Old/New Testament
Miyala Ngati Yoyamba Ija
10 Pa nthawi imeneyo Yehova anati kwa ine, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo ubwere nayo kwa Ine ku phiri. Upangenso bokosi lamatabwa. 2 Ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ndipo iwe ukuyenera kuyika miyalayo mʼbokosimo.”
3 Choncho ndinapanga bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo ndinapita ku phiri nditanyamula miyala iwiri mʼmanja mwanga. 4 Yehova analemba pa miyala iwiriyo zimene analemba poyamba, Malamulo Khumi amene analengeza kwa inu pa phiri paja, mʼmoto, pa tsiku la msonkhano. Ndipo Yehova anawapereka kwa ine. 5 Tsono ndinatsika ku phiri kuja ndi kuyika miyalayo mʼbokosi ndinapanga lija monga Yehova anandilamulira, ndipo panopa ili mʼmenemo.
6 Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake. 7 Kuchokera kumeneko Aisraeli anapita ku Gudigoda, napitirira mpaka ku Yotibata, ku dziko la mitsinje ya madzi. 8 Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero. 9 Nʼchifukwa chake Alevi alibe gawo kapena cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo monga momwe Yehova Mulungu wanu anawawuzira.
10 Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni. 11 Yehova anati kwa ine, “Pita ndi kutsogolera anthuwa pa njira yawo, kuti alowe ndi kulandira dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndiwapatse.”
Kuopa Yehova
12 Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, 13 ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.
14 Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 15 Yehova anayika mtima wake pa makolo anu okha ndipo anawakondadi nasankha adzukulu awo mwa mitundu yonse pa dziko lapansi, kunena inuyo monga mulili lero. 16 Motero chitani mdulidwe wa mitima yanu ndipo musakhalenso opulupudza. 17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. 18 Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. 19 Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto. 20 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye. Mumukakamire Iyeyo ndi kuchita malumbiro anu mʼdzina lake. 21 Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija. 22 Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.
Kukonda ndi Kumvera Yehova
11 Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake. 2 Lero kumbukirani kuti si ana anu amene anaona ndi kulawa chilango cha Yehova Mulungu wanu: ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, mkono wake wotambasuka; 3 zizindikiro zozizwitsa zimene anazionetsa ndi zinthu zimene anazichita mʼkati mwa Igupto, Farao mfumu ya Igupto ndi kwa dziko lake lonse; 4 zimene Iye anachita kwa gulu lankhondo la Aigupto, kwa akavalo ndi magaleta awo, mmene Iye anawamizira ndi madzi a mu Nyanja Yofiira pamene amakuthamangitsani, ndi mmene Yehova anawagonjetsera kufikira lero. 5 Si ana anu amene anaona zimene Iye anakuchitirani mʼchipululu kufikira pamene munafika pa malo anu, 6 ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo. 7 Koma ndinuyo amene munaona ntchito zonse zikuluzikulu zimenezi Yehova anakuchitirani.
8 Tsono muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero kuti mukhale ndi mphamvu ndi kuti mupite kukalanda mʼdziko limene mwakhala pangʼono kulowamo mukawoloka Yorodani, 9 ndiponso kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu ndi zidzukulu zawo, lomwe ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi. 10 Dziko limene mukukalanda ndi kulowamo silokhala ngati dziko la ku Igupto kumene mukuchokera ayi, kuja mumadzala mbewu ndi kumathirira ndi mapazi anu ngati ku dimba. 11 Koma dziko limene mukalande mukawoloka Yorodani ndi dziko la mapiri ndi zigwa, dziko limene limalandira mvula kuchokera kumwamba. 12 Ili ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu amalisamalira. Maso a Yehova Mulungu wanu amaliyangʼanira nthawi zonse kuchokera ku mayambiriro a chaka mpaka kumapeto kwake.
13 Choncho mukasunga mokhulupirika malamulo amene ndikukupatsani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iyeyo ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, 14 pamenepo ndidzatumiza mvula mʼdziko mwanu pa nthawi yake mʼnyengo ya dzinja ndi chilimwe, kuti mudzakolole tirigu wambiri ndi kuti mudzakhale ndi vinyo watsopano ndi mafuta. 15 Ndidzakupatsani udzu mʼminda mwanu woti muzidzadyetsera ngʼombe zanu ndipo inuyo mudzadya ndi kukhuta.
