Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 21-22

Malamulo a Ansembe

21 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi ansembe, ana a Aaroni, ndipo uwawuze kuti, ‘Wansembe asadzidetse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake. Koma akhoza kukhudza thupi lakufa la amayi ake, abambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake, kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amadalira iye chifukwa sanakwatiwe. Iye akhoza kudzidetsa pokhudza thupi lakufa la mchemwali wake wosakwatiwa yekha. Koma wansembe asadzidetse chifukwa cha anthu amene ali nawo pa ubale obwera chifukwa cha ukwati.

“ ‘Ansembe asamete tsitsi kumutu kwawo kapena mʼmphepete mwa ndevu zawo, kapenanso kudzichekacheka pa thupi lawo. Ayenera kukhala oyera pamaso pa Mulungu wawo ndipo asachititse manyazi dzina la Mulungu wawo. Popeza amapereka nsembe zotentha pa moto kwa Yehova, chakudya cha Mulungu wawo, iwo azikhala woyera.

“ ‘Asakwatire akazi amene adzidetsa ndi chiwerewere kapena akazi amene amuna awo awasudzula, chifukwa ansembe ndi oyera pamaso pa Mulungu wawo. Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera.

“ ‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto.

10 “ ‘Munthu amene ali mkulu wa ansembe pakati pa abale ake, amene anamudzoza pomutsanulira mafuta pamutu pake, ndiponso amene anapatulidwa pomuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake kapena kungʼamba zovala zake kusonyeza kuti ali pa chisoni. 11 Asalowe mʼnyumba mmene muli munthu wakufa ngakhale womwalirayo ndi amayi ake kapena abambo ake. 12 Asadzidetse potulukira kunja kwa malo opatulika popeza mafuta womupatula kukhala wansembe ali pamutu pake. Ine ndine Yehova.

13 “ ‘Iye akwatire namwali wosadziwa mwamuna. 14 Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, 15 kuti mtundu wake usakhale wodetsedwa pakati pa abale popeza ndine Yehova, amene ndimamuyeretsa.’ ”

16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Muwuze Aaroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa zidzukulu zake ku mibado yawo yonse ikubwera akakhala ndi chilema asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake. 18 Munthu aliyense wachilema motere: munthu wakhungu kapena wolumala miyendo, munthu wolumala nkhope kapena waziwalo zambiri, 19 munthu wa phazi lolumala kapena dzanja lolumala, 20 kapena munthu wokhota msana kapena wamfupi kwambiri, kapena wolumala maso, munthu wa nthenda yonyerenyetsa, kapena wamphere, kapenanso wophwanyika mavalo, sayenera kusendera pafupi. 21 Mdzukulu aliyense wa Aaroni wansembe, amene ali ndi chilema asadzayandikire kukapereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Popeza kuti ali ndi chilema, asayandikire kudzapereka nsembe ya chakudya kwa Mulungu wake. 22 Koma iye angathe kudya chakudya chopatulika kwambiri chija, ngakhalenso chakudya chotsala pa nsembe zopatulika. 23 Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’ ”

24 Choncho Mose anawuza Aaroni ndi ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse zimenezi.

22 Yehova anawuza Mose kuti, “Uza Aaroni ndi ana ake kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraeli azipereka kwa Ine, kuti asayipitse dzina langa loyera. Ine ndine Yehova.

“Uwawuze kuti ngati wina aliyense mwa zidzukulu zawo mʼmibado yonse imene ikubwera adzayandikira zinthu zopatulika zimene ana a Israeli apereka kwa Yehova, ali wodetsedwa, ameneyo achotsedwe pamaso pa Yehova. Ine ndine Yehova.

“Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aaroni amene ali ndi khate kapena amatulutsa zoyipa mʼthupi mwake, asadye zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Wansembe angakhale wodetsedwa atakhudzana ndi chinthu chimene chadetsedwa ndi chinthu chakufa kapena kukhudza munthu amene wataya umuna, kapena kukhudza chilichonse chokwawa chomwe chimadetsa munthu, kapena kukhudza munthu amene angamudetse, kapenanso kukhudza kanthu kena kalikonse kodetsedwa. Tsono ngati wansembe angakhudze chilichonse mwa zimenezi ndiye kuti adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Asadye chopereka chilichonse chopatulika mpaka atasamba thupi lake lonse. Munthuyo adzakhala woyeretsedwa pamene dzuwa lalowa, ndipo angathe kudya chopereka chopatulikacho popeza ndi chakudya chake. Wansembe sayenera kudya chinthu chofa chokha kapena chojiwa ndi chirombo kuopa kuti angadzidetse ndi chakudyacho. Ine ndine Yehova.

“ ‘Choncho ansembe azisunga malamulo angawa kuti asapezeke wolakwa ndi kufa chifukwa chopeputsa malamulowa. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.

