Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 1-3

Mose Akumbutsa Aisraeli za ku Horebu

Awa ndi mawu amene Mose anayankhula kwa Aisraeli onse mʼchipululu kummawa kwa Yorodani, ku Araba moyangʼanana ndi Sufi, pakati pa Parani ndi Tofeli, Labani, Heziroti ndi Dizahabu. (Kuyenda kuchokera ku Horebu kukafika ku Kadesi Barinea kudzera njira ya ku Phiri la Seiri ndi ulendo wa masiku khumi ndi limodzi).

Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo. Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni, ndipo pa Ederi anagonjetsa Ogi mfumu ya ku Basani, amene amalamulira mu Asiteroti.

Chakummawa kwa Yorodani mʼchigawo cha Mowabu, Mose anayamba kufotokozera lamulo ili kunena kuti:

Ku Horebu, Yehova Mulungu wathu anati kwa ife, “Mwakhalitsa pa phiri lino. Sasulani msasa ndipo pitani ku dziko la mapiri la Aamori. Pitani kwa anthu onse oyandikana nawo ku Araba, ku mapiri, mʼmbali mwa mapiri a ku madzulo, ku Negevi ndiponso mʼmbali mwa nyanja, ku dziko la Akanaani ndi ku Lebanoni mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. Taonani, Ine ndakupatsani dziko ili. Lowani ndi kulilanda dziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo komanso kwa zidzukulu zawo.”

Kukhazikitsa Atsogoleri

Pa nthawi imeneyi ine ndinati kwa inu, “Inu ndinu katundu olemera kwambiri woti sindingathe kumunyamula ndekha. 10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani kotero kuti lero lino ndinu ochuluka ngati nyenyezi za kumwamba. 11 Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera! 12 Koma nanga ndekha ndidzasenza bwanji zovuta ndi zipsinjo zanu komanso milandu yanu? 13 Sankhani amuna ena anzeru, ozindikira ndi amene mumawalemekeza kuchokera ku mtundu uliwonse wa mitundu yanu, ndipo ndidzawayika kuti akulamulireni.”

14 Inu munandiyankha kuti, “Maganizo amenewa ndi abwino kuwachita.”

15 Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko. 16 Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo. 17 Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.” 18 Ndipo nthawi imeneyo ndinakuwuzani chilichonse chimene munayenera kuchita.

Atumizidwa Kukazonda Dziko

19 Tsono monga Yehova Mulungu wathu anatilamulira, tinanyamuka kuchoka ku Horebu ndi kupita cha ku dziko lamapiri la Aamori kudzera ku chipululu chachikulu ndi choopsa chija munachionachi, kotero kuti tinakafika ku Kadesi Barinea. 20 Ndipo ndinati kwa inu, “Mwafika ku dziko la mapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa. 21 Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.”

22 Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.”

23 Ndinaona kuti maganizo amenewa anali abwino, choncho ndinasankha anthu khumi ndi awiri, mmodzi ku fuko lililonse. 24 Iwo ananyamuka napita mʼdziko la mapiri, ndipo anafika ku Chigwa cha Esikolo ndi kukazonda dzikolo. 25 Pobwerera anatitengerako zipatso za mʼdzikomo ndipo anatipatsa mawu akuti, “Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.”

Awukira Yehova

26 Koma inu simunafune kupitako ndipo munawukira lamulo la Yehova Mulungu wanu. 27 Inu munanyinyirika mʼmatenti anu nʼkumati, “Mulungu amatida nʼchifukwa chake anatitulutsa ku Igupto kuti atipereke mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge. 28 Tigwire mtengo wanji? Abale athu anatitayitsa mtima. Iwo akuti, ‘Anthuwo ndi amphamvu ndi aatali kuposa ife, mizindayo ndi yayikulu ndipo mipanda yake ndi yayitali yofika kumwamba. Ife tinaonanso Aanaki kumeneko.’ ”

29 Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa. 30 Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona, 31 ndi mʼchipululu muja. Kumeneko munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani monga abambo anyamulira mwana wawo, njira yonse yomwe munayenda mpaka munafika pamalo ano.”

32 Ngakhale zinali choncho, simunadalire Yehova Mulungu wanu 33 amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo.

34 Yehova atamva zimene munanena anakwiya nalumbira kuti, 35 “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu, 36 kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.”

