Old/New Testament
Mizinda Yothawirako
19 Yehova Mulungu wanu akadzawononga anthu amene dziko lawo akukupatsani, ndipo inu mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼmizinda ndi mʼnyumba zawo, 2 mukapatule mizinda itatu imene ili pakati pa dziko lomwe Yehova Mulungu akukupatsani kukhala lanu. 3 Mudzakonze misewu ndi kuligawa patatu dzikolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, kuti aliyense wopha munthu akhoza kuthawirako.
4 Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wapha mnzake mosazindikira osati mwadala, nathawira kumeneko kupulumutsa moyo wake. Ndi munthu amene wapha mnzake mosazindikira, popanda maganizo oyipa. 5 Mwachitsanzo, munthu atapita ku nkhalango ndi mnzake kukadula mitengo, ndiye posamula nkhwangwa kuti adule mtengo, nkhwangwa ikhoza kuguluka nʼkukagwera mnzake uja nʼkumupha. Munthu ameneyo akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizindayo napulumutsa moyo wake. 6 Kupanda kutero ndiye kuti wolipsira akhoza kumuthamangitsa mwaukali ndi kumugwira ngati mtunda utalika, ndipo akhoza kumupha ngakhale kuti sanayenera kufa popeza sanaphe mnzake mwadala. 7 Ichi ndi chifukwa chake ndikukulamulani kuti mudzipatulire nokha mizinda itatu.
8 Ngati Yehova Mulungu wanu akulitsa malire anu monga analonjezera pa malumbiro ndi makolo anu, nakupatsani dziko lonse monga analonjezera, 9 chifukwa chotsatira bwino malamulo onse amene ndikukuwuzani lero, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse, ndiye kuti mukuyenera kupatula mizinda itatu yowonjezera. 10 Muchite zimenezi kuti musakhetse magazi wosalakwa mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa, ndipo kuti musapezeke ndi mlandu wokhetsa magazi.
11 Koma ngati munthu adana ndi mnzake namubisalira panjira nʼkumuvulaza mpaka kumupha, nathawira ku umodzi mwa mizindayi, 12 akuluakulu a mu mzinda wake akamugwire ndi kumubwezera ku mzinda wake namupereka kwa wolipsira kuti aphedwe. 13 Osamumvera chisoni. Muyenera kuchotsa tchimo lokhetsa magazi wosalakwa mu Israeli kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
14 Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Mboni
15 Mboni imodzi siyokwanira kupeza munthu kuti ndi wolakwa pa mlandu uliwonse umene wapalamula. Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.
16 Ngati mboni yonama ifuna kunamizira munthu mlandu, 17 anthu awiri okhudzidwa ndi mlanduwo ayenera kuyima pamaso pa Yehova pali ansembe ndi oweruza amene ali pa ntchito pa nthawiyo. 18 Oweruza afufuze bwinobwino, ndipo ngati zatsimikizika kuti mboniyo ndi yabodza, yopereka umboni wonama pa mʼbale wake, 19 ndiye kuti amuchitire iyeyo zimene anafuna kuchitira mʼbale wakezo. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu. 20 Anthu ena onse adzamva zimenezi nachita mantha, ndipo choyipa choterechi sichidzachitikanso pakati panu. 21 Osachita chisoni, moyo uzilipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja ndi phazi kulipira phazi.
Za ku Nkhondo
20 Pamene mukupita kokachita nkhondo ndi adani anu, mukaona akavalo kapena magaleta kapena gulu la ankhondo kuposa inuyo musamaope chifukwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto adzakhala nanu. 2 Pamene mwatsala pangʼono kuyamba nkhondo, wansembe azibwera kutsogolo ndipo aziyankhula ku gulu lonse lankhondolo. 3 Iye aziti, “Tamverani inu Aisraeli, mukupita kukachita nkhondo ndi adani anu lero. Musataye mitima kapena kuchita mantha ayi. Musaopsedwe kapena kunjenjemera pamaso pawo, 4 pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene apite nanu kukakumenyerani nkhondo ndi kugonjetsa adani anu.”
