Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 25-26

Zopereka Zomangira Chihema

25 Yehova ananena kwa Mose kuti, “Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha; mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.

“Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere.

Bokosi la Chipangano

10 “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 11 Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 12 Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 13 Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 14 Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. 15 Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe. 16 Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse.

17 “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 18 Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, 19 kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 20 Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. 21 Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. 22 Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.

Tebulo la Buledi Woperekedwa kwa Mulungu

23 “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. 24 Tebulolo ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo upange mkombero wagolide mʼmbali mwake. 25 Upange feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo uyike mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. 26 Upange mphete zinayi zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zake zinayi, kumene kuli miyendo yake inayi. 27 Mphetezo uziyike kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. 28 Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. 29 Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe. 30 Pa tebulopo uyikepo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthawi zonse.

Choyikapo Nyale

31 “Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi. 32 Mʼmbali mwake mukhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. 33 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho. 34 Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa. 35 Mphukira yoyamba ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Ndipo mphukira yachitatu ikhale mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zikhale nthambi zisanu ndi imodzi 36 Mphukira ndi nthambi zonse zisulidwe kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.

37 “Ndipo upange nyale zisanu ndi ziwiri ndi kuziyika pa choyikapo nyalecho kuti ziwunikire kutsogolo. 38 Mbaniro ndi zowolera phulusa zikhale zagolide wabwino kwambiri. 39 Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. 40 Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”

Chihema cha Mapemphero

26 “Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi. Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.

“Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi. Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri. Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri. 10 Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. 11 Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. 12 Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho. 13 Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo. 14 Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.

15 “Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. 16 Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69. 17 Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. 18 Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho. 19 Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. 20 Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri. 21 Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. 22 Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo. 23 Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. 24 Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana. 25 Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.

26 “Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, 27 mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. 28 Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. 29 Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.

30 “Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.

31 “Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi. 32 Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi. 33 Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri. 34 Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri. 35 Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.

36 “Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. 37 Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”

Mateyu 20:17-34

Yesu Anenanso za Imfa Yake

17 Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, 18 “Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, 19 ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”

Pempho la Mkazi wa Zebedayo

20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.

21 Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”

Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”

22 Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”

Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”

23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”

24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25 Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26 Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27 Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28 Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”

Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona

29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”

31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”

32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”

33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”

34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.