Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 3-5

Nkhondo ya pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide inachitika nthawi yayitali. Mphamvu za Davide zinkakulirakulirabe, pamene banja la Sauli mphamvu zake zimapita zicheperachepera.

Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli.

Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli.

Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;

wachinayi anali Adoniya, amayi ake anali Hagiti;

wachisanu, Sefatiya amayi ake anali Abitali;

ndipo wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila, mkazi wa Davide.

Ana awa a Davide anabadwira ku Hebroni.

Abineri Agwirizana ndi Davide

Pamene kunali nkhondo pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide, Abineri anayamba kudzipatsa yekha mphamvu pakati pa banja la Sauli. Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?”

Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu! Mulungu andilange ine Abineri, andilange kwambiri, ngati sindichitira Davide zimene Yehova anamulonjeza iye mwa lumbiro. 10 Ndidzachotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazikitsa ufumu wa Davide pa Aisraeli onse ndi Yuda kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba.” 11 Isiboseti sanayerekezenso kunena mawu ena kwa Abineri, chifukwa ankamuopa.

12 Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”

13 Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.” 14 Ndipo Davide anatuma amithenga kwa Isi-Boseti mwana wa Sauli, kumulamula kuti, “Patse mkazi wanga Mikala, amene ndinamukwatira ndi makungu 100 a msonga za mavalo a Afilisti.”

15 Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi. 16 Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo.

17 Abineri anakambirana ndi akuluakulu a Israeli ndipo anati, “Kwa kanthawi mwakhala mukufuna kulonga Davide kuti akhale mfumu yanu. 18 Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’ ”

19 Abineri anayankhulanso nawo yekha anthu a fuko la Benjamini. Kenaka anapita ku Hebroni kukamuwuza Davide zonse zimene Aisraeli ndi fuko lonse la Benjamini amafuna kuchita. 20 Abineri, amene anali ndi anthu makumi awiri, atafika kwa Davide ku Hebroni, Davide anamukonzera phwando pamodzi ndi anthu ake. 21 Ndipo Abineri anawuza Davide kuti, “Loleni kuti ndipite msanga kukasonkhanitsa Aisraeli onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuye wanga mfumu, kuti adzachite nanu pangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Kotero Davide analola Abineri kuti apite, ndipo anapita mwamtendere.

Yowabu Apha Abineri

22 Nthawi yomweyo ankhondo a Davide ndi Yowabu anafika kuchokera kumene anakathira nkhondo ndipo anabweretsa katundu wambiri wolanda ku nkhondo. Koma Abineri sanalinso ndi Davide ku Hebroni, chifukwa Davide anamulola kuti apite, ndipo anapita mu mtendere. 23 Yowabu ndi asilikali onse amene anali naye atafika, anawuzidwa kuti Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu ndipo kuti mfumu yamulola kuti apite ndi kuti wapita ndi mtendere.

24 Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Mwachita chiyani? Taonani, Abineri anabwera kwa inu. Nʼchifukwa chiyani mwamulola kuti apite? Tsopanotu wapitadi! 25 Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.”

26 Kenaka Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza amithenga kutsatira Abineri, ndipo anabwera naye kuchokera ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanadziwe zimenezi. 27 Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.

28 Patapita nthawi, Davide atamva zimenezi anati, “Ine ndi ufumu wanga tidzakhala osalakwa pamaso pa Yehova pa imfa ya Abineri mwana wa Neri. 29 Mlandu umenewu ukhala pa Yowabu ndi banja lonse la abambo ake! Mʼbanja la Yowabu musadzasowe munthu wodwala matenda a chizonono kapena khate, kapena wolumala woyendera ndodo kapena wophedwa ndi lupanga, kapena wosowa chakudya.”

30 (Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anapha Abineri chifukwa iye anapha mʼbale wawo Asaheli ku nkhondo ku Gibiyoni).

31 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho. 32 Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso.

33 Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri:

“Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru.
34     Manja ako anali osamanga,
    mapazi ako anali osakulungidwa.
Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.”

Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri.

35 Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”

36 Anthu onse anadziwa zimenezi ndipo zinawakondweretsa ndithu. Zonse zimene mfumu inachita zinawakondweretsa. 37 Kotero tsiku limeneli anthu onse ndi Aisraeli onse anadziwa kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abineri mwana wa Neri aphedwe.

38 Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu? 39 Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!”

Kuphedwa kwa Isiboseti

Isiboseti mwana wa Sauli atamva kuti Abineri waphedwa ku Hebroni, anataya mtima ndipo Aisraeli onse anachita mantha kwambiri. Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini, chifukwa anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu ndipo akhala ali kumeneko ngati alendo mpaka lero lino.

(Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti).

Choncho Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti ananyamuka kupita ku nyumba ya Isi-Boseti, ndipo anafika nthawi ya masana kukutentha pamene iye amapumula. Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa.

Iwo analowa mʼnyumbamo iye akugona pa bedi mʼchipinda chake. Atamulasa ndi kumupha, anadula mutu wake nʼkuwutenga, nayenda usiku wonse mʼnjira yopita ku Araba. Iwo anabweretsa mutu wa Isi-Boseti kwa Davide ku Hebroni ndipo anati kwa mfumu, “Nawu mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu, amene anafuna kukuphani. Lero lino Yehova wabwezera mbuye wanga mfumu adani anu, Sauli ndi ana ake.”

Davide anayankha Rekabu ndi mʼbale wake Baana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene wandipulumutsa ku mavuto anga onse, 10 pamene munthu wina anandiwuza kuti, ‘Sauli wafa’ ndipo ankaganiza kuti wabweretsa nkhani yabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha ku Zikilagi. Iyi inali mphotho imene ndinapereka kwa iyeyo chifukwa cha uthenga wake! 11 Nanji pamene anthu oyipa apha munthu wosalakwa ali mʼnyumba mwake ndiponso pa bedi lake! Kodi ine ndingaleke kukulangani ndi kukuchotsani pa dziko lapansi pano?”

12 Kotero Davide analamulira ankhondo ake, ndipo anawapha. Iwo anawadula manja ndi mapazi ndi kupachika matupi awo pa dziwe la ku Hebroni. Koma anatenga mutu wa Isi-Boseti nawuyika mʼmanda a Abineri ku Hebroni.

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli

Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu. Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”

Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli.

Davide anali ndi zaka makumi atatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka makumi anayi. Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.

Davide Alanda Mzinda wa Yerusalemu

Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.

Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.”

Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. 10 Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

11 Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu. 12 Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.

13 Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, anakwatira azikazi natenganso akazi ena kumeneko, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. 14 Mayina a ana amene anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, 15 Ibihari, Elisua, Nefegi, Yafiya, 16 Elisama, Eliada ndi Elifeleti.

Davide Agonjetsa Afilisti

17 Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga. 18 Ndipo Afilisti anabwera ndi kukhala momwazika mʼChigwa cha Refaimu. 19 Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?”

Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka ndithu mʼmanja mwako.”

20 Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu. 21 Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga.

22 Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu; 23 Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. 24 Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukayende mofulumira, chifukwa izi zikasonyeza kuti Yehova ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” 25 Kotero Davide anachita zimene Yehova anamulamulira ndipo anakantha Afilisti njira yonse kuchokera ku Geba mpaka ku Gezeri.

Luka 14:25-35

Dipo la Kutsatira Yesu

25 Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati, 26 “Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. 27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.

28 “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire? 29 Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka, 30 nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’

31 “Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000? 32 Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere. 33 Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.

34 “Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani? 35 Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja.

“Amene ali ndi makutu akumva, amve.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.