Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 49-50

Yakobo Adalitsa Ana ake Aamuna

49 Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.

“Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo;
    mverani abambo anu Israeli.

“Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa;
    mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga,
    wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.
Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana,
    iwe unagona pa bedi la abambo ako,
    ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.

“Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo,
    anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.
Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri,
    kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo,
pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo
    ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.
Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi
    ndi ukali wawo wankhanza choterewu!
Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo
    ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.

“Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda;
    dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako;
    abale ako adzakugwadira iwe.
Yuda ali ngati mwana wa mkango;
    umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga.
Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi,
    ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?
10 Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda,
    udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse,
mpaka mwini wake weniweni atabwera
    ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.
11 Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa,
    ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino.
Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo;
    ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.
12 Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo,
    mano ake woyera chifukwa cha mkaka.

13 “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja;
    adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi;
    malire ake adzafika ku Sidoni.

14 “Isakara ali ngati bulu wamphamvu
    wogona pansi pakati pa makola.
15 Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira
    ndi kukongola kwa dziko lake,
iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake
    ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.

16 “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake
    monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.
17 Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu,
    songo yokhala mʼnjira
imene imaluma chidendene cha kavalo
    kuti wokwerapoyo agwe chagada.

18 “Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.

19 “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo,
    koma iye adzawathamangitsa.

20 “Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma,
    ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.

21 “Nafutali ali ngati mbawala yayikazi
    yokhala ndi ana okongola kwambiri.

22 “Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso,
    mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe,
    nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.
23 Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza;
    anamuthamangitsa ndi mauta awo.
24 Koma uta wake sunagwedezeke,
    ndi manja ake amphamvu aja analimbika,
chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo,
    chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.
25 Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza;
    chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa
ndi mvula yochokera kumwamba,
    ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka,
    ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.
26 Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa
    madalitso a mapiri akale
    oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona.
Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe,
    pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.

27 “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa;
    umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha,
    ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”

28 Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.

Kumwalira kwa Yakobo

29 Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. 30 Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 31 Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya. 32 Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”

33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.

50 Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo. Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.

Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti, ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”

Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”

Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi. Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.

10 Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. 11 Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.

12 Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: 13 Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 14 Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.

Yosefe Abwereza Kutsimikizira Abale Ake

15 Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?” 16 Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati: 17 ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.

18 Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”

19 Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu? 20 Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri. 21 Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.

Kumwalira kwa Yosefe

22 Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 23 ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.

24 Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.” 25 Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”

26 Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.

Mateyu 13:31-58

Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi Yisiti

31 Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. 32 Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”

33 Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”

34 Yesu anayankhula zinthu zonsezi kwa gulu la anthu mʼmafanizo ndipo Iye sananene kalikonse kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. 35 Kotero zinakwaniritsidwa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri kuti,

“Ndidzatsekula pakamwa panga ndi mafanizo,
    ndidzawulula zinthu zobisika
    chiyambire kukhazikidwa kwa dziko lapansi.”

Yesu Awatanthauzira Fanizo la Namsongole

36 Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”

37 Iye anayankha nati, “Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu. 38 Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. 39 Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo.

40 “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. 41 Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. 42 Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano. 43 Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”

Fanizo la Chuma Chobisika ndi la Ngale

44 “Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.

45 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. 46 Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”

Fanizo la Khoka

47 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. 48 Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. 49 Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. 50 Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

51 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi mwamvetsetsa zonsezi?”

Iwo anayankha kuti, “Inde.”

52 Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”

Amupeputsa Yesu ku Nazareti

53 Yesu atatsiriza mafanizowa anachoka kumeneko. 54 Atafika ku mudzi kwawo anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo iwo anadabwa nati, “Munthu uyu anayitenga kuti nzeru iyi ndi mphamvu zodabwitsazi? 55 Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? 56 Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?” 57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye.

Koma Yesu anawawuza kuti, “Mneneri sapatsidwa ulemu ku mudzi kwawo ndi ku nyumba kwawo.”

58 Ndipo Iye sanachite zodabwitsa zambiri kumeneko chifukwa cha kusowa kwa chikhulupiriro kwawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.