Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 17-19

Kuphukira kwa Ndodo ya Aaroni

17 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake. Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse. Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe. Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.”

Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo. Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano.

Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi. Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake.

10 Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.” 11 Mose anachita monga Yehova anamulamulira.

12 Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika! 13 Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?”

Ntchito za Ansembe ndi Alevi

18 Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni. Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe. Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu.

“Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli. Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano. Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.

Zopereka za Ansembe ndi Alevi

“Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. 10 Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika.

11 “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako.

12 “Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. 13 Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako.

14 “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. 15 Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. 16 Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika.

17 “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 18 Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. 19 Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.”

20 Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli.

21 “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. 22 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. 23 Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. 24 Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ”

25 Yehova anati kwa Mose, 26 “Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. 27 Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa. 28 Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. 29 Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’

30 “Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa. 31 Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano. 32 Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’ ”

Phulusa ndi Madzi Oyeretsera

19 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: “Lamulo limene Yehova wapereka ndi ili: Uzani Aisraeli kuti abweretse ngʼombe yayikazi yofiira yopanda chilema chilichonse imenenso sinakhalepo pa goli. Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo. Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano. Wansembeyo akuona, ngʼombeyo ayiwotche chikopa chake, mnofu wake, magazi ake ndi zamʼkati zake. Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo. Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

“Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo. 10 Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo.

11 “Aliyense wokhudza mtembo wa munthu wina aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. 12 Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa. 13 Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo.

14 “Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, 15 ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa.

16 “Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri.

17 “Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino. 18 Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda. 19 Munthu woyeretsedwa ndiye awaze munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amuyeretse. Munthu amene akuyeretsedwayo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa. 20 Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa. 21 Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo.

“Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.”

Marko 6:30-56

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

30 Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa. 31 Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”

32 Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha. 33 Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika. 34 Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35 Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. 36 Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.”

37 Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.”

Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”

38 Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.”

Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.”

39 Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. 40 Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. 41 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. 42 Onse anadya ndipo anakhuta, 43 ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. 44 Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.

Yesu Ayenda pa Nyanja

45 Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. 46 Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.

47 Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. 48 Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, 49 koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, 50 pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.

Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” 51 Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, 52 popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.

53 Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko. 54 Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu. 55 Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye. 56 Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.