Old/New Testament
Aisraeli Achita Nkhondo ndi Akanaani Otsala
1 Atamwalira Yoswa Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Ndani mwa ife ayambe nkhondo yomenyana ndi Akanaani?”
2 Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe kupita. Ndawapatsa dzikolo mʼmanja mwawo.”
3 Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo.
4 Choncho Ayuda ananyamuka, ndipo Yehova anapereka Akanaani ndi Aperezi mʼmanja mwawo. Ndipo anapha anthu 10,000 ku Bezeki. 5 Ku Bezekiko anakumana ndi ankhondo a mfumu Adoni-Bezeki ndipo anamenyana nawo, ndipo Ayudawo anagonjetsa Akanaani ndi Aperezi. 6 Adoni-Bezekiyo anathawa, koma anamuthamangira ndi kumupeza, namugwira. Atamugwira anamudula zala zake zazikulu za ku manja ndi miyendo.
7 Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko.
8 Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse.
9 Kenaka Ayuda anapita kukamenyana ndi Akanaani omwe amakhala ku dziko la ku mapiri, dziko la Negevi kummwera ndiponso mu zigwa. 10 Anakalimbananso ndi Akanaani amene ankakhala ku Hebroni (mzinda womwe kale unkatchedwa Kiriyati-Araba). Kumeneko anagonjetsa Sesai, Ahimani ndi Talimai.
11 Kuchokera kumeneko, iwo anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). 12 Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” 13 Otanieli mwana wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.
14 Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani?”
15 Iye anayankha kuti, “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
16 Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki.
17 Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima. 18 Anthu a fuko la Yuda analandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lonse lozungulira, mzinda wa Asikeloni pamodzi ndi dziko lake lonse lozungulira, ndi mzinda wa Ekroni pamodzi ndi dziko lonse lozungulira.
19 Yehova anathandiza anthu a fuko la Yuda. Iwo analanda dziko la kumapiri, koma sanathe kuwachotsa anthu ku zigwa, chifukwa anali ndi magaleta azitsulo. 20 Monga analonjezera Mose, Kalebe anapatsidwa Hebroni. Kalebe anapirikitsa mafuko atatu a Anaki mu mzindamo. 21 Koma fuko la Benjamini linalephera kuwachotsa Ayebusi, amene amakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusiwo akukhalabe ndi fuko la Benjamini mu Yerusalemu mpaka lero.
22 A banja la Yosefe nawonso anathira nkhondo mzinda wa Beteli, ndipo Yehova anali nawo. 23 Anatumiza anthu kuti akazonde Beteli. Mzindawo kale unkatchedwa Luzi. 24 Anthu okazondawo anaona munthu akutuluka mu mzindamo ndipo anamuwuza kuti, “Tisonyeze njira yolowera mu mzindamu, ndipo ife tidzakuchitira chifundo.” 25 Choncho iye anawaonetsa njirayo, ndipo iwo anapha anthu onse mu mzindamo ndi lupanga koma munthu uja pamodzi ndi banja lake sanawaphe. 26 Ndipo iye anapita ku dziko la Ahiti, kumene anamangako mzinda nawutcha dzina lake Luzi. Mpaka lero lino mzindawo dzina lake ndi lomwelo.
