Old/New Testament
Mafuko a ku Tsidya la Yorodani
32 Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo. 2 Choncho Arubeni ndi Agadi anapita kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa atsogoleri a anthu ndi kunena kuti, 3 “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni, 4 dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto. 5 Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’ ”
6 Ndipo Mose anati kwa Agadi ndi Arubeni, “Kodi anthu a mtundu wanu apite ku nkhondo inu mutangokhala kuno? 7 Chifukwa chiyani mukufowoketsa Aisraeli kupita mʼdziko limene Yehova wawapatsa? 8 Izi ndi zimene makolo anu anachita pamene ndinawatuma kuchokera ku Kadesi kukaona dzikolo. 9 Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa. 10 Yehova anakwiya tsiku limenelo ndipo analumbira kuti, 11 ‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 12 Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ 13 Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha.
14 “Ndipo onani tsopano, inu mʼbado wochimwa, mwalowa mʼmalo mwa makolo anu ndipo mwachititsa kuti Yehova akwiyire Israeli kwambiri. 15 Ngati muleka kumutsata, Iye adzawasiyiranso anthu onsewa mʼchipululu ndipo mudzawonongetsa anthu onsewa.”
16 Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu. 17 Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli. 18 Sitidzabwerera ku midzi yathu mpaka Mwisraeli aliyense atalandira cholowa chake. 19 Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.”
20 Tsono Mose anati kwa anthuwo, “Ngati inu mudzachita zimenezi, kutenga zida zankhondo pamaso pa Yehova kuti muchite nkhondo, 21 ndipo ngati nonsenu mudzapita ndi zida kuwoloka Yorodani pamaso pa Yehova mpaka atachotsa adani ake pamaso pake, 22 dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.
23 “Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani. 24 Amangireni akazi ndi ana anu mizinda, mangani makola a ziweto zanu, koma chitani zomwe mwalonjeza.”
25 Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira. 26 Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi, 27 koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.”
28 Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli. 29 Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo. 30 Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani.
31 Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena. 32 Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.”
33 Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira.
34 Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri, 35 Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha, 36 Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo. 37 Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu, 38 Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo.
39 Zidzukulu za Makiri mwana wa Manase zinapita ku Giliyadi kulanda mzindawo ndi kuthamangitsira kunja Aamori omwe anali kumeneko. 40 Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko. 41 Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi. 42 Ndipo Noba analanda Kenati ndi midzi yozungulira ndi kuyitcha Noba, kutengera dzina la iye mwini.
Malo omwe Aisraeli Anayima pa Ulendo Wawo
33 Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni. 2 Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa:
3 Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona, 4 pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.
5 Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti.
6 Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu.
7 Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.
8 Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara.
9 Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.
10 Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.
11 Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini.
12 Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika.
13 Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi.
14 Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa.
15 Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai
16 Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava.
17 Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti.
18 Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima.
19 Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi.
20 Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina.
21 Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa.
22 Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata.
23 Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi.
24 Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada.
25 Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti.
26 Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati.
27 Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera.
28 Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika.
29 Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona.
30 Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti.
31 Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani.
32 Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi.
33 Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata.
34 Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona.
35 Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi.
36 Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi.
37 Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu. 38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. 39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.
40 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera.
41 Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni.
42 Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni.
43 Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti.
44 Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu.
45 Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi.
46 Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu.
47 Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo.
48 Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. 49 Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu.
50 Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, 51 “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, 52 mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. 53 Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo. 54 Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.
55 “ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo. 56 Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ”
Malire a Dziko la Kanaani
34 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
3 “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. 4 Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, 5 kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
6 “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
7 “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori 8 ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, 9 ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. 11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. 12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere.
“ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”
13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, 14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. 15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. 18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. 19 Mayina awo ndi awa:
Kalebe mwana wa Yefune,
wochokera ku fuko la Yuda,
20 Semueli mwana wa Amihudi,
wochokera ku fuko la Simeoni;
21 Elidadi mwana wa Kisiloni,
wochokera ku fuko la Benjamini;
22 Buki mwana wa Yogili,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
23 Hanieli mwana wa Efodi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
24 Kemueli mwana wa Sifitani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
25 Elizafani mwana wa Parinaki,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
26 Palitieli mwana wa Azani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
27 Ahihudi mwana wa Selomi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
28 Pedaheli mwana wa Amihudi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.
Yesu aneneratu za Imfa yake Kachiwiri
30 Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali, 31 chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.” 32 Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.
Wamkulu Ndani mu Ufumu wa Mulungu?
33 Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti, “Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?” 34 Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.
35 Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”
36 Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, 37 “Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
Wosatsutsana Nafe Athandizana Nafe
38 Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”
39 Yesu anati, “Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine, 40 pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu. 41 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”
Zochimwitsa Ena
42 “Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake. 43 Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. 44 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). 45 Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. 46 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). 47 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, 48 kumene
“ ‘mphutsi zake sizifa
ndipo moto wake suzima.’
49 Aliyense adzayesedwa ndi moto.
50 “Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.