Old/New Testament
Kuphedwa kwa Banja la Ahabu
10 Tsono Ahabu anali ndi ana aamuna 70 a ku Samariya. Ndipo Yehu analemba makalata nawatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a mu mzinda wa Yezireeli, kwa akuluakulu ndiponso kwa amene ankalera ana a Ahabu, nati, 2 “Inu mukangolandira kalatayi, popeza ana a mbuye wanu ali ndi inu ndiponso muli ndi magaleta ndi akavalo, mzinda wotetezedwa ndi zida zankhondo, 3 sankhani mwana wa mbuye wanu amene ndi wooneka bwino ndiponso woyenera, mulowetseni ufumu wa abambo ake. Kenaka muchite nkhondo kuteteza nyumba ya mbuye wanu.”
4 Koma anthuwo anachita mantha kwambiri ndipo anati, “Taonani, mafumu awiri sanathe kulimbana naye, nanga ife tingathe bwanji?”
5 Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, bwanamkubwa wa mzinda, akuluakulu ena ndiponso olera anawo anatumiza uthenga uwu kwa Yehu: “Ife ndife atumiki anu ndipo tidzachita chilichonse chomwe mutiwuze. Sitidzasankha munthu wina aliyense kukhala mfumu ndipo chitani chimene mukuganiza kuti nʼchabwino kwa inu.”
6 Ndipo Yehu anawalembera kalata yachiwiri yonena kuti, “Ngati inu muli mbali yanga ndi kuti mudzandimvera, mudule mitu ya ana a mbuye wanu ndipo mubwere nayo kwa ine ku Yezireeli mawa nthawi ngati yomwe ino.”
Tsono ana a mfumu onse 70 anali pamodzi ndi akuluakulu a mu mzindamo, amene ankawalera. 7 Kalatayo itafika, anthuwo anatenga ana a mfumu 70 aja ndi kuwapha onse. Anayika mitu yawo mʼmadengu ndi kuyitumiza ku Yezireeli kwa Yehu. 8 Mthenga uja atafika, anamuwuza Yehu kuti, “Abweretsa mitu ya ana a mfumu.”
Ndipo Yehu analamula kuti, “Unjikani mituyo mʼmilu iwiri pa chipata cha mzinda ndipo ikhale pamenepo mpaka mmawa.”
9 Mmawa mwake Yehu anatuluka. Iye anayimirira pamaso pa anthu onse ndipo anati, “Inu ndinu osalakwa. Ndine amene ndinachita chiwembu mbuye wanu ndi kumupha, koma kodi wapha anthu onsewa ndani? 10 Koma dziwani tsono, kuti mawu amene Yehova anayankhula kunena za banja la Ahabu sadzapita padera. Yehova wachita chimene analonjeza kudzera mwa mtumiki wake Eliya.” 11 Choncho Yehu anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Yezireeli, pamodzinso ndi akuluakulu ake onse, abwenzi ake ndiponso ansembe ake, sanasiyeko ndi mmodzi yemwe wamoyo.
12 Kenaka Yehu ananyamuka kupita ku Samariya. Atafika pa malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa, 13 Yehu anakumana ndi abale ena a Ahaziya mfumu ya Yuda nawafunsa kuti, “Kodi ndinu yani?”
Iwo anayankha kuti, “Ndife abale ake a Ahaziya, ndipo tabwera kulonjera banja la mfumu ndi ana a mfumukazi.”
14 Yehu analamula kuti, “Atengeni amoyo!” Choncho anawatenga amoyo ndipo anakawaphera ku chitsime cha ku malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa; anthu onse 42. Iye sanasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo.
15 Yehu atachoka kumeneko anakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu, amene amabwera kudzakumana naye. Yehu anamulonjera nati kwa iye, “Kodi mtima wako uli bwino monga momwe mtima wanga ugwirizana nawo mtima wako?”
Yehonadabu anayankha kuti, “Inde ndikugwirizana nawe.”