27 Koma a fuko la Manase sanachotse nzika za mzinda wa Beti-Seani pamodzi ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena nzika za mzinda wa Taanaki ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mzinda wa Dori ndi mʼmidzi yake yozungulira. Iwo sanapirikitse nzika za mzinda wa Ibuleamu ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena mzinda wa Megido ndi mʼmidzi yake yozungulira. Choncho Akanaani anapitirirabe kukhala mʼdzikomo. 28 Aisraeli atakhala amphamvu, anawagwiritsa Akanaaniwo ntchito yakalavulagaga, koma sanawapirikitse. 29 Nawonso Aefereimu sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Gezeri, choncho Akanaaniwo ankakhalabe pakati pawo ku Gezeriko. 30 Azebuloni sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Kitironi kapena a ku Nahaloli. Iwo ankakhala pakati pawo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga. 31 A fuko la Aseri nawo sanathamangitse amene amakhala mu Ako, Sidoni, Ahilabu, Akizibu, Heliba, Afiki, ndi Rehobu. 32 Choncho anthu a fuko la Aseri anakhala pakati pa Akanaani amene ankakhala mʼdzikomo popeza sanawapirikitse. 33 Nalonso fuko la Nafutali silinathamangitse anthu amene ankakhala ku Beti Semesi kapena ku Beti Anati. Koma Anafutaliwo ankakhala pakati pa Akanaaniwo mʼdzikomo. Koma anthu amene ankakhala ku Beti Semesi ndi ku Beti Anati anawasandutsa kukhala ogwira ntchito yathangata. 34 Aamori anapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko la ku mapiri popeza sanawalole kuti atsikire ku chigwa. 35 Aamori anatsimikiza mtima zokhalabe ku phiri la Hara-Heresi, ku Ayaloni, ndiponso ku Saalibimu. Koma a fuko la Yosefe anakula mphamvu ndipo anagwiritsa Aamoriwo ntchito yakalavulagaga. 36 Malire a Aamori anayambira ku chikweza cha Akirabimu nʼkulowera ku Sela napitirira kumapita chakumapiri ndithu.
Mngelo wa Yehova ku Bokimu
2 Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu, 2 ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? 3 Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”
4 Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza, 5 ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova.
Agonjetsedwa Chifukwa Chosamvera
6 Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake. 7 Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.
8 Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110. 9 Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10 Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli. 11 Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala. 12 Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova. 13 Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti. 14 Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse. 15 Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.
16 Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo. 17 Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi. 18 Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa. 19 Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.
20 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere, 21 Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira. 22 Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.” 23 Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.
3 Iyi ndi mitundu ya anthu yomwe Yehova anayisiya kuti ayese nayo Aisraeli amene sanadziwe kumenya nkhondo mu Kanaani 2 (Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo. 3 Mitundu ya anthuyo ndi: Mafumu asanu a Afilisti, Akanaani onse, Asidoni, ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni kuyambira ku phiri la Baala-Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. 4 Iwowa Yehova anawasiya kuti aziyesa nawo Aisraeli kuti aone ngati angamvere malamulo a Yehova, amene anapatsa makolo awo kudzera mwa Mose.
5 Choncho Aisraeli anakhala pakati pa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 6 Tsono Aisraeli aja amalola ana awo aamuna ndi aakazi kuti azikwatira ndi kukwatiwa ndi anthu amitundu ina. Kenaka anayamba kupembedza milungu yawo.
Otanieli
7 Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. 8 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. 9 Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. 10 Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. 11 Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira.
Ehudi
12 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova. 13 Egiloniyo anamemeza Aamori ndi Aamaleki kupita kukamenyana ndi Israeli, ndipo analanda Yeriko, mzinda wa migwalangwa. 14 Aisraeli anatumikira ngati akapolo Egiloni mfumu ya Mowabu kwa zaka 18.
15 Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi. 16 Ndipo Ehudi anapanga lupanga lakuthwa kuwiri lotalika masentimita makumi asanu, ndipo anamangirira lupangalo pa ntchafu yake ya kumanja mʼkati mwa zovala zake. 17 Iye anakapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, amene anali munthu wonenepa kwambiri. 18 Ehudi atapereka msonkhowo, anawuza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19 Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.”
Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa.
20 Kenaka Ehudi anayandikira pafupi ndi mfumuyo, ndipo iyo inakhala yokha mʼchipinda chapamwamba, mozizira bwino. Tsono Ehudi anati, “Ndili ndi mawu ochokera kwa Mulungu woti ndikuwuzeni.” Mfumuyo itadzuka pa mpando wake waufumu, 21 Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, anasolola lupanga pa ntchafu yake ya kumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. 22 Lupanga linalowa mʼmimba pamodzi ndi chogwirira chake. Mafuta anaphimba lupangalo popeza silinatulutsidwe mʼmimbamo. Ndiponso matumbo anatuluka. 23 Kenaka Ehudi anatuluka panja pa khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapamwambacho.