5 Akuluakulu ankhondo adzati kwa gulu la ankhondolo, “Kodi pali wina amene wangomanga nyumba kumene ndipo sanayitsekulire? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondoko ndipo wina ndi kudzayitsekulira. 6 Kodi pali wina amene analima munda wamphesa ndipo sanayambe kudyerera? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzadyerera mundawo. 7 Kodi pali amene wachita chinkhoswe ndi mkazi ndipo sanamukwatire mkaziyo? Ayambe wabwerera ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzakwatira mkaziyo.” 8 Ndipo akuluakulu ankhondowo akapitirize kuti, “Kodi pali amene akuchita mantha kapena kutaya mtima? Abwerere ku mudzi kuopa kuti abale ake angatayenso mtima.” 9 Akuluakuluwo akatsiriza kuyankhula ndi gulu la ankhondolo, adzasankhe olilamulira.
10 Pamene mukuyandikira kuphwanya mzinda, muyambe mwafunsa anthu a mu mzindawo ngati afuna zamtendere. 11 Akavomera natsekula zipata zawo, anthu wonse mu mzindawo adzagwidwa ukapolo nakugwirirani ntchito. 12 Koma akakana za mtendere nachita nanu nkhondo, muwuphwanye mzindawo. 13 Yehova Mulungu wanu akakupatsani mzindawo, muwaphe amuna onse. 14 Akazi, ana, ziweto ndi china chilichonse mu mzindamo, mukhoza kuzitenga kuti zikhale zanu monga katundu wolanda ku nkhondo. Katundu wa adani anuyu amene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, mukhoza kumugwiritsa ntchito. 15 Mizinda yonse yakutali osati ya mitundu yapafupi, muzichita nayo chomwechi.
16 Komabe mʼmizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, musasiyemo chamoyo chilichonse. 17 Muwawononge kwathunthu Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi monga momwe Yehova Mulungu wanu anakulamulirani. 18 Mukapanda kutero adzakuphunzitsani kuti mutengere zinthu zonyansa zimene amachita popembedza milungu yawo ndipo mudzachimwira Yehova Mulungu wanu.
19 Mukalimbana ndi mzinda nthawi yayitali, kuchita nawo nkhondo pofuna kuwugonjetsa, musawononge podula mitengo yake ndi nkhwangwa, osayidula chifukwa zipatso zakezo mukhoza kudya. Kodi mitengo ya ku munda ndi anthu kuti mukalimbane nayo? 20 Komabe mukhoza kudula mitengo imene mukudziwa kuti si ya zipatso ndi kuyigwiritsa ntchito pa nkhondo mpaka mzinda umene mukumenyana nawowo utagwetsedwa.
Nsembe Yopepesera Munthu Akaphedwa Mosadziwika Bwino
21 Ngati munthu apezeka ataphedwa mʼmunda mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala lanu koma inu osadziwa amene wamupha, 2 akuluakulu anu ndi oweruza adzapite ndi kuyeza kutalikirana kuchokera pamene pali mtembowo ndi mizinda yoyandikira. 3 Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzatenge ngʼombe imene sinagwirepo ntchito kapena kuvalapo goli 4 ndi kuyikusira ku chigwa chimene sichinalimidwepo ndiponso kumene kuli mtsinje woyenda. Ku chigwa kumeneko ayenera kukayithyola khosi ngʼombeyo. 5 Ansembe, ana a Aaroni, adzapite patsogolo pangʼono, popeza ndiwo amene Yehova Mulungu wanu anawasankha kuti azitumikira, kupereka mdalitso mʼdzina la Yehova ndi kugamula milandu yonse yamikangano ndi yovulazana. 6 Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzasamba mʼmanja pamwamba pa ngʼombe yothyoledwa khosi ija, 7 nadzatsimikiza kuti, “Manja athu sanakhetse magazi awa ndipo sitinaonerere kuphedwako. 8 Yehova, landirani nsembe yopepesa ya anthu anu Aisraeli amene munawapulumutsa, ndipo muwakhululukire tchimo la kupha munthu wosalakwa.” Mukatero ndiye kuti adzapezeka kuti ndi osalakwa. 9 Kotero mudzadzichotsera nokha tchimo lokhetsa magazi wosalakwa, popeza mwachita zoyenera pamaso pa Yehova.