Yehu anati, “Ngati ndi choncho, gwire dzanja.” Ndipo iye anaterodi, ndipo Yehu anamugwira dzanja namulowetsa mʼgaleta lake. 16 Yehu anati, “Tiye kuno uwone mmene ndikudziperekera kwa Yehova.” Ndipo anayenda naye mʼgaleta mwake.
17 Yehu atafika ku Samariya, anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Samariya; anawawonongeratu potsata mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Eliya.
Aneneri a Baala Aphedwa
18 Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi nawawuza kuti, “Ahabu ankatumikira Baala pangʼono chabe; Yehu adzamutumikira kwambiri. 19 Tsopano itanani aneneri a Baala onse, atumiki ake onse ndi ansembe ake onse. Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotsala chifukwa ine ndidzapereka nsembe yayikulu kwa Baala. Aliyense amene alephere kubwera adzaphedwa.” Koma Yehu anachita zimenezi mwachinyengo ndi cholinga choti awononge atumiki onse a Baala.
20 Yehu anati, “Itanitsani msonkhano wodzalemekeza Baala.” Ndipo analengeza za msonkhanowo. 21 Pamenepo Yehu anatumiza mawu ku dziko lonse la Israeli ndipo atumiki onse a Baala anabwera; palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala. Iwo anadzaza nyumba ya Baala. Nyumbayo inadzaziratu kuchokera ku khoma lina mpaka ku khoma lina. 22 Ndipo Yehu anawuza munthu wosunga mikanjo kuti, “Bweretsa mikanjo yokwanira atumiki onse a Baala.” Ndipo iye anabweretsa mikanjoyo.
23 Kenaka Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu analowa mʼnyumba ya Baala. Yehu anawawuza atumiki a Baala kuti, “Yangʼanitsitsani ndipo muone kuti muno musapezeke atumiki a Yehova, koma mukhale atumiki okhawo a Baala.” 24 Choncho Yehu analowa kukapereka nsembe zina ndi nsembe zopsereza. Nthawi iyi nʼkuti Yehu atayika anthu 80 kunja kwa nyumbayo ndi chenjezo lakuti, “Ngati wina aliyense wa inu adzathawitsa wina aliyense wa anthu amene ndayika kuti muziwayangʼanira, munthu woteroyo adzaphedwa.”
25 Yehu atangotsiriza kupereka nsembe yopsereza, analamula alonda ndi akulu a ankhondo kuti, “Lowani ndipo mukawaphe ndipo musalole kuti wina athawe.” Choncho iwo anawapha ndi lupanga. Alonda ndi akulu a ankhondo anaponya mitembo ya anthuwo panja ndipo anakalowa mʼkati mwenimweni mwa nyumba ya Baala. 26 Iwo anakatulutsa mwala wopatulika umene unali mʼnyumba ya Baala ndipo anawutentha. 27 Anawononga mwala wopatulika wa Baala ndi kugwetsa nyumba ya Baala, ndipo anthu anayisandutsa chimbudzi mpaka lero lino.
28 Motero Yehu anawononga Baala mu Israeli. 29 Koma Yehuyo sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli kupembedza mafano a golide a ana angʼombe ku Beteli ndi ku Dani.
30 Yehova anati kwa Yehu, “Chifukwa wachita bwino pokwaniritsa kuchita zabwino pamaso panga ndipo wachitira banja la Ahabu zonse zimene zinali mʼmaganizo anga, zidzukulu zako zidzakhala pa mpando waufumu wa Israeli mpaka mʼbado wachinayi.” 31 Komatu Yehu sanasamalire kusunga lamulo la Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wake wonse. Iyeyo sanaleke machimo a Yeroboamu amene anachimwitsa nawo Israeli.
32 Masiku amenewo Yehova anayamba kuchepetsa dziko la Israeli. Hazaeli anagonjetsa Aisraeli, 33 kuyambira kummawa kwa Yorodani, dziko lonse la Giliyadi (chigawo cha Gadi, Rubeni ndi Manase), kuchokera ku Aroeri pafupi ndi chigwa cha Arinoni kudutsa Giliyadi mpaka ku Basani.
