Old/New Testament
Hoseya Mfumu Yotsiriza ya Israeli
17 Mʼchaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoseya mwana wa Ela anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka zisanu ndi zinayi. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi mafumu a Israeli amene ankalamulira iye asanalowe ufumuwo.
3 Salimenezeri mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo Hoseya amene anali pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iyeyo. 4 Koma mfumu ya ku Asiriya inazindikira kuti Hoseya akuwukira, pakuti Hoseyayo anali atatumiza nthumwi kwa So mfumu ya Igupto ndiponso analeka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, monga ankachitira chaka ndi chaka. Choncho Salimenezeri anagwira Hoseya ndi kumuyika mʼndende. 5 Mfumu ya ku Asiriya inapita kukathira nkhondo dziko lonse la Israeli ndipo inapita mpaka ku Samariya ndipo inazinga mzindawo kwa zaka zitatu. 6 Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya, mfumu ya ku Asiriya inalanda Samariya ndipo inatenga Aisraeli ndi kupita nawo ku Asiriya. Anakawakhazika ku Hala ndi Habori mʼmbali mwa mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.
Israeli Apita ku Ukapolo chifukwa cha Tchimo
7 Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina, 8 ndiponso ankatsatira miyambo ya anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika mʼdzikomo pamodzinso ndi miyambo yonse imene mafumu a Israeli anayambitsa. 9 Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano. 10 Anayimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya mafano a Asera pa phiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 11 Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. 12 Ndipo iwowo ankapembedza mafano ngakhale Yehova ananena kuti, “Musadzachite zimenezi.” 13 Yehova anachenjeza Israeli ndi Yuda kudzera mwa aneneri ake onse ndi alosi kuti, “Lekani mchitidwe wanu woyipawo. Mverani malamulo anga ndi malangizo anga potsatira zonse zolembedwa mʼmalamulo a Mose, zimene ndinalamulira makolo anu kuti azimvere, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”
14 Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo. 15 Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.
16 Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. 17 Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa.
18 Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha. 19 Yuda nayenso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wawo. Iwo ankatsatira machitidwe amene Israeli anayambitsa. 20 Motero Yehova anakana Aisraeli onse. Iye anawazunza nawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha mpaka Iye atawachotseratu pamaso pake.
21 Yehova atangʼamba Israeli kumuchotsa ku nyumba ya Davide, Aisraeliwo anasankha Yeroboamu mwana wa Nebati kukhala mfumu yawo. Yeroboamu ananyengerera Aisraeli kuti asatsatire Yehova ndipo anawachimwitsa tchimo lalikulu. 22 Aisraeli anakakamira machimo onse amene Yeroboamu anachita ndipo sanawasiye 23 mpaka pamene Yehova anawachotsa pamaso pake monga anawachenjezera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Choncho Aisraeli anachotsedwa mʼdziko lawo kupita ku ukapolo ku Asiriya ndipo ali komweko mpaka lero lino.
Anthu Achilendo Akhala mu Samariya
24 Mfumu ya ku Asiriya inabweretsa anthu a ku Babuloni, Kuta, Awa, Hamati ndi a ku Sefaravaimu kudzawakhazika mʼmizinda ya Samariya kulowa mʼmalo mwa Aisraeli. Iwo anatenga Samariya ndi kukhala mʼmizinda yake. 25 Iwo atayamba kukhala kumeneko, sanapembedze Yehova choncho Yehova anatumiza mikango pakati pawo ndipo inapha ena mwa iwo. 26 Tsono mfumu ya ku Asiriya inawuzidwa za nkhaniyi kuti, “Anthu amene munawatumiza ndi kuwakhazika mʼmizinda ya Samariya sakudziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna. Choncho Iye watumiza mikango pakati pawo imene ikuwapha chifukwa anthuwo sadziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna.”
27 Tsono mfumu ya ku Asiriya inalamula kuti, “Tengani wansembe mmodzi mwa amene munawagwira ukapolo, mupite naye kumeneko ndipo akakhale komweko nakaphunzitse anthu zimene Mulungu wa dzikolo amafuna.” 28 Choncho mmodzi mwa ansembe amene anawatenga ku Samariya anabwera kudzakhala ku Beteli ndipo ankaphunzitsa anthuwo kupembedza Yehova.
29 Koma mtundu uliwonse wa anthu unkapangabe mafano a milungu yawoyawo mʼmizinda yambiri imene anthuwo ankakhala, ndipo anayika milunguyo mʼnyumba za milungu zimene anthu a ku Samariya anamanga ku malo opembedzera mafano. 30 Anthu a ku Babuloni anapanga Sukoti-Benoti, anthu a ku Kuti anapanga Nerigali, ndipo anthu a ku Hamati anapanga Asima; 31 Aava anapanga Nibihazi ndi Taritaki, ndipo Asefaravaimu ankawotcha ana awo pa moto ngati nsembe kwa Adirameleki ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. 32 Iwo ankapembedza Yehova, koma ankadzisankhira okha pakati pawo anthu wamba kuti akhale ansembe awo ku nyumba za milungu za ku malo opembedzera mafano. 33 Iwowo ankapembedza Yehova, komanso ankatumikira milungu yawo molingana ndi miyambo ya mitundu ya kumene ankachokera.
