Old/New Testament
6 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, 3 kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, 4 ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo 5 kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. 6 Pambuyo pake apereke kwa Yehova nsembe yopalamula. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake wogwirizana ndi nsembe yopepesera machimo. 7 Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.”
Nsembe Yopsereza
8 Yehova anawuza Mose kuti, 9 “Lamula Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza ndi ili: Nsembe yopserezayo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka mmawa, ndipo moto wa paguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse. 10 Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. 11 Akatero avule zovala zakezo ndi kuvala zovala zina. Kenaka atulutse phulusalo ndi kukaliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa chithando. 12 Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo. 13 Moto uzikhala ukuyaka pa guwa nthawi zonse ndipo usazimepo.
Nsembe Zachakudya
14 “ ‘Lamulo la nsembe yachakudya ndi ili: ana a Aaroni azibwera nayo nsembeyo pamaso pa Yehova, patsogolo pa guwa. 15 Wansembe mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala wa nsembe yachakudya ija kuti ukhala ufa wachikumbutso ndi mafuta pamodzi ndi lubani yense amene ali pa nsembe ya chakudyacho, ndipo azitenthe pa guwa kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse kuti zikhale nsembe ya fungo lokomera Yehova. 16 Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano. 17 Poziphika asathire yisiti. Ndawapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lawo la nsembe zanga zopsereza. Zonsezi ndi zopatulika kwambiri monga nsembe yopepesera tchimo ndiponso nsembe yopepesera machimo. 18 Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’ ”
19 Yehova anawuzanso Mose kuti, 20 “Nsembe imene Aaroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene wansembe akudzozedwa ndi iyi: ufa wosalala kilogalamu imodzi ngati chopereka chachakudya cha nthawi zonse. Azipereka theka limodzi mmawa ndipo theka linalo madzulo. 21 Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya ndipo ubwere nayo ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi nsembe yachakudya. Iphikidwe moti itulutse fungo lokomera Yehova. 22 Mwana wa fuko la Aaroni amene adzadzozedwe kukhala wansembe kulowa mʼmalo mwa Aaroni ndiye amene azidzakonza ndi kupereka nsembeyi kwa Yehova nthawi zonse monga kunalembedwera. 23 Nsembe iliyonse yachakudya ya wansembe izitenthedwa kwathunthu, isamadyedwe.”
Nsembe Yopepesera Tchimo
24 Yehova anawuza Mose kuti 25 “Uza Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Malamulo a nsembe ya tchimo ndi awa: Nsembeyi iziphedwa pamaso pa Yehova pa malo pamene mumaphera nsembe yopsereza popeza ndi nsembe yopatulika. 26 Wansembe amene apereke nsembeyi adyere ku malo wopatulika ndiye kuti mʼbwalo la tenti ya msonkhano. 27 Chilichonse chimene chidzakhudza nsembeyo chidzakhala chopatulika, ndipo ngati magazi ake agwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo opatulika. 28 Mʼphika wadothi umene aphikira nyamayo auphwanye. Koma ngati yaphikidwa mu mʼphika wa mkuwa, awukweche ndi kuwutsukuluza ndi madzi. 29 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kuyidya popeza nsembeyi ndi yopatulika kwambiri. 30 Koma nsembe yopepesera tchimo imene magazi ake amabwera nawo mu tenti ya msonkhano kudzachita mwambo wopepesera tchimo ku malo opatulika isadyedwe, mʼmalo mwake itenthedwe.’ ”
Nsembe Yopepesera Kupalamula
7 “ ‘Malamulo a nsembe yopepesera kupalamula imene ndi nsembe yopatulika kwambiri ndi awa: 2 Nsembe yopepesera machimo iziphedwa pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza ndipo awaze magazi ake mbali zonse za guwa. 3 Tsono apereke mafuta ake onse: mchira wamafuta ndi mafuta amene amakuta matumbo. 4 Aperekenso impsyo ziwiri, mafuta ake pamodzi ndi mafuta onse amene ali chamʼchiwuno, ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi. 5 Wansembe azitenthe pa guwa kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo lopalamula. 6 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri.
7 “ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake. 8 Wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. 9 Chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni kapena chokazinga mu mʼphika kapena mu chiwaya ndi cha wansembe amene wapereka nsembezo. 10 Ndipo chopereka china chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chowuma, chikhale cha ana onse a Aaroni ndipo anawo achigawane mofanana.
Nsembe Yachiyanjano
11 “ ‘Malamulo a nsembe ya chiyanjano imene munthu angathe kupereka kwa Yehova ndi awa:
12 “ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta. 13 Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo abwerenso ndi makeke opangidwa ndi yisiti ngati chopereka chake. 14 Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano. 15 Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozera idyedwe pa tsiku lomwe nsembeyo yaperekedwa ndipo isatsaleko mpaka mmawa.
