Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 7-8

Zopereka Popatula Chihema

Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka. Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema.

Yehova anawuza Mose kuti, “Ulandire zimenezi kwa iwo kuti zigwire ntchito ku tenti ya msonkhano. Uzipereke kwa Alevi, aliyense monga mwa ntchito yake.”

Choncho Mose anatenga ngolo ndi ngʼombe zothenazo nazipereka kwa Alevi. Anapereka ngolo ziwiri ndi ngʼombe zothena zinayi kwa Ageresoni monga mwantchito yawo ndiponso anapereka ngolo zinayi ndi ngʼombe zothena zisanu ndi zitatu kwa Amerari molingananso ndi ntchito yawo. Onsewa ankawayangʼanira anali Itamara mwana wa Aaroni wansembe. Koma Mose sanapereke zimenezi kwa Akohati chifukwa zinthu zawo zopatulika zomwe ankayangʼanira zinali zoti azinyamula pa mapewa awo.

10 Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo. 11 Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, “Tsiku lililonse mtsogoleri mmodzi azibweretsa chopereka chake chopatulira guwa lansembe.”

12 Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda.

13 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, ndi beseni lasiliva limodzi lowazira, lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo wopatulika ndipo zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka chachakudya; 14 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 15 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 16 mbuzi yayimuna imodzi, nsembe ya machimo; 17 ndi ngʼombe zothena ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Naasoni mwana wa Aminadabu.

18 Pa tsiku lachiwiri, Natanieli mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa Isakara, anabweretsa chopereka chake.

19 Chopereka chomwe anabwera nacho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, molingana ndi muyeso wa ku malo opatulika. Mbale zonse zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha chakudya. 20 Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110 yodzaza ndi lubani; 21 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza: 22 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yotetezera machimo; 23 ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi, nsembe ya chiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Netanieli mwana wa Zuwara.

24 Pa tsiku lachitatu, Eliabu mwana wa Heloni, mtsogoleri wa Azebuloni, anabweretsa chopereka chake.

25 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, mbale zonse zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka cha chakudya; 26 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 27 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 28 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 29 ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliabu mwana wa Heloni.

30 Tsiku lachinayi linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa fuko la Rubeni, anabweretsa chopereka chake.

31 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka chachakudya. 32 Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 33 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 34 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 35 ndi ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri.

36 Pa tsiku lachisanu Selumieli mwana wa Zurisadai, mtsogoleri wa fuko la Simeoni, anabweretsa chopereka chake.

37 Chopereka chake chinali mbale yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 38 mbale yagolide imodzi yolemera 110, yodzaza ndi lubani; 39 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wamwamuna wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 40 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 41 ngʼombe ziwiri, nkhosa zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Selumieli mwana wa Zurisadai.

42 Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Eliyasafu mwana wa Deuweli, mtsogoleri wa fuko la Gadi, anabweretsa chopereka chake.

43 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 44 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 45 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, chopereka cha nsembe yopsereza: 46 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 47 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuweli.

48 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa fuko la Efereimu, anabweretsa chopereka chake.

49 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonsezi monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 50 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 51 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 52 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 53 ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi.

54 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Gamalieli mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa fuko Manase, anabweretsa chopereka chake.

55 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 56 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani, 57 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 58 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 59 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Gamalieli mwana wa Pedazuri.

60 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi Abidani mwana wa Gideoni mtsogoleri wa fuko la Benjamini, anabweretsa chopereka chake.

61 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha zakudya; 62 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 63 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 64 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 65 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni.

66 Pa tsiku lakhumi Ahiyezeri mwana wa Amisadai, mtsogoleri wa fuko la Dani anabweretsa chopereka chake.

67 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 68 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 69 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 70 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 71 ndi ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

72 Pa tsiku la khumi ndi chimodzi, Pagieli mwana wa Okirani, mtsogoleri wa fuko la Aseri, anabweretsa chopereka chake.

73 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 74 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 75 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 76 mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo; 77 ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Pagieli mwana wa Okirani.

78 Pa tsiku la khumi ndi chimodzi Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa fuko la Nafutali, anabweretsa chopereka chake.

79 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 80 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 81 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 82 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 83 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahira mwana wa Enani.