34 Ntchito zina za Yehu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
35 Yehu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ku Samariya. Ndipo Yehowahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 36 Yehu analamulira Aisraeli ku Samariya zaka 28.
Ataliya ndi Yowasi
11 Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu. 2 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe. 3 Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
4 Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja. 5 Yehoyada anawalamulira kuti, “Chimene muti muchite ndi ichi: Inu magulu atatu amene muti mudzakhale pa ntchito tsiku la Sabata, gulu loyamba lidzalondera nyumba ya mfumu, 6 gulu lachiwiri lidzalondera Chipata cha Suri, ndipo gulu lachitatu lidzalondera chipata cha kumbuyo kwa asilikali amene amasinthana polondera nyumbayo. 7 Ndipo inu amene muli mʼmagulu ena awiri amene simugwira ntchito pa tsiku la Sabata, nonse mudzalondere mfumu ku nyumbayo. 8 Mudzakhale mozungulira mfumuyo, munthu aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake. Wina aliyense amene adzakuyandikireni adzayenera kuphedwa. Muzikhala pafupi ndi mfumu kulikonse kumene ikupita.”
9 Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada. 10 Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova. 11 Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo.
12 Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
13 Ataliya atamva phokoso limene alonda ndi anthuwo amachita, anapita ku Nyumba ya Yehova kumene kunali anthuwo. 14 Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
15 Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.” 16 Choncho anamugwira pamene amafika pa malo amene akavalo amalowera ku nyumba ya mfumu ndipo anamuphera pamenepo.
17 Tsono Yehoyada anachititsa pangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu kuti adzakhala anthu a Yehova. Iye anachititsanso pangano pakati pa mfumu ndi anthu. 18 Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo.
Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova. 19 Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu. 20 Choncho anthu onse a mʼdzikomo anasangalala. Ndipo mu mzindamo munakhala bata chifukwa Ataliya nʼkuti ataphedwa ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.
21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anayamba kulamulira.
Yowasi Akonzanso Nyumba ya Yehova
12 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka makumi anayi. Amayi ake anali Zibiya wa ku Beeriseba. 2 Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova masiku onse amene wansembe Yehoyada ankamulangiza. 3 Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo opembedzerako mafanowo.
4 Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. 5 Wansembe aliyense alandire ndalamazo kuchokera kwa abwenzi ake, ndipo zigwiritsidwe ntchito yokonzera chilichonse chimene chipezeke kuti ndi chowonongeka mʼnyumbayo.”
6 Koma pofika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonze nyumbayo. 7 Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.” 8 Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo.
9 Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova. 10 Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba. 11 Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, 12 amisiri a miyala ndiponso anthu ophwanya miyala. Iwo ankagula matabwa ndi miyala yosema yokonzera Nyumba ya Yehova ndipo ankalipira zinthu zonse zofunika pokonzanso nyumbayo.
13 Koma ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku nyumbayo sanagulire siliva wopangira mabeseni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, malipenga kapena ziwiya zina zilizonse zagolide kapena zasiliva za ku Nyumba ya Yehova. 14 Ndalamazi anazipereka kwa anthu antchito amene anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo. 15 Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri. 16 Ndalama zomwe zinkaperekedwa pa nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo sanabwere nazo ku Nyumba ya Yehova pakuti zinali za ansembe.
17 Pa nthawi imeneyo, Hazaeli, mfumu ya Aramu anapita kukathira nkhondo mzinda wa Gati nawulanda. Kenaka Hazaeli anatembenuka kupita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. 18 Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zinthu zonse zopatulika zomwe anazipatula Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya abambo ake, mafumu a Yuda ndi mphatso zonse zomwe iye mwini anazipereka: golide yense amene anapezeka mʼnyumba yosungiramo chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi zomwe zinali mʼnyumba ya mfumu, nazipereka kwa Hazaeli mfumu ya Aramu. Pamenepo iye anachoka ku Yerusalemuko.