37 Chifukwa cha inu, Yehova anakwiyiranso ine ndipo anati, “Iwenso sudzalowa mʼdzikomo. 38 Koma Yoswa mwana wa Nuni amene amakuthandiza, adzalowa mʼdzikomo. Umulimbikitse chifukwa adzatsogolera Israeli kukalandira dzikolo. 39 Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo. 40 Koma inu, tembenukani nyamukani kulowera cha ku chipululu kutsatira njira ya ku Nyanja Yofiira.”

41 Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija.

42 Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’ ”

43 Choncho ndinakuwuzani koma simunamve. Inu munawukira lamulo la Yehova ndipo mwamwano munayenda kulowa mʼdziko la mapiri. 44 Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima. 45 Munabwererako mukulira pamaso pa Yehova, koma Iye sanalabadire kulira kwanuko ndipo sanakumvetsereni. 46 Pamenepo munakhala ku Kadesi masiku ambiri kwa nthawi yayitali ndithu.

Kuyendayenda Mʼchipululu

Kenaka tinabwerera ndi kuyamba ulendo wolowera ku chipululu motsatira njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anatilamulira. Kwa nthawi yayitali tinayendayenda cha ku dziko la mapiri la Seiri.

Ndipo Yehova anati kwa ine, “Mwazungulira mokwanira dziko la mapiri, tsopano tembenukirani kumpoto. Apatse anthu malamulo awa: ‘Muli pafupi kudutsa mʼchigawo cha abale anu adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Iwowa adzachita nanu mantha koma musamale kwambiri. Musayambane nawo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo ngakhale poti mungoyika phazi. Ndamupatsa Esau dziko lamapiri la Seiri kuti likhale lakelake. Inu muyenera kuwalipira ndi siliva pa chakudya chimene mudye ndi madzi amene mumwe.’ ”

Yehova Mulungu wanu wakudalitsani mʼntchito zonse za manja anu. Iye wakuyangʼanirani pa ulendo wanu wodutsa mʼchipululu chachikulu. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu mʼzaka makumi anayi, ndipo simunasowe kalikonse.

Choncho tinapitiriza ulendo modutsa abale athu, adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Tinapatukira njira ya ku Araba imene imachokera ku Elati ndi Ezioni Geberi ndipo tinayenda njira ya ku chipululu cha Mowabu.

Ndipo Yehova anati kwa ine, “Musawavutitse Amowabu kapena kuwaputa kuti muchite nawo nkhondo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo. Ndinapereka Ari kwa adzukulu a Loti ngati chuma chawo.”

10 (Aemi, anthu amphamvu ndi ochuluka komanso ataliatali ngati Aanaki amakhala kumeneko. 11 Ngati Aanaki, nawonso ankawayesa kuti anali Arefai, koma Amowabu ankawatcha iwo Aemi. 12 Ahori amakhala ku Seiri koma adzukulu a Esau anawapirikitsa. Iwo anawononga Ahori pamaso pawo nawakhalira pamalo pawo monga Aisraeli anachitira mʼdziko limene Yehova anawapatsa ngati chuma chawo).

13 Ndipo Yehova anati, “Tsopano nyamukani ndipo muwoloke Chigwa cha Zeredi.” Choncho tinawoloka chigwacho.

14 Panapita zaka 38 kuchokera pa nthawi imene tinachoka ku Kadesi Barinea mpaka pamene tinawoloka Chigwa cha Zeredi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mʼbado wonse wa anthu ankhondowo utawonongeka ku msasa monga Yehova anawalumbirira. 15 Dzanja la Yehova linatsutsana nawo mpaka wonse anathera ku msasa.

16 Tsono atafa munthu wotsiriza mwa anthu ankhondowo, 17 Yehova anati kwa ine, 18 “Lero mudutsa malire a Mowabu ku Ari podzera ku Ari. 19 Mukafika kwa Aamoni, musawavutitse kapena kuwaputa, popeza sindidzakupatsani gawo lililonse la dziko la Aamoni. Ine ndalipereka dzikoli ngati chuma kwa adzukulu a Loti.”