16 Dzisamalireni nokha, kuopa kuti mungakopeke mtima ndi kubwerera mʼmbuyo kuyamba kutumikira milungu ina ndi kumayigwadira. 17 Mukatero Yehova Mulungu wanu adzakukwiyirani kwambiri, nadzaletsa thambo kuti lisabweretsenso mvula ndipo dziko silidzapereka zokolola. Choncho mudzawonongeka msanga mʼdziko limene Yehova akukupatsani. 18 Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu. 19 Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka. 20 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu, 21 kuti inu ndi ana anu mukhale mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu mpaka kalekale monga umakhalira mlengalenga pamwamba pa dziko.
22 Mukatsatira mosamalitsa malamulo amene ndikukupatsaniwa, kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumugwiritsitsa Iye 23 Yehova adzapirikitsa mitundu ina yonseyi inu musanafike ndipo mudzagonjetsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inu. 24 Malo aliwonse amene mudzaponda adzakhala anu: dziko lanu lidzachokera ku chipululu mpaka ku Lebanoni, ndi ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku nyanja ya kumadzulo. 25 Palibe munthu amene adzalimbana nanu. Monga analonjezera, Yehova adzachititsa kuti anthu onse mʼdziko limene mukupitalo adzachite nanu mantha ndi kukuopani.
26 Taonani, lero ndikuyika dalitso ndi temberero pakati panu, 27 dalitso ngati mumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero. 28 Temberero ngati simumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu ndi kupatuka pa njira imene ndikulamulirani lero potsata milungu ina imene simunayidziwe. 29 Yehova Mulungu wanu akakakufikitsani mʼdziko mukukalandalo kuti mulowemo mukanene za madalitso pa Phiri la Gerizimu, ndi za matemberero pa Phiri la Ebala. 30 Monga mudziwa, mapiriwa ali kutsidya kwa Yorodani, kumadzulo kolowera dzuwa, kufupi ndi mitengo ya thundu ya More, mʼdziko la Akanaani aja okhala ku Araba moyangʼanana ndi Giligala. 31 Mwatsala pangʼono kuwoloka Yorodani kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukadzalitenga dzikolo ndi kukhalamo, 32 mudzaonetsetse kuti mukumvera malangizo ndi malamulo amene ndikukuwuzani lero.
Malo Amodzi Opembedzera
12 Awa ndi malangizo ndi malamulo amene muyenera kusamalitsanso kuti muwatsatire mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani kuti mutenge pa nthawi yonse imene muti mudzakhale mʼdzikomo. 2 Muwonongeretu kwathunthu malo onse a pamwamba pa mapiri ataliatali ndi pa mapiri angʼonoangʼono ndi pansi pa mtengo uliwonse wotambalala pamene mitundu imene muyilande dzikolo ankapembedzerapo milungu yawo. 3 Mugumule maguwa awo ansembe, ndi kuphwanya miyala yawo yachipembedzo ndipo mutenthe pa moto mafano awo a Asera: mugwetse mafano a milungu yawo ndi kufafaniza mayina awo mʼmalo amenewo.
4 Musapembedze Yehova Mulungu wanu monga mmene amachitira iwowa. 5 Koma inu muzifunafuna kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati pa mafuko anu kuti ayikeko dzina lake ndi kukhalako. Ku malo amenewa muyenera kupitako. 6 Kumeneko muzipititsako zopereka zanu ndi nsembe zanu zopsereza, ndi chakhumi chanu ndi mphatso zapadera zimene munalonjeza kupereka ndi zopereka zanu zaufulu ndi ana oyamba a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. 7 Kumeneko, pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalalako pa china chilichonse chimene mudzakhudza, chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.
8 Musadzachite monga tikuchitira lero lino, aliyense kumachita zimene akuona kuti ndi zoyenera, 9 pakuti simunafike ku malo opumulirako ndi ku cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 10 Koma mudzawoloka Yorodani ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, ndipo Iye adzakupatsani inu mpumulo ku adani anu okuzungulirani kuti mukhale motchinjirizidwa. 11 Tsono kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti azikhalako muzikabweretsako chilichonse chimene ndikulamulirani inu: zopereka ndi nsembe zanu zopsereza, chakhumi chanu ndi mphatso zapadera, ndi chuma chanu chonse chosankhika chimene munalonjeza kwa Yehova. 12 Ndipo kumeneko inu mukasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamodzi ndi ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi a mʼmidzi yanu, amene alibe gawo kapena cholowa chawochawo. 13 Musamalitse kuti musakaphere nsembe zanu zopsereza paliponse pamene mungafune. 14 Mukaphere pa malo okhawo amene Yehova adzawasankhe mwa limodzi la mafuko anu, ndipo kumeneko mukasunge chilichonse chimene ndikulamulireni.
