Old/New Testament
23 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.
Za Sabata
3 “ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.
Za Paska ndi za Buledi Wopanda Yisiti
4 “ ‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake: 5 Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. 6 Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. 7 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse. 8 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ”
Za Zipatso Zoyambirira Kucha
9 Yehova anawuza Mose kuti, 10 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo ndi kukolola za mʼminda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa tirigu woyambirira kucha wa mʼminda mwanu. 11 Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Yehova kotero mtolowo udzalandiridwa mʼmalo mwanu. Wansembe auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata. 12 Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 13 Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka. 14 Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
Chikondwerero cha Masabata
15 “ ‘Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, tsiku limene munabwera ndi mtolo wa nsembe yoweyula, muziwerenga masabata asanu ndi awiri athunthu. 16 Ndiye kuti muwerenge masiku makumi asanu kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata la chisanu ndi chiwiri, ndipo kenaka mupereke nsembe ya tirigu watsopano kwa Yehova. 17 Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha. 18 Pamodzi ndi bulediyu muperekenso ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, aliyense akhale wa chaka chimodzi ndi wopanda chilema. Pakhalenso ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa zazimuna ziwiri. Zimenezi zidzakhala nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova pamodzi ndi nsembe za zakudya ndi nsembe za zakumwa. Zonsezi zikhale nsembe zopsereza za fungo lokomera Yehova. 19 Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano. 20 Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe. 21 Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
22 “ ‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
Chikondwerero cha Malipenga
23 Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga. 25 Musagwire ntchito zolemetsa koma mupereke nsembe yopsereza kwa Yehova.’ ”
Tsiku Lopepesera Machimo
26 Yehova anawuza Mose kuti, 27 “Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi tsiku lochita Mwambo Wopepesera Machimo. Muzichita msonkhano wopatulika. Muzidzichepetsa pamaso pa Yehova ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. 28 Tsiku limeneli musamagwire ntchito chifukwa ndi tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo, kupepesera machimo anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29 Munthu aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 30 Aliyense wogwira ntchito tsiku limeneli ndidzamuwononga pakati pa anthu a mtundu wake. 31 Inu musadzagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale. 32 Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.”
Chikondwerero cha Misasa
33 Yehova anawuza Mose kuti, 34 “Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova. 35 Tsiku loyamba ndi la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zolemetsa. 36 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa.
37 (“ ‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku. 38 Zopereka zimenezi ndi zowonjezera pa zopereka za Yehova za pa Sabata, zopereka zanu zolumbira ndiponso mphatso zanu zaufulu zopereka kwa Yehova.)
39 “ ‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso. 40 Pa tsiku loyamba muzitenga zipatso zabwino kwambiri zothyola mʼmitengo, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondozi yakumtsinje, ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu kwa masiku asanu ndi awiri. 41 Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri. 42 Muzikhala mʼmisasa masiku asanu ndi awiri. Onse amene ali mbadwa mʼdziko la Israeli azikhala mʼmisasa 43 kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
44 Choncho Mose analengeza kwa Aisraeli masiku osankhika a zikondwerero za Yehova.
Mafuta ndi Buledi wa Pamaso pa Yehova
24 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse. 3 Kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, mʼchihema cha msonkhano, Aaroni azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa, nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yonse. 4 Aaroni ayatse nyale zimene zili pa choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri kuti zikhale zoyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova.
5 “Mutenge ufa wosalala ndipo muphike makeke khumi ndi awiri ndipo keke iliyonse ikhale ya ufa wa makilogalamu awiri. 6 Muwayike pa tebulo la golide wabwino kwambiri pamaso pa Yehova mʼmizere iwiri. Mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi. 7 Pa mzere uliwonse muyikepo lubani wafungo lokoma kuti pamodzi ndi bulediyo akhale wachikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova. 8 Sabata ndi sabata nthawi zonse Aaroni aziyika makeke amenewa pamaso pa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti akhale pangano lamuyaya. 9 Chakudyacho ndi cha Aaroni ndi ana ake ndipo azidyera ku malo wopatulika chifukwa kwa iye chakudyacho ndi chopatulika kwambiri chochokera pa chopereka chopsereza cha Yehova.”
Woyankhula Monyoza Mulungu Aphedwa ndi Miyala
10 Tsiku lina munthu wina wamwamuna amene amayi ake anali Mwisraeli koma abambo ake anali Mwigupto anapita kwa Aisraeli ndipo anakangana ndi Mwisraeli wina ku msasa. 11 Munthu uja ananyoza dzina la Yehova ndi kulitemberera. Choncho anabwera naye kwa Mose. Dzina la amayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. 12 Anamuyika mʼndende mpaka atadziwa bwino chofuna cha Yehova.
13 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 14 “Pita naye kunja kwa msasa munthu wotembererayo. Onse amene anamumva akutemberera asanjike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse la anthu limugende miyala. 15 Choncho uza Aisraeli kuti, ‘Aliyense wotemberera Mulungu wake alangidwe. 16 Aliyense wonyoza dzina la Yehova, mlendo ngakhale mbadwa, aphedwe. Gulu lonse la anthu limuponye miyala.
17 “ ‘Ngati munthu wina aliyense achotsa moyo wa munthu mnzake, munthuyo ayenera kuphedwa. 18 Aliyense wopha chiweto cha mnzake ayenera kulipira china. Moyo kulipa moyo. 19 Ngati munthu avulaza mnzake, nayenso amuchite zomwe wachitira mnzakeyo: 20 kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Monga momwe anavulazira mnzake, amuvulaze chimodzimodzinso. 21 Aliyense wopha chiweto cha mnzake, alipire chiweto china, koma aliyense wopha munthu ayenera kuphedwa. 22 Lamulo la mlendo ndi mbadwa ndi limodzi lomweli. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
23 Pamenepo Mose anawuza Aisraeli zimenezi, ndipo iwo anatulutsira munthu wotembererayo kunja kwa msasa ndi kumugenda miyala. Aisraeli anachita zimene Yehova analamula Mose.
Yohane Mʼbatizi Akonza Njira
1 Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, 2 monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya:
“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
amene adzakonza njira yanu,”
3 “Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.’ ”
4 Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. 5 Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani. 6 Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo. 7 Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. 8 Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
Kubatizidwa ndi Kuyesedwa kwa Yesu
9 Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 10 Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. 11 Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
12 Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, 13 ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino
14 Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15 “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
16 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. 17 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. 20 Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa
21 Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa. 22 Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.