24 Ehudi atachoka, atumiki a mfumu aja anabwera, ndipo ataona kuti zitseko za chipinda chapamwamba zinali zokhoma anaganiza kuti mwina mfumu ikudzithandiza mʼkatimo. 25 Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa.
26 Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri. 27 Atafika kumeneko, anayimba lipenga ku dziko la ku mapiri la Efereimu. Iye akutsogolera, Aisraeli onse anatsika naye pamodzi kuchoka ku mapiriko.
28 Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. 29 Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa. 30 Tsiku limenelo Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Israeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 80.
Samugara
31 Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli.
Kuyesedwa kwa Yesu
4 Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu, 2 kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.
3 Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.”
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”
5 Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi. 6 Ndipo anati kwa Iye, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wawo; pakuti anandipatsa ine, ndipo ndingathe kupereka kwa aliyense amene ndikufuna. 7 Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.”
8 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
9 Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano. 10 Pakuti kwalembedwa,
“Adzalamulira angelo ake za iwe
kuti akutchinjirize mosamala;
11 ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”
12 Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”
13 Mdierekezi atamaliza mayesero awa onse, anamusiya Iye kufikira atapeza mpata wina.
Yesu Akanidwa ku Nazareti
14 Yesu anabwerera ku Galileya mu mphamvu ya Mzimu Woyera, ndipo mbiri yake inafalikira ku madera onse a ku midzi. 15 Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo, ndipo aliyense ankamulemekeza.
16 Iye anapita ku Nazareti, kumene anakulira, ndipo pa tsiku la Sabata anakalowa mʼsunagoge, monga mwa chikhalidwe chake. Ndipo anayimirira kuti awerenge malemba. 17 Anamupatsa buku la mneneri Yesaya. Atalitsekula, anapeza pamalo pamene panalembedwa kuti,
18 “Mzimu wa Ambuye ali pa Ine;
chifukwa wandidzoza
kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka.
Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe
ndi kwa osaona kuti apenyenso,
kumasulidwa kwa osautsidwa,
19 ndi kulalikira za nthawi imene Ambuye adzakomere mtima anthu awo.”
20 Kenaka Iye anatseka bukulo, nalibwezera kwa wotumikira ndipo anakakhala pansi. Maso a aliyense mʼsunagogemo anali pa Iye, 21 ndipo anawawuza kuti, “Lero malemba awa akwaniritsidwa mmene mwamveramu.”
22 Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?”
23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, mudzandiwuza mwambi uwu: Singʼanga, dzichiritse wekha! Chitanso mʼmudzi wa kwanu kuno zimene ife tamva kuti Iwe unazichita ku Kaperenawo.”
24 Iye anapitiriza kuti, “Zoonadi, ndikukuwuzani kuti palibe mneneri amene amavomerezedwa ku mudzi kwawo. 25 Ine ndikukutsimikizirani kunali amayi ambiri amasiye mu Israeli mʼnthawi ya Eliya, kumwamba kutatsekedwa kwa zaka zitatu ndi theka ndipo kunali njala yayikulu mʼdziko lonselo. 26 Komabe Eliya sanatumidwe kwa mmodzi mwa iwo, koma kwa mkazi wamasiye wa ku Zerefati ku chigawo cha Sidoni. 27 Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”
28 Anthu onse mʼsunagogemo anapsa mtima atamva izi. 29 Anayimirira namutulutsira kunja kwa mzindawo, ndipo anamutengera pamwamba pa phiri pamene mzindawo unamangidwapo, ndi cholinga chakuti amuponyere ku phompho. 30 Koma Iye anangoyenda pakati pa gulu la anthulo nachokapo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.