19 Ndipo ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 20 Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu ndi kumupha ku Beti Milo, pa njira yotsikira ku Silo. 21 Yozakara mwana wa Simeati ndi Yehozabadi mwana wa Someri atumiki ake anamukantha nafa. Ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yesu Mwana Wankhosa wa Mulungu
29 Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi! 30 Uyu ndi amene ndimatanthauza pamene ndinanena kuti, ‘Munthu amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa analipo ine ndisanabadwe.’ 31 Ine mwini sindinamudziwe Iye, koma ndinabwera kubatiza ndi madzi kuti Iye adziwike mu Israeli.”
32 Kenaka Yohane anapereka umboni uwu: “Ine ndinaona Mzimu Woyera ngati nkhunda kuchokera kumwamba nakhala pa Iye. 33 Ine sindikanamudziwa Iye, koma kuti amene anandituma ine kudzabatiza ndi madzi anati kwa ine, ‘Munthu amene udzaona Mzimu Woyera akutsika nakhazikika pa Iye ndi amene adzabatize ndi Mzimu Woyera.’ 34 Ine ndaona ndipo ndikuchitira umboni kuti uyu ndi Mwana wa Mulungu.”
Ophunzira Oyamba a Yesu
35 Pa tsiku lotsatira Yohane analinso pamenepo pamodzi ndi awiri a ophunzira ake. 36 Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”
37 Ophunzira ake awiriwo atamva iye akunena izi, iwo anamutsatira Yesu. 38 Atatembenuka, Yesu anaona iwo akumutsatira ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?”
Iwo anati, “Rabi (kutanthauza kuti Aphunzitsi), kodi mukukhala kuti?”
39 Iye anayankha kuti, “Bwerani mudzaone.”
Choncho iwo anapita ndi kukaona kumene Iye amakhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Linali ngati pafupifupi ora la khumi.
40 Andreya mʼbale wake wa Simoni Petro, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndiponso amene anamutsata Yesu. 41 Choncho chimene Andreya anachita ndi kukapeza mʼbale wake Simoni ndipo anamuwuza kuti, “Ife tamupeza Mesiya,” (kutanthauza kuti Khristu).
42 Kenaka iye anabweretsa Simoni kwa Yesu, amene anamuyangʼana ndipo anati, “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Udzatchedwa Kefa” (limene litanthauza kuti Petro).
Yesu Ayitana Filipo ndi Natanieli
43 Pa tsiku lotsatira Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Atamupeza Filipo, anati kwa iye, “Nditsate.”
44 Filipo monga Andreya ndi Petro, anali wochokera ku mzinda mudzi Betisaida. 45 Filipo anakapeza Natanieli ndipo anamuwuza kuti, “Ife tapeza amene Mose analemba za Iye mʼmalamulo, ndi zimene aneneri analembanso za Iye, Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe.”
46 Natanieli anafunsa kuti, “Nazareti! Kodi kanthu kalikonse kabwino kangachokere kumeneko?”
Filipo anati, “Bwera udzaone.”
47 Yesu atamuona Natanieli akuyandikira, anati kwa iye, “Uyu ndi Mwisraeli weniweni, mwa iye mulibe chinyengo.”
48 Natanieli anafunsa kuti, “Kodi mwandidziwa bwanji?”
Yesu anayankha kuti, “Ine ndinakuona iwe utakhala pansi pamtengo wamkuyu Filipo asanakuyitane.”
49 Kenaka Natanieli ananena kuti, “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli.”
50 Yesu anati, “Ukukhulupirira chifukwa chakuti ndakuwuza kuti Ine ndinakuona iwe uli pansi pamtengo wamkuyu? Iwe udzaona zinthu zazikulu kuposa izo.” 51 Ndipo Iye anapitirira kuti, “Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.