10 “ ‘Aliyense amene si wabanja la wansembe, kaya ndi mlendo wa wansembe, kapena wantchito wake, asadye chopereka chopatulika. 11 Koma kapolo amene wagulidwa ndi ndalama kapena kubadwira mʼbanja la wansembe angathe kudya chakudya cha wansembeyo. 12 Mwana wamkazi wa wansembe amene wakwatiwa ndi munthu amene si wansembe, asadyeko nsembe zopatulikazo. 13 Koma mwana wamkazi wa wansembe amene ali wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, komanso anabwerera ku nyumba ya abambo ake monga pa nthawi ya utsikana wake, angathe kudya chakudya cha abambo ake. Mlendo asadye chakudya chopatulika.

14 “ ‘Ngati munthu wina aliyense adya chopereka chopatulika mosadziwa, munthuyo amubwezere wansembe chinthu chopatulikacho ndipo awonjezerepo limodzi la magawo asanu a chinthucho. 15 Choncho ansembe asayipitse zopereka zopatulika za Aisraeli zimene apereka kwa Yehova 16 ndipo asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraeli powalola kudya zakudya zawo zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndimawayeretsa.’ ”

Nsembe Zosavomerezeka

17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aaroni, ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse, ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati wina aliyense wa inu, Mwisraeli kapena mlendo amene akukhala mu Israeli abwera ndi mphatso ya nsembe yopsereza kwa Yehova, kupereka chimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, 19 ndiye kuti abwere ndi ngʼombe yayimuna, nkhosa yayimuna kapena mbuzi yayimuna. Izi zikhale zopanda chilema kuti zilandiridwe. 20 Musapereke nyama iliyonse yokhala ndi chilema chifukwa sidzalandiridwa mʼmalo mwanu. 21 Pamene wina aliyense abweretsa ngʼombe kapena nkhosa kuti ikhale nsembe yachiyanjano kwa Yehova, kukwaniritsa zimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, nyamayo iyenera kukhala yangwiro ndi yopanda chilema kuti ilandiridwe. 22 Musapereke kwa Yehova nyama zakhungu, zovulala kapena zolumala, kapena nyama zimene zikutulutsa mafinya mʼthupi mwake, kapena zimene zili ndi nthenda yonyerenyetsa, kapena zimene zili ndi mphere. Nyama zotere musaziyike pa guwa kuti zikhale nsembe yopsereza kwa Yehova. 23 Koma mungathe kupereka ngʼombe yayimuna kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi kukhala nsembe yaufulu. Koma simungayipereke ngati nsembe yoperekera zimene munalumbirira chifukwa sidzalandiridwa. 24 Nyama iliyonse imene mavalo ake ndi onyuka kapena ophwanyika, ongʼambika kapena oduka, musamayipereke kwa Yehova mʼdziko lanu. 25 Ndipo musalandire nyama zotere kuchokera kwa mlendo ndi kuzipereka kukhala zakudya za Mulungu wanu. Zimenezi sizidzalandiridwa mʼmalo mwanu chifukwa zili ndi chilema ndipo ndi zolumala.’ ”

26 Yehova anawuza Mose kuti, 27 “Pamene mwana wangʼombe, mwana wankhosa kapena mwana wambuzi wabadwa, akhale ndi make kwa masiku asanu ndi awiri. Kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka mʼtsogolo mwake, angathe kulandiridwa kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 28 Musaphe ngʼombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi. Muyidye pa tsiku lomwelo; musasiyeko ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.

29 “Pamene mupereka nsembe yoyamika kwa Yehova, muyipereke mwakufuna kwanu mu njira yoti ilandiridwe mʼmalo mwanu. 30 Muyidye pa tsiku lomwelo, wosasiyako ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.

31 “Choncho sungani malamulo anga ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova. 32 Musanyoze dzina langa loyera. Koma lilemekezedwe pakati pa Aisraeli. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani 33 ndipo ndine amene ndinakutulutsani mu Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.”

Mateyu 28

Yesu Auka kwa Akufa

28 Litapita tsiku la Sabata, mmawa wa tsiku loyamba la Sabata, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anapita kukaona manda.

Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira. Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala. Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa.

Mngelo anati kwa amayiwo, “Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona. Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.”

Pamenepo amayiwo anachoka mofulumira ku mandako ali ndi mantha komabe atadzaza ndi chimwemwe, ndipo anathamanga kukawuza ophunzira ake. Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nati, “Moni.” Iwo anabwera kwa Iye, nagwira mapazi ake namulambira. 10 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Musachite mantha, pitani kawuzeni abale anga kuti apite ku Galileya ndipo kumeneko akandiona Ine.”

Uthenga wa Alonda

11 Amayi aja akupita, ena mwa alonda aja anapita ku mzinda nafotokozera akulu a ansembe zonse zimene zinachitika. 12 Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri, 13 nawawuza kuti, “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku ndipo amuba ife tili mtulo.’ 14 Ngati nkhani iyi imupeze bwanamkubwa, ife tidzamukhazika mtima pansi ndipo simudzakhala mʼmavuto.” 15 Pamenepo alondawo anatenga ndalamazo nachita monga mmene anawuzidwira. Ndipo mbiri iyi inawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.

Yesu Atuma Ophunzira Ake

16 Ndipo ophunzira khumi ndi mmodzi aja anapita ku Galileya, ku phiri limene Yesu anawawuza kuti apite. 17 Atamuona Iye, anamulambira; koma ena anakayika. 18 Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. 19 Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, 20 ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.