Old/New Testament
Agibiyoni Abwezera
21 Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide kunali njala kwa zaka zitatu zotsatana. Kotero Davide anapemphera kwa Yehova. Yehova anati, “Izi zachitika chifukwa chakuti Sauli ndi banja lake akanali ndi mlandu wakupha Agibiyoni.”
2 Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu). 3 Davide anafunsa Agibiyoni kuti, “Kodi ine ndikuchitireni chiyani? Ndipepese bwanji kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?”
4 Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.”
Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”
5 Iwo anayankha mfumu kuti, “Tsono za munthu amene anatiwononga ndi kukonza chiwembu choti titheretu ndi kukhala wopanda malo mu Israeli, 6 mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.”
Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”
7 Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova. 8 Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati. 9 Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele.
10 Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku. 11 Davide atawuzidwa zimene Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa, mzikazi wa Sauli anachita, 12 anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa). 13 Davide anakatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kumeneko ndiponso mafupa otayidwa a amene anaphedwa nawasonkhanitsa pamodzi.
14 Iwo anayika mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani mʼmanda a Kisi abambo ake a Sauli ku Zera mʼdziko la Benjamini, ndipo anachita zonse zimene mfumu inalamula. Atachita zimenezi, Mulungu anayankha pemphero lopempherera dzikolo.
Nkhondo ndi Afilisti
15 Nthawi inanso panali nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraeli, Davide anapita ndi ankhondo ake kukamenyana ndi Afilisti ndipo iye anatopa kwambiri. 16 Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide. 17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anabwera kudzapulumutsa Davide. Iye anamukantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti, “Inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuti nyale ya Israeli isadzazimitsidwe.”
18 Patapita nthawi, panali nkhondo ina ndi Afilisti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Safu, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai.
19 Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu.
20 Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. 21 Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha.
22 Anthu anayi amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo onse anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.
Nyimbo ya Mayamiko ya Davide
22 Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. 2 Iye anati,
“Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo,
chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa.
Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga.
Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
4 “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
5 “Mafunde a imfa anandizinga;
mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
6 Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
misampha ya imfa inalimbana nane.
7 “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
ndinapemphera kwa Mulungu wanga.
Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;
kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
8 “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,
maziko a miyamba anagwedezeka;
ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
9 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;
moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,
makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
10 Iye anangʼamba thambo natsika pansi;
pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
11 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;
nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
12 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,
mitambo yakuda ya mlengalenga.
13 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake
munkachokera makala amoto alawilawi.
14 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,
mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
15 Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake,
ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
16 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera,
ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera,
Yehova atabangula mwaukali,
pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.
17 “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;
anandivuwula mʼmadzi ozama.
18 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.
19 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,
koma Yehova anali thandizo langa.
20 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;
anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
21 “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
22 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.
23 Malamulo ake onse ali pamaso panga,
sindinasiye malangizo ake.
24 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
25 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.
26 “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu,
kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
27 Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
28 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.
29 Inu Yehova, ndinu nyale yanga;
Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
30 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo,
ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
31 “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
kwa onse amene amathawira kwa iye.
32 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?
Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
33 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu
ndi kulungamitsa njira yanga.
34 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;
Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
35 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
36 Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso;
mumawerama kuti mundikweze.
37 Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino,
kuti mapazi anga asaterereke.
38 “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha;
sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.
39 Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso;
Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.
40 Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo;
munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.
41 Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa;
ndipo ndinawononga adani anga.
42 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.
Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
43 Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi;
ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
44 “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu;
Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
45 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
akangomva za ine, amandigonjera.
46 Iwo onse anataya mtima;
anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
47 “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa.
Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!
48 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,
49 amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
50 Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;
ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
51 “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake,
amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake,
kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”
24 Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”
26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”
29 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu 30 adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”
Yesu Aneneratu za Imfa Yake Kachitatu
31 Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa. 32 Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira, 33 adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”
34 Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.
Yesu Achiritsa Wosaona
35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. 37 Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”
38 Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, 41 “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”
Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”
42 Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.” 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.