Kukwatira Mkazi Wogwidwa ku Nkhondo
10 Mukapita kukachita nkhondo ndi adani anu, Yehova Mulungu wanu nawapereka adani anuwo mʼmanja mwanu muwagwira ukapolo, 11 ndiye ngati muona mkazi wokongola pakati pa ogwidwawo nakutengani mtima, mukhoza kumutenga kuti akhale mkazi wanu. 12 Mumutengere ku nyumba kwanu, kumumeta tsitsi lake, mumuwenge zikhadabo zake 13 ndipo avulidwe zovala zimene anagwidwa nazo. Atakhala mʼnyumba mwanu nalira maliro a abambo ndi amayi ake kwa mwezi wathunthu, ndiye mukhoza kupita kwa iye ndi kukhala mwamuna wake ndipo iyeyo adzakhala mkazi wanu. 14 Ngati simukukondweretsedwa naye, muloleni kuti apite kumene afuna. Musamugulitse kapena kumuzunza ngati kapolo, popeza mwamuchotsa ulemu.
Ufulu wa Mwana Woyamba Kubadwa
15 Ngati munthu ali ndi akazi awiri, nakonda wina koposa mnzake, onsewa ndikubereka ana aamuna koma woyamba nakhala mwana wa mkazi amene samukondayo, 16 akamagawa chuma chake akanali moyo kwa ana akewo, asapereke ufulu wa mwana woyamba kubadwa kwa mwana wamwamuna wa mkazi amene amamukonda mʼmalo mwa mwana wake woyamba kubadwa weniweni amene ndi mwana wamkazi amene samukonda. 17 Iye ayenera kuonetsa kuti mwana wake wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa pomupatsa miyeso iwiri ya zonse zimene ali nazo. Mwana wamwamuna ameneyo ndiye chizindikiro cha mphamvu za abambo ake. Ufulu wokhala mwana wamwamuna woyamba ndi wake.
Mwana Wamwamuna Wowukira
18 Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wowukira amene samvera a abambo ake ndi amayi ake akamuweruza, 19 abambo ndi amayi ake amugwire ndi kupita naye kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda wake ndipo 20 akawawuze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu wamwamunayu ndi wosamva ndi wowukira. Iyeyu satimvera. Ndi mwana wadyera komanso ndi chidakwa.” 21 Pamenepo anthu onse a mu mzinda wake adzamuphe ndi miyala. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu. Aisraeli onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha.
Malamulo Osiyanasiyana
22 Ngati munthu wopezeka ndi mlandu wopha mnzake waphedwa ndipo mtembo wake wapachikidwa pamtengo, 23 musasiye mtembowo pa mtengopo usiku wonse. Muonetsetse kuti mwakawukwirira tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu. Musayipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani ngati cholowa chanu.
21 Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. 22 Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero. 23 Choncho khalani tcheru; ndakuwuzani zonse nthawi isanafike.
24 “Koma masiku amenewo, masautsowo atatha,
“ ‘dzuwa lidzada,
ndipo mwezi sudzawala;
25 nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo,
ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’
26 “Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero. 27 Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
28 “Tsopano phunzirani phunziro ili kuchokera ku mtengo wamkuyu. Pamene msonga za nthambi zake zikhala za nthete ndipo masamba ake ayamba kuphukira, mumadziwa kuti dzinja layandikira. 29 Momwenso pamene muona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti wayandikira, ali pa khomo. 30 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 31 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Tsiku ndi Ora Sizikudziwika
32 “Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha. 33 Khalani maso! Khalani tcheru! Simudziwa pamene nthawi imeneyo idzafike. 34 Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.
35 “Inunso muyenera kukhala maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwini nyumba adzabwere, kaya madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena tambala akulira, kapena mʼbandakucha. 36 Ngati atabwera mwadzidzidzi, asadzakupezeni inu muli mtulo. 37 Zimene ndikunena kwa inu, ndikunena kwa aliyense: ‘Khalani tcheru!’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.