokosilo. 24 Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo.
25 Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera. 26 Popeza Mulungu anathandiza Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, anapereka nsembe ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndiponso nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri. 27 Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala. 28 Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe.
29 Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake.
Yesu Apita Kuphwando Lamisasa
7 Zitatha izi Yesu anayendayenda mu Galileya, ndi cholinga chakuti asafike ku Yudeya chifukwa Ayuda kumeneko amadikira kuti amuphe. 2 Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira, 3 abale a Yesu anati kwa Iye, “Inu muyenera kuchoka kuno ndi kupita ku Yudeya, kuti ophunzira anu akaone zodabwitsa zomwe mumachita. 4 Palibe wina aliyense amene amafuna kukhala wodziwika amachita zinthu mseri. Popeza Inu mukuchita zinthu izi, mudzionetsere nokha ku dziko la pansi.” 5 Pakuti ngakhale abale ake omwe sanamukhulupirire.
6 Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera. 7 Dziko lapansi silingakudeni inu, koma limandida Ine chifukwa Ine ndimachitira umboni kuti zomwe limachita ndi zoyipa. 8 Inu pitani kuphwando. Ine sindipita tsopano kuphwando ili chifukwa kwa Ine nthawi yoyenera sinafike.” 9 Atanena izi, Iye anakhalabe mu Galileya.
10 Komabe, abale ake atanyamuka kupita kuphwando, Iye anapitanso, osati moonekera, koma mseri. 11 Tsopano kuphwandoko Ayuda anakamufunafuna ndi kumafunsana kuti, “Kodi munthu ameneyu ali kuti?”
12 Pakuti pa chigulu cha anthu panali kunongʼona ponseponse za Iye. Ena ankanena kuti, “Iye ndi munthu wabwino.”
Ena ankayankha kuti, “Ayi, Iye amanamiza anthu.” 13 Koma panalibe amene ankanena kalikonse poyera za Iye chifukwa choopa Ayuda.
Yesu Aphunzitsa pa Phwando
14 Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa. 15 Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?”
16 Yesu anayankha kuti, “Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma. 17 Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha. 18 Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse. 19 Kodi Mose sanakupatseni lamulo? Komatu palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akusunga lamulo. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha Ine?”
20 Gulu la anthu linayankha kuti, “Iwe ndiye wagwidwa ndi ziwanda. Ndani akufuna kukupha?”
21 Yesu anawawuza kuti, “Ine ndinachita chodabwitsa chimodzi ndipo inu mwadabwa. 22 Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata. 23 Tsopano ngati mwana angachite mdulidwe pa Sabata kuti lamulo la Mose lisaswedwe, nʼchifukwa chiyani mukundipsera mtima chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata? 24 Musamaweruze potengera maonekedwe chabe, koma weruzani molungama.”
Kodi Yesu ndi Khristu?
25 Pa nthawi imeneyi anthu ena a ku Yerusalemu anayamba kufunsana kuti, “Kodi uyu si munthu uja akufuna kumuphayu? 26 Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu? 27 Koma ife tikudziwa kumene achokera munthuyu; pamene Khristu adzabwere, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.