Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 14-15

Ahiya Anenera za Kugwa kwa Yeroboamu

14 Pa nthawi imeneyo Abiya mwana wa Yeroboamu anayamba kudwala, ndipo Yeroboamu anati kwa mkazi wake, “Nyamuka ndipo udzibise kuti usadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yeroboamu, ndipo upite ku Silo. Kumeneko kuli mneneri Ahiya amene anandiwuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthu awa. Utenge buledi khumi, makeke ndiponso botolo la uchi ndipo upite kwa mneneriyo. Iye adzakuwuza zimene zidzamuchitikire mwanayu.” Choncho mkazi wa Yeroboamu anadzibisa ndipo anapita ku nyumba ya Ahiya ku Silo.

Tsono Ahiya sankatha kupenya bwino. Ankangoona kuti mbuu chifukwa cha ukalamba. Koma Yehova nʼkuti atamuwuza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yeroboamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake pakuti akudwala, ndiye udzamuyankhe zakutizakuti mkaziyo. Iye akafika, adzadzibisa.”

Tsono Ahiya atamva mgugu wa mapazi ake pa khomo, anati, “Lowa, iwe mkazi wa Yeroboamu. Bwanji ukudzibisa? Ine ndatumidwa kuti ndikuwuze nkhani yoyipa. Pita, kamuwuze Yeroboamu kuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakukweza pakati pa anthu ndipo ndinakuyika kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. Ndinachotsa ufumu ku nyumba ya Davide ndi kuwupereka kwa iwe, koma iwe sunafanane ndi mtumiki wanga Davide, amene ankasunga malamulo anga ndi kunditsata Ine ndi mtima wake wonse, kuchita zolungama zokhazokha pamaso panga. Ndipo iwe wachita zoyipa kupambana onse amene analipo kale. Wadzipangira milungu ina, mafano a zitsulo. Iweyo wandikwiyitsa ndipo wandiwukira.

10 “ ‘Choncho taona, ndidzabweretsa masautso pa nyumba ya Yeroboamu. Ndipo ndidzawononga munthu wamwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yemwe mʼdziko la Israeli. Ndidzatentha nyumba ya Yeroboamu monga mmene munthu amatenthera ndowe mpaka yonse kutheratu. 11 Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’

12 “Ndipo iwe nyamuka, bwerera ku nyumba kwako. Phazi lako likadzangoponda mu mzindamo, mwanayo adzamwalira. 13 Aisraeli onse adzalira maliro ake ndi kumuyika mʼmanda. Ndi yekhayo wa banja la Yeroboamu amene adzayikidwe mʼmanda, pakuti ndi mwa iye yekha mmene Yehova Mulungu wa Israeli wapezamo kanthu kabwino.

14 “Koma Yehova adzadzisankhira yekha mfumu yolamulira Israeli imene idzawononga banja la Yeroboamu. Tsiku lake ndi lero! Ndati chiyani? Inde, ndi lero lomwe lino. 15 Ndipo Yehova adzakantha Israeli, kotero kuti adzakhala ngati bango logwedera pa madzi. Iye adzazula Israeli mʼdziko labwino limene analipereka kwa makolo ake ndi kuwamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa anakwiyitsa Yehova pamene anapanga mafano a Asera. 16 Ndipo Iye sadzasamalanso Israeli chifukwa cha machimo amene anachita Yeroboamu ndi kuchimwitsa nawo Israeli.”

17 Tsono mkazi wa Yeroboamu anayimirira nachoka kupita ku Tiriza. Atangoponda pa khonde la nyumba yake, mwana uja anamwalira. 18 Aisraeli anamuyika mʼmanda, ndipo onse analira maliro ake, monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya.

19 Ntchito zina pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu, nkhondo zake ndi mmene ankalamulirira zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. 20 Iye analamulira zaka 22 ndipo anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Nadabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Rehobowamu Mfumu ya Yuda

21 Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni.

22 Anthu a ku Yuda anachita zoyipa pamaso pa Yehova kupambana mmene anachitira makolo awo ndipo Yehova anawakwiyira. 23 Iwonso anadzipangira malo opembedzerapo mafano pa chitunda chilichonse ndi kuyimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya Asera pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 24 Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli.

25 Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisaki, mfumu ya Igupto, anadzathira nkhondo Yerusalemu. 26 Ananyamula chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse, ngakhalenso zishango zonse zagolide zimene Solomoni anapanga. 27 Ndipo Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zamkuwa mʼmalo mwake, nazipereka mʼmanja mwa olamulira alonda a pa khomo pa nyumba ya mfumu. 28 Nthawi zonse mfumu ikamapita ku Nyumba ya Yehova, alonda ankanyamula zishangozo, kenaka ankazisunga mʼchipinda cha alonda.

29 Tsono ntchito zina za Rehobowamu ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 30 Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 31 Ndipo Rehobowamu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Amayi ake anali Naama wa ku Amoni. Ndipo Abiya analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.

Abiya Mfumu ya Yuda

15 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Nebati, Abiya anakhala mfumu ya Yuda, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zitatu. Amayi ake anali Maaka, mwana wa Abisalomu.

Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide. Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu; pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti.

Panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu masiku onse a moyo wa Abiya. Tsono ntchito zina za Abiya, ndi zina zonse anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu. Ndipo Abiya anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Asa, mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Asa Mfumu ya Yuda

Mʼchaka cha makumi awiri cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda, 10 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu.

11 Asa anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. 12 Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga. 13 Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni. 14 Ngakhale sanachotse malo opembedzerapo mafano, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova masiku onse a moyo wake. 15 Asa anabweretsa ku Nyumba ya Yehova zinthu zimene abambo ake anazipereka, ndiponso zinthu zimene iye mwini anazipereka: zagolide, siliva ndi ziwiya zotengera.

16 Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli nthawi yonse ya ulamuliro wawo. 17 Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda.

18 Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti, 19 “Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.”

20 Choncho Beni-Hadadi anamvera zimene ananena mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira magulu ake ankhondo ku mizinda ya Israeli. Ndipo iye anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Beti-Maaka ndi dera lonse la Kinereti kuphatikiza dziko lonse la Nafutali. 21 Baasa atamva zimenezi, anasiya kumangira linga Rama ndipo anakakhala ku Tiriza. 22 Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa.

23 Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi. 24 Ndipo Asa anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Nadabu Mfumu ya Israeli

25 Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. 26 Nadabu anachita zoyipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira za abambo ake ndi mu uchimo womwe anachimwitsa nawo Israeli.

27 Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira. 28 Baasa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa, mfumu ya ku Yuda ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.

29 Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo 30 chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli.

31 Tsono ntchito za Nadabu ndi zina zonse zimene anazichita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 32 Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli pa nthawi yonse ya ulamuliro wawo.

Baasa Mfumu ya Israeli

33 Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24. 34 Anachita zoyipa pamaso pa Yehova, nayenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchita tchimo lake limene linachimwitsa anthu a ku Israeli.

Luka 22:31-46

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu. 32 Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”

33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”

34 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”

35 Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?”

Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.”

36 Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula. 37 Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”

38 Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.”

Iye anayankha kuti, “Amenewa akwanira.”

Yesu Apemphera ku Phiri la Olivi

39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye. 40 Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.” 41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti, 42 “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.” 43 Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa. 44 Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi.

45 Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni. 46 Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.