Old/New Testament
Debora
4 Ehudi atamwalira, Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. 2 Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu. 3 Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri.
4 Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo. 5 Iye ankakhala pansi pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Beteli mʼdziko la ku mapiri la Efereimu, ndipo Aisraeli ankapita kwa iye kuti akaweruze milandu yawo. 6 Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni. 7 Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ”
8 Baraki anamuyankha kuti, “Mukapita nane limodzi ine ndipita. Koma ngati sitipitira limodzi, inenso sindipita.”
9 Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. 10 Baraki anayitana mafuko a Zebuloni ndi Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu 10,000 anamutsatira, ndipo Debora anapita naye pamodzi.
11 Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi.
12 Pamene Sisera anamva kuti Baraki mwana wa Abinoamu wapita ku phiri la Tabori, 13 anasonkhanitsa magaleta ake achitsulo 900 ndi anthu onse amene anali naye ndipo anachoka ku Haroseti-Hagoyimu kupita ku mtsinje wa Kisoni.
14 Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata. 15 Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi. 16 Baraki analondola magaletawo pamodzi ndi ankhondo onse mpaka ku Haroseti-Hagoyimu, ndipo ankhondo onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe anatsala.
17 Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja.
18 Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndipo anati, “Bwerani mbuye wanga, lowani momwemo musaope.” Choncho analowa mʼtenti muja, ndipo anamufunditsa chofunda.
19 Anati, “Ndili ndi ludzu, chonde patseniko madzi pangʼono akumwa, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo anatsekula thumba la chikopa mmene munali mkaka, namupatsa kuti amwe, ndipo anamufunditsanso.
20 Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ”
21 Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo.
22 Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake.
23 “Choncho pa tsiku limenelo Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Akanaani, pamaso pa Aisraeli. 24 Ndipo Aisraeli anapanikizabe Yabini, mfumu ya Akanaani, mpaka kumuwonongeratu.
Nyimbo ya Debora
5 “Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:
2 “Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli;
ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu,
tamandani Yehova:
3 “Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu!
Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova,
Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.
4 “Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri,
pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu,
dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka
nigwetsa madzi.
5 Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,
Mulungu wa Israeli.
6 “Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati,
pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa;
alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.
7 Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi
mpaka pamene iwe Debora unafika;
unafika ngati mayi ku Israeli.
8 Pamene anasankha milungu ina,
nkhondo inabwera ku zipata za mzinda,
ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke
pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
9 Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli,
uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu.
Tamandani Yehova!
10 “Inu okwera pa abulu oyera,
okhala pa zishalo,
ndi inu oyenda pa msewu,
yankhulani. 11 Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta;
kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana;
akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli.
“Choncho anthu a Yehova
anasonkhana ku zipata za mzinda.
12 Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera;
tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo.
Iwe Baraki! nyamuka
Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’
13 “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo;
anthu a Yehova anapita
kukamenyera Yehova nkhondo
kulimbana ndi adani amphamvu.
14 Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu;
akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako.
Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri,
ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
15 Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora;
inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki,
ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira.
Koma pakati pa mafuko a Rubeni
panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
16 Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera
zitoliro zoyitanira nkhosa?
Pakati pa anthu a fuko la Rubeni
panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
17 Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani.
Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi?
Aseri anali pa gombe la Nyanja;
anangokhala mʼmadooko mwawo.
18 Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa.
Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.
19 “Mafumu anabwera, anachita nkhondo;
mafumu Akanaani anachita nkhondo
ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido,
koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
20 Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo,
zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,
chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola.
Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
22 Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu,
akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
23 Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’
‘Tembererani nzika zake mwaukali,
chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova,
kulimbana ndi adani ake amphamvu.’
24 “Akhale wodala kupambana akazi onse,
Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni;
inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.
25 Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka;
anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.
26 Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake,
anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja.
Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake,
ndi kumubowola mu litsipa mwake.
27 Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa,
anagwa; iye anagona pamenepo.
Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa;
pamene anagwera, pamenepo anaferapo.
28 “Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera;
nafuwula mokweza kuti,
‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika?
Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
29 Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha,
ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,
30 ‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane;
akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri.
Sisera akumupatsa zofunkha:
zovala zonyikidwa mu utoto,
zoti ndizivala mʼkhosi
zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’
31 “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke,
koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa
pamene lituluka ndi mphamvu zake.”
Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.
Gideoni
6 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 2 Amidiyani anapondereza Aisraeli. Tsono chifukwa cha Amidiyaniwa, Aisraeli anakonza malo obisalamo mʼmapiri ndi mʼmapanga. Anamanganso malinga. 3 Aisraeli amati akadzala mbewu, Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena akummawa amabwera ndi kudzawathira nkhondo. 4 Iwo anamanga misasa mʼdzikomo ndi kuwononga zokolola zawo zonse mpaka ku Gaza, ndipo sanawasiyireko chamoyo chilichonse Aisraeliwo, kaya nkhosa kapena ngʼombe ndi bulu yemwe. 5 Iwo ankabwera ndi zoweta zawo ndi matenti awo omwe. Ankabwera ambiri ngati dzombe, motero kuti kunali kovuta kuwawerenga anthuwo ndi ngamira zawo. Tsono iwo ankabwera ndi kuwononga dziko lonse. 6 Aisraeli anasauka chifukwa cha Amidiyani ndipo analirira kwa Yehova kuti awathandize.
