Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 46-48

Yakobo Apita ku Igupto

46 Israeli anasonkhanitsa zonse anali nazo napita ku Beeriseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa abambo ake Isake.

Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!”

Iye anayankha, “Ee, Ambuye.”

Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu. Ine ndidzapita ku Igupto pamodzi ndi iwe ndipo mosakayika konse zidzukulu zako ndidzazibweretsa konkuno. Yosefe adzakhalapo pa nthawi yako yomwalira.”

Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo. Iwo anatenganso ziweto zawo ndi katundu wawo amene anali naye ku Kanaani, ndipo Yakobo pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake anapita ku Igupto. Ndiye kuti popita ku Igupto Yakobo anatenga ana aamuna, zidzukulu zazimuna, ana aakazi ndi zidzukulu zazikazi.

Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto:

Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.

Ana aamuna a Rubeni ndi awa:

Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.

10 Ana aamuna a Simeoni ndi awa:

Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani.

11 Ana aamuna a Levi ndi awa:

Geresoni, Kohati ndi Merari.

12 Ana aamuna a Yuda ndi awa:

Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani.

Ana a Perezi anali

Hezironi ndi Hamuli.

13 Ana aamuna a Isakara ndi awa:

Tola, Puwa, Yobi ndi Simironi.

14 Ana aamuna a Zebuloni ndi awa:

Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.

15 Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33.

16 Ana aamuna a Gadi ndi awa:

Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.

17 Ana aamuna a Aseri ndi awa:

Imuna, Isiva, Isivi, Beriya

ndi Sera mlongo wawo.

Ana aamuna a Beriya ndi awa:

Heberi ndi Malikieli.

18 Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16.

19 Ana aamuna a Rakele mkazi wa Yakobo anali:

Yosefe ndi Benjamini. 20 Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.

21 Ana aamuna a Benjamini ndi awa:

Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi.

22 Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa mkazi wake Rakele. Onse analipo khumi ndi anayi.

23 Mwana wa mwamuna wa Dani anali:

Husimu.

24 Ana aamuna a Nafutali ndi awa:

Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu.

25 Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Biliha amene Labani anapereka kwa mwana wake Rakele. Onse pamodzi analipo asanu ndi awiri.

26 Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66. 27 Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.

28 Tsopano Yakobo anatumiza Yuda kwa Yosefe kukamupempha kuti akakumane naye ku Goseni. Iwo atafika ku chigawo cha Goseni, 29 Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.

30 Israeli anati kwa Yosefe, “Tsopano ndikhoza kumwalira poti ndaona nkhope yako kuti ukanali ndi moyo.”

31 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, ‘Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine. 32 Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’ 33 Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34 Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”

47 Yosefe anapita kukamuwuza Farao kuti, “Abambo anga, abale anga pamodzi ndi nkhosa, ngʼombe zawo, ndi antchito awo abwera kuchokera ku dziko la Kanaani ndipo tsopano ali ku Goseni.” Iye anapita kwa Farao kuja ndi abale ake asanu, kukawaonetsa.

Farao anafunsa abale akewo kuti, “Mumagwira ntchito yanji?”

Iwo anamuyankha kuti, “Ife, bwana ndife oweta ziweto, monga ankachitira makolo athu. Ife tabwera kudzakhala kuno kwa kanthawi chifukwa njala yafika poopsa ku Kanaani motero kuti kulibe msipu wodyetsera ziweto. Ndiye bwana tiloleni kuti tikhale ku Goseni.”

Farao anati kwa Yosefe, “Abambo ako ndi abale ako abwera kwa iwe. Dziko lonse la Igupto lili mʼdzanja lako. Uwakhazike abambo ako ndi abale ako mʼmalo achonde kwambiri. Akhale ku Goseni. Ndipo ngati ukudziwapo ena mwa iwo amene ali akatswiri pa kuweta ziweto, uwapatse udindo woyangʼanira ziweto zanga.”

Kenaka Yosefe anapita ndi abambo ake kwa Farao kukawaonetsa, ndipo Yakobo anadalitsa Faraoyo. Atatero, Farao anafunsa Yakobo kuti, “Muli ndi zaka zingati?”

Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.” 10 Atatha kumudalitsa Farao uja, Yakobo anatsanzika nʼkunyamuka.