34 Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli. 35 Pamene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli, Iye anawalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuyigwadira iyo, kuyitumikira kapena kupereka nsembe kwa iyoyo. 36 Koma Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndiye amene muyenera kumupembedza. 37 Muyenera kusamalitsa nthawi zonse kusunga malangizo anga ndi malemba anga, chiphunzitso ndi malamulo amene anakulemberani. Musapembedze milungu ina. 38 Musayiwale pangano limene ndinapangana nanu ndipo musamapembedze milungu ina. 39 Mʼmalo mwake muzipembedza Yehova Mulungu wanu pakuti ndiye amene adzakulanditsani mʼdzanja la adani anu onse.”
40 Komabe iwo sanamvere ndipo anapitiriza kuchita zomwe ankachita kale. 41 Ngakhale anthuwo ankapembedza Yehova, ankatumikiranso mafano awo. Mpaka lero lino ana awo ndi zidzukulu zawo zikupitiriza kuchita zomwe ankachita makolo awo.
Hezekiya Mfumu ya Yuda
18 Mʼchaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu. 2 Anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Abi, mwana wa Zekariya. 3 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. 4 Anachotsa malo opembedzerako mafano, anaphwanya miyala yachipembedzo ndiponso anadula mafano a Asera. Iye anaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, pakuti mpaka kufikira nthawi imeneyi Aisraeli amafukiza lubani kwa njoka imeneyi. (Imatchedwa Nehusitani).
5 Hezekiya anadalira Yehova Mulungu wa Israeli. Kotero panalibe wina wofanana naye pakati pa mafumu onse a Yuda, asanakhale mfumu kapena atakhala kale mfumu. 6 Iye anakangamira Yehova ndipo sanamusiye koma anasunga malamulo amene Yehova anapatsa Mose. 7 Ndipo Yehova anali naye ndipo kulikonse kumene anapita zinthu zinkamuyendera bwino. Iye anagalukira mfumu ya ku Asiriya ndipo sanayitumikirenso. 8 Iye anakantha Afilisti kuyambira ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa. Anakafika mpaka ku Gaza ndi ku malire ake.
9 Mʼchaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Salimenezeri, mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya ndi kuwuzinga 10 Asiriya analanda mzindawu patatha zaka zitatu. Choncho mzinda wa Samariya unalandidwa chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya mfumu ya Israeli. 11 Mfumu ya ku Asiriya inatenga Aisraeli kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya ndipo anakawakhazika ku Hala, ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi. 12 Izi zinachitika chifukwa sanamvere zonena za Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula. Iwo sanamvere malamulowo kapena kuwagwiritsa ntchito.
13 Mʼchaka chakhumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, nayilanda. 14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya ku Asiriya ku Lakisi wonena kuti, “Ine ndalakwa. Chokani kuno ndipo ndidzakupatsani chilichonse chimene munene.” Mfumu ya ku Asiriya inalamula mfumu Hezekiya, mfumu ya Yuda, kuti azipereka makilogalamu a siliva okwana 3,000 ndi makilogalamu a golide 1,000. 15 Mfumu Hezekiya inapereka siliva yense amene anapezeka mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba zosungiramo chuma cha mfumu.
16 Nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anakanganula golide amene anakuta zitseko ndi mphuthu za chipata cha Nyumba ya Yehova namupereka kwa mfumu ya ku Asiriya.
Senakeribu Aopseza Yerusalemu
17 Mfumu ya ku Asiriya inatuma Taritani, Rabusarisi ndi Rabusake pamodzi ndi gulu lalikulu la ankhondo, kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwo anafika ku Yerusalemu nakayima pafupi ndi ngalande ya madzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu waukulu wopita ku malo a Munda wa Mmisiri Wochapa. 18 Iwo anayitana mfumu, ndipo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa anthuwo.
19 Ndipo Rabusake anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,
“ ‘Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, ‘Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?’ 20 Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? 21 Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.’ ” 22 Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, “Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa lansembe ili mu Yerusalemu?”
23 “ ‘Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! 24 Ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo? 25 Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga malo ano popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.’ ”
26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina ndi Yowa anawuza Rabusakeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
27 Koma Rabusake anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
28 Tsono Rabusake anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! 29 Zimene mfumu ikunena ndi izi: ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni mʼdzanja langa. 30 Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
31 “ ‘Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, 32 mpaka nditabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanuli, dziko la tirigu ndi vinyo watsopano, dziko la chakudya ndi minda ya mipesa, dziko la mitengo ya olivi ndi uchi. Sankhani moyo osati imfa!
“Musamvere zonena Hezekiya, pakuti iye akukusocheretsani ponena kuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ 33 Kodi mulungu wa anthu a mtundu wina uliwonse wapulumutsapo dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? 34 Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, Hena ndi Ivani? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? 35 Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja langa? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
36 Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”
37 Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu, mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza Hezekiya zonse zimene anayankhula Rabusake uja.
19 Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. 20 Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. 21 Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”
Yohane Mʼbatizi Achita Umboni za Yesu
22 Zitatha izi, Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼmadera a ku midzi ya ku Yudeya, kumene Iye anakhala kanthawi akubatiza. 23 Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa. 24 (Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende). 25 Mkangano unabuka pakati pa ophunzira ena a Yohane ndi Ayuda ena pa zamwambo wodziyeretsa wa Ayuda. 26 Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.”
27 Atamva zimenezi, Yohane anayankha kuti, “Munthu amalandira chokhacho chapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. 28 Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’ 29 Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri. 30 Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe.
31 “Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. 32 Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. 33 Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. 35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. 36 Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.