16 “ ‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake. 17 Ngati nyama ina ya nsembe yatsalabe mpaka tsiku lachitatu, imeneyo itenthedwe pa moto. 18 Ngati munthu adya nyama yachiyanjano pa tsiku lachitatu, nsembeyo sidzalandiridwa. Amene wayipereka nsembeyo Mulungu sadzamulandira ndipo nsembeyo idzakhala yonyansa pamaso pa Mulungu, yosamupindulira kanthu woperekayo.
19 “ ‘Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, munthu asayidye, koma itenthedwe pa moto. Aliyense amene ali woyeretsedwa angathe kudya nyama inayo. 20 Koma ngati munthu wina amene ndi wosayeretsedwa adya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake. 21 Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’ ”
Za Kuletsa Kudya Mafuta ndi Magazi
22 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 23 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Musadye mafuta a ngʼombe, nkhosa kapenanso mbuzi. 24 Mafuta a nyama yofa yokha, kapena mafuta a nyama yophedwa ndi zirombo akhoza kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma inu musadye mafuta amenewo. 25 Pakuti munthu wakudya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe yotentha pa moto, ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 26 Ndipo kulikonse kumene mukakhale musakadye magazi a mbalame iliyonse kapena magazi a nyama iliyonse. 27 Ngati munthu aliyense adya magazi achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.’ ”
Gawo la Ansembe
28 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 29 “Awuze Aisraeli kuti, Aliyense amene apereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Yehova. 30 Atenge ndi manja ake zigawo za chopereka zoyenera kuzitentha pa moto ngati chopereka kwa Yehova. Abweretse mafuta, pamodzi ndi chidale chomwe, ndipo chidalecho achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa Yehova. 31 Wansembe atenthe mafutawo pa guwa koma chidalecho chikhale cha Aaroni ndi ana ake. 32 Mumupatse wansembe ntchafu ya kumanja ya nsembe yanu yachiyanjano kuti ikhale chopereka chanu kwa iye. 33 Mwana wa Aaroni amene amapereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, adzitenga ntchafu ya kumanja kukhala gawo lake. 34 Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.”
35 Zimenezi ndi chigawo cha Aaroni ndi ana ake chotapidwa pa zopereka kwa Yehova zoti zitenthedwe pa moto zimene zinaperekedwa pa tsiku limene anapatulidwa kuti akhale ansembe otumikira Yehova. 36 Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse.
37 Awa ndi malamulo a nsembe izi: nsembe yopsereza, nsembe yachakudya, nsembe yopepesera machimo, nsembe yopepesera kupalamula, nsembe ya mwambo wodzoza ndi nsembe yachiyanjano. 38 Malamulo amenewa Yehova anapereka kwa Mose pa Phiri la Sinai pa tsiku limene Yehova analamulira Aisraeli kuti abwere ndi zopereka za kwa Yehova, ku chipululu cha Sinai kuja.
Fanizo la Anamwali Khumi
25 “Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. 2 Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. 3 Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; 4 koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. 5 Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.
6 “Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’
7 “Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo. 8 Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’
9 “Ochenjerawo anayankha, nati, ‘Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.’
10 “Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.
11 “Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’
12 “Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’
13 “Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi.”
Fanizo la Kagwiritsidwe Ntchito ka Ndalama
14 “Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake. 15 Wina anamupatsa ndalama 5,000, kwa wina 2,000 ndi kwa wina 1,000. Aliyense monga mwa nzeru zake. Pamenepo anapita pa ulendo wake. 16 Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja, anapita nthawi yomweyo nachita nazo malonda napindula 5,000 zina. 17 Chimodzimodzinso amene analandira 2,000 uja anapindula 2,000 zina. 18 Koma munthu amene analandira 1,000 uja, anapita nakumba dzenje nabisapo ndalama ya mbuye wake.
19 “Patapita nthawi yayitali, mbuye wa antchitowo anabwera nawayitana kuti afotokoze chimene anachita ndi ndalama zija. 20 Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, ‘Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.’
21 “Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
22 “Munthu amene anali ndi ndalama 2,000 uja anabweranso nati, ‘Ambuye munandisungitsa 2,000, onani, ndapindula 2,000 zinanso.’
23 “Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
24 “Kenaka munthu amene analandira ndalama 1,000 uja anabwera nati, ‘Ambuye ndinadziwa kuti ndinu munthu wowuma mtima, amene mumakolola pamene simunadzale ndi kututa kumene simunafese. 25 Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita ndi kukabisa ndalama yanuyo pa dzenje. Onani, si iyi ndalama yanu ija.’
26 “Mbuye wake anayankha nati, ‘Iwe wantchito woyipa ndi waulesi! Iwe umadziwa kuti ndimakolola pamene sindinadzale, ndi kututa kumene sindinafese. 27 Bwanji sunayike ndalama yanga kwa osunga ndalama kuti ine pobwera ndidzalandire ndalama yangayo pamodzi ndi chiwongoladzanja?
28 “ ‘Mulandeni ndalamayo, ndipo patsani iye amene ali ndi ndalama 10,000. 29 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, ndipo adzakhala nazo zochuluka. Aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. 30 Ndipo muponyeni wantchito wopanda phinduyu kunja, ku mdima kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.