11 Choncho Yosefe anakhazika abambo ake aja ndi abale ake mʼdziko la Igupto. Iye anawapatsa dera la Ramesesi limene linali dziko lachonde kwambiri monga analamulira Farao. 12 Yosefe anaperekanso chakudya kwa abambo ake, kwa abale ake ndi kwa onse a mʼnyumba ya abambo ake monga mwa chiwerengero cha ana awo.

Yosefe pa Nthawi ya Njala

13 Njala inakula kwambiri motero kuti chakudya chinasowa mʼdziko lonse. Anthu a ku Igupto ndi ku Kanaani analefuka nayo njalayo. 14 Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a mu Igupto ndi Kanaani ankapereka pogula tirigu, ndipo anabwera nazo ku nyumba kwa Farao. 15 Anthu a ku Igupto ndi Kanaani ndalama zitawathera, Aigupto onse anabwera kwa Yosefe nati, “Tipatseni chakudya. Nanga tiferenji pamaso panu? Ndalama zathu zatha.”

16 Ndipo Yosefe anawayankha kuti, “Bwerani ndi ziweto zanu ndipo tidzasinthana ndi chakudya poti mukuti ndalama zanu zatha.” 17 Choncho anthu anabwera ndi ziweto zawo monga akavalo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi abulu ndipo Yosefe anawapatsa zakudya.

18 Chitatha chaka chimenecho, anthu anapitanso kwa Yosefe chaka chinacho nati, “Ife sitingakubisireni mbuye wathu kuti ndalama zathu zatithera ndipo ziweto zathu zili ndi inu, palibenso choti nʼkukupatsani mbuye wathu kupatula matupi athu ndi dziko lathu. 19 Tiferenji ife ndi dziko lathu inu mukuona? Mutipatse chakudya ndipo tidzigulitsa ife ndi minda yathu yomwe. Ife tidzakhala akapolo a Farao. Tipatseni mbewuzo kuti tikhale ndi moyo tisafe ndipo dziko lisachite bwinja.”

20 Choncho Yosefe anamugulira Farao dziko lonse la Igupto. Aliyense mu Igupto anagulitsa munda wake chifukwa njala inakula kwambiri. Dziko lonse linasanduka la Farao, 21 ndipo Yosefe anawasandutsa anthu onse kukhala akapolo a Farao, kuchokera ku malire a mbali ina ya Igupto kukafika ku malire a mbali ina ya dzikolo. 22 Komabe, sanagule minda ya ansembe chifukwa Farao ankawapatsa thandizo lokwanira. Nʼchifukwa chake sanagulitse minda yawo.

23 Yosefe anati kwa anthuwo, “Tsono poti ndakugulani inu ndi minda yanu, kugulira Farao. Nayi mbewu kuti mudzale mʼminda yanu. 24 Koma podzakolola, mudzapereka gawo limodzi la magawo asanu aliwonse kwa Farao. Magawo anayi enawo adzakhala anu. Zina mudzasunge mbewu ndi zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi ana anu.”

25 Iwo anati, “Mwatipulumutsa potichitira zabwinozi, mbuye wathu, tsono tidzakhala akapolo a Farao.”

26 Choncho Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero mʼdziko lonse la Igupto kuti limodzi la magawo asanu a zokolola ndi la Farao. Ndi minda ya ansembe yokha imene sinatengedwe kukhala ya Farao.

27 Tsono Aisraeli anakhazikika mʼdziko la Igupto ku chigawo cha Goseni. Kumeneko anapeza chuma ndipo anaberekana nachuluka kwambiri.

28 Yakobo anakhala ku Igupto zaka 17 ndipo zaka za moyo wake zinali 147. 29 Nthawi itayandikira yoti Israeli amwalire, anayitanitsa mwana wake Yosefe nati kwa iye, “Ngati ukundikondadi monga abambo ako, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga ndipo ulonjeze kuti udzaonetsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwako kwa ine kuti sudzayika mtembo wanga kuno ku Igupto. 30 Ine ndikagona pamodzi ndi makolo anga. Choncho ndikadzamwalira udzanditulutse mu Igupto muno ndipo ukayike mtembo wanga kumene anayikidwa makolo anga.”

Yosefe anati, “Ndidzachita monga mwanenera.”