84 Zopereka za atsogoleri a Israeli zopatulira guwa lansembe pamene linadzozedwa zinali izi: mbale khumi ndi ziwiri zasiliva, mabeseni owazira asiliva khumi ndi awiri ndi mbale zagolide khumi ndi ziwiri. 85 Mbale iliyonse yasiliva inkalemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndipo beseni lililonse lowazira linkalemera magalamu 800. Pamodzi, mbale zonse zasiliva zinkalemera makilogalamu 27 monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. 86 Mbale khumi ndi ziwiri zagolide zodzaza ndi lubanizo zinkalemera magalamu 110 iliyonse, monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Pamodzi, mbale zagolide zinkalemera kilogalamu imodzi ndi theka. 87 Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yopsereza chinali motere: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, nkhosa zazimuna khumi ndi ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi awiri a chaka chimodzi pamodzi ndi chopereka chachakudya. Mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri zinali za nsembe yopepesera machimo. 88 Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa.

89 Mose atalowa mu tenti ya msonkhano kukayankhula ndi Yehova, anamva mawu kuchokera pakati pa Akerubi awiri amene anali pamwamba pa chivundikiro cha bokosi la umboni. Ndipo anayankhula naye.

Za Nyale

Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.”

Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose. Choyikapo nyalecho chinapangidwa motere: chinasulidwa kuchokera ku golide, kuyambira pa tsinde pake mpaka ku maluwa ake. Choyikapo nyalecho chinapangidwa monga momwe Yehova anaonetsera Mose.

Za Kupatulidwa kwa Alevi

Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga Alevi pakati pa Aisraeli ndipo uwayeretse. Powayeretsa uchite izi: uwawaze madzi oyeretsa ndipo amete thupi lawo lonse ndi kuchapa zovala zawo kuti adziyeretse. Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo. Ubwere nawo Aleviwo kutsogolo kwa tenti ya msonkhano ndipo usonkhanitse gulu la Aisraeli. 10 Ubwere nawo pamaso pa Yehova, ndipo Aisraeli asanjike manja awo pa iwo. 11 Aaroni apereke Alevi aja pamaso pa Yehova ngati chopereka choweyula kuchokera kwa Aisraeli kuti akhale okonzeka kugwira ntchito ya Yehova.

12 “Alevi akatsiriza kusanjika manja awo pa mitu ya ngʼombe zazimuna, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza ya kwa Yehova, kupepesera machimo a Alevi. 13 Uyimiritse Aleviwo pamaso pa Aaroni ndi ana ake aamuna ndipo uwapereke ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. 14 Pochita zimenezi mudzapatula Alevi pakati pa Aisraeli ndipo Aleviwo adzakhala anga.

15 “Utatha kuyeretsa ndi kupereka Aleviwo monga nsembe yoweyula, apite kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano. 16 Iwo ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwathunthu kwa Ine. Ndawatenga kuti akhale anga mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Mwisraeli aliyense wamkazi. 17 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. 18 Ndipo ndatenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa mu Israeli. 19 Mwa Aisraeli onse, ndapereka Alevi kuti akhale mphatso kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kugwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti azikapereka nsembe yopepesera machimo, kuti mliri usadzaphe Aisraeli pamene ayandikira ku malo wopatulika.”

20 Mose, Aaroni pamodzi ndi gulu lonse la Israeli anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. 21 Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa. 22 Zitatha zimenezi, Alevi anapita kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose.

23 Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Ntchito za Alevi ndi izi: Amuna a zaka 24 kapena kuposera pamenepa ndiye azibwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano. 25 Koma akakwana zaka makumi asanu, apume pa ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku ndi kulekeratu kugwira ntchitoyo. 26 Atha kuthandiza abale awo kugwira ntchito za ku tenti ya msonkhano, koma iwowo asamagwire ntchitoyo. Mmenemu ndimo ugawire ntchito yomwe azigwira Alevi.”

Marko 4:21-41

Fanizo la Nyale

21 Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? 22 Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera. 23 Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”

24 Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri. 25 Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”

Fanizo la Mbewu Imene Ikukula

26 Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. 27 Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. 28 Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. 29 Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”

Fanizo la Mbewu ya Mpiru

30 Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? 31 Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. 32 Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”

33 Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa. 34 Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.

Yesu Aletsa Namondwe

35 Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.” 36 Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. 37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”

39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.

40 Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”

41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.