Old/New Testament
Mabanja Ena a Yuda
4 Ana a Yuda anali awa:
Perezi, Hezironi, Karimi, Huri ndi Sobali.
2 Reaya mwana wa Sobala anabereka Yahati, ndipo Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Awa anali mabanja a Azorati.
3 Ana a Etamu anali awa:
Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi. 4 Penueli anabereka Gedori, ndipo Ezeri anabereka Husa.
Awa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi abambo a Betelehemu.
5 Asihuri abambo a Tekowa anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.
6 Naara anamuberekera Ahuzamu, Heferi, Temani ndi Haahasitari. Awa ndiwo anali ana a Naara.
7 Ana a Hela:
Zereti, Zohari, Etinani, 8 ndi Kozi, amene anali abambo ake a Anubi ndi Hazo-Beba ndi mabanja a Ahariheli mwana wa Harumi.
9 Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.” 10 Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.
11 Kelubi, mʼbale wa Suha, anabereka Mehiri, amene anabereka Esitoni. 12 Esitoni anabereka Beti-Rafa, Paseya ndi Tehina amene anabereka Iri Nahasi. Amenewa ndiwo anthu a ku Reka.
13 Ana a Kenazi anali awa:
Otanieli ndi Seraya.
Ana a Otanieli anali awa:
Hatati ndi Meonotai. 14 Meonotai anabereka Ofura.
Seraya anabereka Yowabu,
amene anabereka Ge-Harasimu. Anawatcha dzina ili chifukwa anthu ake anali amisiri.
15 Ana a Kalebe mwana wa Yefune anali awa:
Iru, Ela ndi Naama.
Mwana wa Ela anali
Kenazi.
16 Ana a Yehaleleli anali awa:
Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli.
17 Ana a Ezara anali awa:
Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa. 18 (Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.
19 Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa:
abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka.
20 Ana a Simeoni anali awa:
Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni.
Ana a Isi anali awa:
Zoheti ndi Beni-Zoheti.
21 Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa:
Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya, 22 Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale). 23 Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu.
Simeoni
24 Ana a Simeoni anali awa:
Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli;
25 Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu.
26 Zidzukulu za Misima zinali izi:
Hamueli, Zakuri ndi Simei.
27 Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda. 28 Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali, 29 Biliha, Ezemu, Toladi, 30 Betueli, Horima, Zikilagi, 31 Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide. 32 Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu 33 ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo.
34 Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35 Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli, 36 komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, 37 ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya.
38 Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri 39 ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo. 40 Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba.
41 Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. 42 Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri. 43 Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.
Fuko la Rubeni
5 Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa, 2 ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe) 3 ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa:
Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi.
4 Ana a Yoweli anali awa:
Semaya, Gogi,
Simei, 5 Mika,
Reaya, Baala,
6 ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri.
7 Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa:
Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya, 8 ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni. 9 Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi.
10 Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi.
Fuko la Gadi
11 Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka:
12 Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati.
13 Abale awo mwa mabanja awo anali awa:
Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri.
14 Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi.
15 Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo.
16 Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera.
17 Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli.
18 Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo. 19 Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu. 20 Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira. 21 Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, 22 enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo.
Theka la Fuko la Manase
23 Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri.
24 Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo. 25 Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika. 26 Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.
Fuko la Levi
6 Ana a Levi anali awa:
Geresoni, Kohati ndi Merari.
2 Ana a Kohati anali awa:
Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
3 Ana a Amramu anali awa:
Aaroni, Mose ndi Miriamu.
Ana a Aaroni anali awa:
Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara
4 Eliezara anabereka Finehasi,
Finehasi anabereka Abisuwa,
5 Abisuwa anabereka Buki,
Buki anabereka Uzi.
6 Uzi anabereka Zerahiya,
Zerahiya anabereka Merayoti,
7 Merayoti anabereka Amariya,
Amariya anabereka Ahitubi.
8 Ahitubi anabereka Zadoki,
Zadoki anabereka Ahimaazi.
9 Ahimaazi anabereka Azariya,
Azariya anabereka Yohanani,
10 Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),
11 Azariya anabereka Amariya,
Amariya anabereka Ahitubi,
12 Ahitubi anabereka Zadoki,
Zadoki anabereka Salumu,
13 Salumu anabereka Hilikiya,
Hilikiya anabereka Azariya,
14 Azariya anabereka Seraya,
ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.