31 Yakobo anati, “Lumbira kwa ine.” Yosefe analumbira kwa iye, ndipo Israeli anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.

Manase ndi Efereimu

48 Patapita kanthawi Yosefe anawuzidwa kuti, “Abambo ako akudwala.” Choncho anatenga ana ake awiri aja Manase ndi Efereimu ndi kupita nawo kwa Yakobo. Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.

Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa, nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’

“Tsopano ana ako aamuna awiri amene anabadwa ine ndisanabwere kuno adzakhala ana anga. Efereimu ndi Manase adzakhala anga monga mmene alili Rubeni ndi Simeoni. Koma amene ati adzabadwe pambuyo pa iwowa adzakhala ako ndipo cholowa chawo chidzadziwika ndi mayina a abale awo. Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).

Israeli ataona ana a Yosefe anafunsa kuti, “Anyamatawa ndi a yani?”

Yosefe anati kwa abambo ake, “Awa ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kuno.”

Ndipo Israeli anati, “Bwera nawo kuno kuti ndiwadalitse.”

10 Koma maso a Israeli anali ofowoka chifukwa cha kukalamba moti sankaona nʼkomwe. Tsono Yosefe anabwera nawo ana ake aja pafupi ndi abambo ake ndipo abambo ake anawapsompsona nawakumbatira.

11 Israeli anati kwa Yosefe, “Ine sindinali kuyembekeza kuti nʼkudzaonanso nkhope yako, ndipo tsopano Mulungu wandilola kuti ndionenso ngakhale ana ako.”

12 Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi. 13 Yosefe anawagwira ana onse awiri padzanja, Efereimu ku dzanja lake lamanja kulunjika dzanja lamanzere la Israeli ndipo Manase ku dzanja lamanzere kulunjikitsa dzanja lamanja la Israeli, ndipo anawayandikiza kwa Yakobo. 14 Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba.

15 Kenaka anadalitsa Yosefe nati,

“Mulungu amene makolo anga
    Abrahamu ndi Isake anamutumikira,
Mulungu amene wakhala ali mʼbusa wanga
    moyo wanga wonse kufikira lero,
16 mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse,
    ameneyo adalitse anyamata awa.
Kudzera mwa iwowa
    dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka.
Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu
    pa dziko lapansi.”

17 Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase, 18 nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”

19 Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.” 20 Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati,

“Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati:
    Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.”

Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase.

21 Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu. 22 Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.”

Mateyu 13:1-30

Fanizo la Wofesa Mbewu

13 Tsiku lomwelo Yesu anatuluka mʼnyumba ndipo anakhala mʼmbali mwa nyanja. Magulu a anthu anasonkhana mozungulira ndipo Iye analowa mʼbwato nakhala pansi ndipo anthu onse anayimirira ku mtunda. Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa. Amene ali ndi makutu amve.”

10 Ophunzira anabwera kwa Iye ndikumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani Inu mukuyankhula kwa anthu mʼmafanizo?”

11 Iye anayankha kuti, “Nzeru zakudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba zapatsidwa kwa inu koma osati kwa iwo. 12 Aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zowonjezera ndipo iye adzakhala nazo zambiri. Aliyense amene alibe, ngakhale zimene ali nazo adzamulanda. 13 Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo:

“Ngakhale akupenya koma saona,
    ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira.

14 Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:

“ ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.
    Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.
15 Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,
    mʼmakutu mwawo ndi mogontha,
    ndipo atsinzina
kuti asaone kanthu.
    Mwina angapenye ndi maso awo,
    angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,
Ineyo nʼkuwachiritsa.’

16 Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva. 17 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama anafuna kuona zimene inu mukupenya koma sanazione ndi kumva zimene inu mukumva koma sanazimve.

Tanthauzo la Fanizo la Wofesa

18 “Tamverani tsono zimene fanizo la wofesa litanthauza: 19 Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira. 20 Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe. 21 Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira. 22 Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. 23 Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”

Fanizo la Namsongole

24 Yesu anawawuza fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake. 25 Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka. 26 Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.

27 “Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’

28 “Iye anayankha kuti, ‘Ndi mdani amene anachita izi.’

“Antchito anamufunsa iye kuti, ‘Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?’

29 “Iye anakana nati, ‘Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu. 30 Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.