7 Pamene Aisraeli analirira kwa Yehova chifukwa cha Amidiyaniwo, 8 Iye anawatumizira mneneri amene anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndine amene ndinakutsogolerani kuchokera ku Igupto. Ndinakutulutsani mʼdziko la ukapolo. 9 Ine ndinakupulumutsani ku ulamuliro wa Igupto komanso mʼmanja mwa amene amakuzunzani. Ndinawathamangitsa adani anu inu mukufika, ndikukupatsani dziko lawo.’ 10 Ndipo ndinakuwuzani kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musapembedze Milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.’ Koma inu simunandimvere.”
11 Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani. 12 Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”
13 Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.”
14 Yehova anamuyangʼana namuwuza kuti, “Pita ndi mphamvu zomwe uli nazo, ukapulumutse Aisraeli mʼmanja mwa Amidiyani. Kodi si ndine amene ndakutuma?”
15 Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.”
16 Yehova anamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo Amidiyaniwo udzawagonjetsa ngati munthu mmodzi.”
17 Gideoni anati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, ndionetseni chizindikiro kusonyeza kuti ndinudi mukuyankhula ndi ine. 18 Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.”
Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.”
19 Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja.
20 Mngelo wa Mulungu anamuwuza iye kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekewa, uziyike pa mwala uwu ndi kuthirapo msuziwu.” Ndipo Gideoni anatero. 21 Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. 22 Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!”
23 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.”
24 Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri.
25 Usiku womwewo Yehova anati kwa Gideoni, “Tenga ngʼombe ya mphongo ya abambo ako, ngʼombe ina yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ugwetse guwa la Baala limene abambo ako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pafupi pake. 26 Kenaka umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe ndi miyala yoyala bwino pamwamba pa chiwunda chimenecho. Utenge ngʼombe ya mphongo yachiwiri ija ndipo uyipereke ngati nsembe yopsereza pogwiritsa ntchito mitengo ya fano la Asera imene udule ngati nkhunizo.”
27 Choncho Gideoni anatenga antchito ake khumi nachita monga Yehova anamuwuzira. Ndipo popeza ankaopa anthu a pa banja lake ndiponso anthu a mʼmudzimo sanachite zimenezi masana koma usiku.
28 Anthu a mu mzindamo atadzuka mʼmamawa anangoona guwa la Baala litagwetsedwa ndi fano la Asera limene linali pamwamba pake litadulidwa ndiponso ngʼombe yamphongo yachiwiri ija itaperekedwa ngati nsembe yopsereza pa guwa limene linamangidwa lija.
29 Iwo anafunsana wina ndi mnzake, “Wachita zimenezi ndani?”
Atafufuza ndi kufunsafunsa, analingalira kuti, “Gideoni mwana wa Yowasi ndiye wachita zimenezi.”
30 Ndipo anthuwo anawuza Yowasi kuti, “Tulutsa mwana wako, ayenera kufa chifukwa wagumula guwa lansembe la Baala ndipo wadula fano la Asera lomwe linali pamwamba pake.”
31 Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.” 32 Choncho tsiku limenelo Gideoni anatchedwa, Yeru-Baala, kutanthauza kuti, “Baala alimbana naye, popeza anagwetsa guwa lake la nsembe.”
33 Tsopano Amidiyani, Amaleki ndi anthu ena akummawa anasonkhana ndipo atawoloka Yorodani anakamanga zinthando za nkhondo ku chigwa cha Yezireeli. 34 Ndipo Mzimu wa Yehova unatsikira pa Gideoni, ndipo anayimba lipenga kuyitana Abiezeri kuti amutsatire iye. 35 Iye anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Manase kuti akamenye nkhondo ndipo Amanase anayitanidwanso kuti amutsate. Anatumanso amithenga kwa Aseri, Azebuloni ndi Anafutali, ndipo onsewo anapita kukakumana naye.
36 Gideoni anati kwa Mulungu, “Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, 37 onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.” 38 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko.
39 Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” 40 Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame.
Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa
31 Kenaka Iye anapita ku Kaperenawo, mudzi wa ku Galileya, ndipo pa Sabata anayamba kuphunzitsa anthu. 32 Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro.
33 Mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu woyipa. Iye analira ndi mawu akulu, akuti 34 “Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
35 Yesu anachidzudzula kwambiri nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye.” Chiwandacho chinamugwetsa munthuyo pansi pamaso pa onse ndipo chinatuluka wosamupweteka.
36 Anthu onse anadabwa ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi chiphunzitso ichi ndi chotani? Ndi ulamuliro ndi mphamvu Iye akulamulira mizimu yoyipa ndipo ikutuluka!” 37 Ndipo mbiri yake inafalikira madera onse ozungulira.
Yesu Achiritsa Anthu Ambiri
38 Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize. 39 Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira.
40 Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa. 41 Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.
42 Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere. 43 Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.” 44 Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.