15 Koma mukhoza kumapha ziweto zanu mʼmizinda iliyonse ndi kudya nyama yake mmene mungafunire, ngati kuti ndi agwape kapena mbawala, monga mwadalitso limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Woyeretsedwa ndi wosayeretsedwa akhoza kuyidya. 16 Koma musamadye magazi. Muziwathira pansi ngati madzi. 17 Musamadyere mʼmizinda yanu chakhumi cha tirigu wanu ndi vinyo watsopano ndi mafuta, kapena za ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu, kapena chilichonse chimene mwalonjeza kuchipereka, nsembe zanu zaufulu, kapena mphatso zapadera, 18 mʼmalo mwake, muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhira inu, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi ochokera mʼmizinda yanu, ndipo mudzasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa chilichonse chimene mudzachikhudza. 19 Muonetsetse kuti musawataye Alevi pa masiku onse amene mukhale mʼdziko lanumo.
20 Yehova Mulungu wanu akadzakulitsa dziko lanu monga anakulonjezerani, ndipo mukapukwa nyama mumanena kuti, “Ndikufuna nyama,” pamenepo mudzadya mmene mungafunire. 21 Ngati malo amene Yehova Mulungu wanu awasankha kuti ayike Dzina lake ali kutali kwambiri ndi inu, mukhoza kupha ziweto pakati pa ngʼombe ndi nkhosa zimene Yehova wakupatsani, monga ndinakulamulani, ndipo mʼmizinda yanuyanu mukhoza kuzidya mmene mungafunire. 22 Muzidye ngati mukudya gwape kapena mbawala. Onse oyeretsedwa monga mwa mwambo ndi osayeretsedwa omwe akhoza kudya. 23 Koma muonetsetse kuti musadye magazi, chifukwa magazi ndi moyo, ndipo musamadye moyo pamodzi ndi nyama. 24 Inu musamadye magazi, muziwathira pansi ngati madzi. 25 Musamadye magazi kuti zikuyendereni bwino inu pamodzi ndi ana anu a pambuyo panu, popeza mudzakhala mukuchita zoyenera pamaso pa Mulungu.
26 Koma mutenge zinthu zanu zoyeretsedwa ndi china chilichonse chimene munalumbira kupereka, ndi kupita kumalo kumene Yehova adzasankhe. 27 Mupereke nsembe zanu zopsereza pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, nyama pamodzi ndi magazi omwe. Magazi a nsembe zanu athiridwe pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyamayo mukhoza kudya. 28 Onetsetsani kuti muzimvera mawu onsewa amene ndikukupatsani kuti zinthu zizikuyenderani bwino nthawi zonse inu ndi ana anu chifukwa mudzakhala mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29 Yehova Mulungu wanu adzachotsa pamaso panu mitundu ya anthu amene mukufuna kuwathira nkhondo ndi kuwalanda dzikolo. Koma mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼdziko lawo, 30 ndipo pamene iwo awonongeka pamaso panu, samalirani kuti musakodwe mu msampha pa kufufuza za milungu yawo, nʼkumati, “Kodi anthu a mitunduwa amatumikira bwanji milungu yawo? Ifenso tichita momwemo.” 31 Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.
32 Onetsetsani kuti mukuchita zimene ndikukulamulirani. Musawonjezerepo kapena kuchotserapo.
Fanizo la Alimi
12 Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. 2 Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. 3 Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. 4 Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. 5 Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.
6 “Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’
7 “Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ 8 Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.
9 “Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. 10 Kodi simunawerenge lemba lakuti:
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wakhala mwala wa pa ngodya.
11 Ambuye achita zimenezi,
ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ”
12 Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.
Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara
13 Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. 14 Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”
Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” 16 Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”
Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”
17 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
Ndipo anazizwa naye.
Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa
18 Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22 Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23 Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”
24 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25 Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26 Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27 Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.