20 (Ilinso ankaliyesa dziko la Arefai amene ankakhala kumeneko. Koma Aamoni ankawatcha iwo Azamuzumi. 21 Iwo anali anthu amphamvu ndiponso ochuluka, ataliatali ngati Aanaki. Yehova anawawononga ndi kuwachotsa pamaso pa Aamoni, amene anawapirikitsa nawakhalira pa malo pawo. 22 Yehova anachitanso chimodzimodzi ndi adzukulu a Esau omwe anakhazikika ku Seiri atawononga Ahori powachotsa pamaso pawo. Iwo anawapirikitsa Ahoriwo ndi kuwakhalira pamalo pawo mpaka lero. 23 Ndipo za Aavi omwe ankakhala mʼmidzi yofika mpaka ku Gaza, anagonjetsedwa ndi Akafitori wochokera ku Akafitori nakhala pamalo pawo).

Kugonjetsedwa kwa Sihoni Mfumu ya ku Hesiboni

24 “Tsopano nyamukani, muwoloke khwawa la Arinoni. Taona ndapereka mʼmanja mwako Sihoni Mwamori mfumu ya Hesiboni ndi dziko lake lonse. Yambapo kutenga chuma chake ndi kumenyana naye nkhondo. 25 Lero lomwe lino ndidzayamba kuyika chiopsezo ndi mantha pa mitundu yonse pansi pa thambo kuti akuope. Iwowo adzamva zambiri yako ndipo adzanjenjemera ndi kuwawidwa mtima chifukwa cha iwe.”

26 Ine ndinatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti kupita kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni kukanena mawu ofuna mtendere ndipo ndinati, 27 “Tiloleni tidutse mʼdziko mwanu. Ife tidzangodutsa ndi msewu waukulu, ndipo sitidzapatukira kumanja kapena kumanzere. 28 Mutigulitse chakudya kuti tidye ndi madzi kuti timwe pa mtengo wa siliva. Mungotilola kuti tidutse, tikuyenda pansi 29 monga mmene anatichitira adzukulu a Esau okhala ku Seiri ndi Amowabu okhala ku Ari mpaka titawoloka Yorodani kufika ku dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.” 30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanalole kuti tidutse. Popeza Yehova Mulungu wanu analimbitsa mzimu wake, nawumitsa mtima wake kuti amupereke mʼmanja mwanu monga wachitira lero lino.

31 Yehova anati kwa ine, “Taona ndayamba kumupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Tsopano yamba kugonjetsa ndi kulanda dziko lake.”

32 Sihoni ndi ankhondo ake atabwera kudzakumana nafe mwankhondo pa Yahazi, 33 Yehova Mulungu anamupereka iye kwa ife ndipo tinankantha, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse lankhondo. 34 Pa nthawi imeneyi tinamulanda mizinda yake yonse ndi kuyiwononga kwathunthu, amuna, akazi ndi ana. Palibe amene anapulumuka. 35 Koma ziweto ndi zinthu zonse zimene tinalanda mʼmizinda imene tinagonjetsayo, tinazitenga kukhala zathu. 36 Kuchokera ku Aroeri mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni ndi ku mzinda wa ku mtsinjeko mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe ndi mzinda ndi umodzi omwe umene unatikanika kuwugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anatipatsa onsewo. 37 Molingana ndi lamulo la Yehova Mulungu wathu, simunalowerere dziko lililonse la Aamoni, ngakhale dera lonse la ku mtsinje wa Yaboki kapena dera lozungulira dera la ku mizinda ya ku mapiri.

Kugonjetsedwa kwa Ogi Mfumu ya ku Basani

Kenaka tinakhota ndi kumayenda mokwera mtunda ndi njira yolowera ku Basani. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anakumana nafe ndipo anamenyana nafe ku Ederi. Yehova anati kwa ine, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”

Choncho Yehova Mulungu wathu anapereka mʼmanja mwathu Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo. Tinawakantha onsewo osasiya ndi mmodzi yemwe. Pa nthawi imeneyo tinatenga mizinda yake yonse. Pa mizinda 60, panalibe ndi umodzi womwe umene sitinawalande, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basani chimene ndi chigawo cha Arigobu. Mizinda yonseyi inali yotetezedwa ndi malinga ataliatali wokhala ndi zitseko ndi zitsulo, komabe panali midzi ina yambiri imene inalibe malinga. Tinawawonongeratu monga momwe tinachitira Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Tinawononga mzinda uliwonse, amayi, amuna ndi ana omwe. Koma tinafunkha ziweto ndi katundu wawo yense.