15 Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.
16 Ana a Levi anali awa:
Geresomu, Kohati ndi Merari.
17 Mayina a ana a Geresomu ndi awa:
Libini ndi Simei.
18 Ana a Kohati anali awa:
Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
19 Ana a Merari anali awa:
Mahili ndi Musi.
Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:
20 Ana a Geresomu ndi awa:
Libini, Yehati,
Zima, 21 Yowa,
Ido, Zera
ndi Yeaterai.
22 Zidzukulu za Kohati ndi izi:
Aminadabu, Kora,
Asiri, 23 Elikana,
Ebiyasafu, Asiri,
24 Tahati, Urieli,
Uziya ndi Sauli.
25 Zidzukulu za Elikana ndi izi:
Amasai, Ahimoti,
26 Elikana, Zofai,
Nahati, 27 Eliabu,
Yerohamu, Elikana
ndi Samueli.
28 Ana a Samueli ndi awa:
Mwana wake woyamba anali Yoweli,
wachiwiri anali Abiya.
29 Zidzukulu za Merari ndi izi:
Mahili, Libini,
Simei, Uza,
30 Simea, Hagiya
ndi Asaya.
Oyimba mʼNyumba ya Mulungu
31 Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo. 32 Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.
33 Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa:
Ochokera ku banja la Kohati:
Hemani, katswiri woyimba,
anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,
34 mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu,
mwana wa Elieli, mwana wa Towa,
35 mwana wa Zufi, mwana wa Elikana,
mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
36 mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli,
mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
37 mwana wa Tahati, mwana wa Asiri,
mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,
38 mwana wa Izihari, mwana wa Kohati,
mwana wa Levi, mwana wa Israeli;
39 ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja:
Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,
40 mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya,
mwana wa Malikiya, 41 mwana wa Etini,
mwana wa Zera, mwana wa Adaya,
42 mwana wa Etani, mwana wa Zima,
mwana Simei, 43 mwana wa Yahati,
mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;
44 ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere:
Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi,
mwana wa Maluki, 45 mwana wa Hasabiya,
mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46 mwana wa Amizi, mwana wa Bani,
mwana wa Semeri, 47 mwana wa Mahili,
mwana wa Musi, mwana wa Merari,
mwana wa Levi.
48 Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu. 49 Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.
50 Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa:
Eliezara, Finehasi,
Abisuwa, 51 Buki,
Uzi, Zerahiya,
52 Merayoti, Amariya,
Ahitubi, 53 Zadoki
ndi Ahimaazi.
54 Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).
55 Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. 56 Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.
57 Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa, 58 Hileni, Debri, 59 Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. 60 Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.
61 Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.
62 Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.
63 Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
64 Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa. 65 Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.
66 Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.
67 Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri, 68 Yokineamu, Beti-Horoni, 69 Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.
70 Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.
71 Ageresomu analandira malo awa:
Kuchokera ku theka la fuko la Manase,
analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;
72 Kuchokera ku fuko la Isakara
analandira Kedesi, Daberati, 73 Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
74 kuchokera ku fuko la Aseri
analandira Masala, Abidoni, 75 Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
76 ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali
analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.
77 Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa:
kuchokera ku fuko la Zebuloni,
iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
78 Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko,
analandira Bezeri ku chipululu, Yaza, 79 Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
80 ndipo kuchokera ku fuko la Gadi
analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu, 81 Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
6 Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya), 2 ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala. 3 Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. 4 Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi.
5 Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?” 6 Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
7 Filipo anamuyankha Iye kuti, “Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!”
8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati, 9 “Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?”
10 Yesu anati, “Awuzeni anthuwa akhale pansi.” Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000. 11 Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
12 Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.” 13 Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.
14 Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.” 15 Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha.
Yesu Ayenda pa Madzi
16 Pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira ku nyanja, 17 kumene iwo analowa mʼbwato ndi kuyamba kuwoloka nyanja kupita ku Kaperenawo. Tsopano kunali kutada ndipo Yesu anali asanabwerere kwa iwo. 18 Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa. 19 Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha. 20 Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.” 21 Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.