Choncho pa nthawi imeneyi tinalanda kwa mafumu awiri Aamori, dera la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku khwawa la Arinoni mpaka ku Phiri la Herimoni. (Asidoni amatcha Herimoni kuti Siriyoni, pamene Aamori amalitcha Seniri). 10 Tinalanda mizinda yonse ya ku mapiri, ku Giliyadi, Basani mpaka ku Saleka ndi Ederi, mizinda ya mu ufumu wa Ogi wa ku Basani. 11 (Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori).

Kugawana Dziko

12 Dziko limene tinalanda nthawi imeneyo, ndinapatsa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi dera la kumpoto kwa Aroeri cha mʼmphepete mwa khwawa la Arinoni kuphatikizapo theka la dziko lamapiri la Giliyadi ndi mizinda yake. 13 Theka la fuko la Manase ndinalipatsa dziko lonse lotsala la Giliyadi ndi Basani yense yemwe ndi dera la ufumu wa Ogi. (Chigawo chonse cha Arigobu mu Basani chinkadziwika kuti ndi dziko la Arefai. 14 Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi). 15 Ndipo ndinapereka Giliyadi kwa Makiri. 16 Koma kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi ndinapereka chigawo chochokera ku Giliyadi kutsetsereka mpaka ku khwawa la Arinoni (pakati pa khwawalo ndiye panali malire) ndi kupitirira mpaka ku mtsinje wa Yaboki umene ndi malire Aamoni. 17 Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga.

18 Ndinakulamulirani nthawi imene ija kuti, “Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili kuti likhale lanu. Koma amuna amphamvu onse ali ndi zida zankhondo, awoloke kutsogolera abale anu Aisraeli. 19 Koma akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri) zikhoza kumakhalabe mʼmizinda imene ndakupatsani, 20 mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, nawonso atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa patsidya pa Yorodani, monga wachitira ndi inu. Kenaka, aliyense wa inu akhoza kudzabwerera ku dziko limene ndinakupatsani.”

Mose Aletsedwa Kuwoloka Yorodani

21 Nthawi imeneyo ndinamulamula Yoswa kuti, “Waona wekha ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wako anachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachita zomwezo ndi mafumu ena onse kumene mukupitako. 22 Musawaope chifukwa Yehova Mulungu mwini adzakumenyerani nkhondo.”

23 Nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24 “Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita? 25 Mundilole ndipite ndi kukaona dziko labwinolo kutsidya kwa Yorodani dziko la mapiri abwinowo ndi Lebanoni.”

26 Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi. 27 Pita pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo uyangʼane kumadzulo, kumpoto, kummwera ndi kummawa. Ulione dzikolo ndi maso ako pakuti suwoloka Yorodaniyu. 28 Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.” 29 Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori.

Marko 10:32-52

Yesu Aneneratunso za Imfa Yake

32 Ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu, Yesu ali patsogolo, ophunzira ake anadabwa, ndipo amene amamutsatira amachita mantha. Anatenganso ophunzira ake khumi ndi awiri pa mbali ndipo anawawuza zimene zikamuchitikire Iye. 33 Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina, 34 amene adzamuchita chipongwe ndi kumuthira malovu, kumukwapula ndi kumupha. Patatha masiku atatu adzauka.”

Pempho la Yakobo ndi Yohane

35 Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, “Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe.”

36 Iye anafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani?”

37 Iwo anayankha kuti, “Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu.”

38 Yesu anati, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwere chikho chimene ndidzamwera kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwe nawo?”

39 Iwo anayankha kuti, “Tikhoza.” Yesu anawawuza kuti, “Mudzamweradi chikho chimene Ine ndidzamwera, ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwe nawo, 40 koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”

41 Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane. 42 Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo. 43 Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira, 44 ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. 45 Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”

Bartumeyu Wosaona

46 Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. 47 Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, “Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

48 Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

49 Yesu anayima nati, “Muyitaneni.” Ndipo anamuyitana kuti, “Kondwera! Imirira! Akukuyitana.” 50 Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.

51 Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?”

Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.”

52 Yesu anati, “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!” Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.