Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 39-40

Yosefe ndi Mkazi wa Potifara

39 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.

Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto. Mbuye wake anaona kuti Yehova anali naye Yosefe ndi kuti pa chilichonse chimene anachita Yehova ankaonetsetsa kuti achite bwino. Potifara anakondwera ndi Yosefe chifukwa cha matumikiridwe ake. Choncho anamusandutsa woyangʼanira nyumba yake ndi zonse za mʼnyumba yake. Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda. Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya.

Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola. Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!”

Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga. Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?” 10 Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi.

11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. 12 Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.

13 Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba, 14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri. 15 Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.”

16 Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. 17 Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. 18 Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.”

19 Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. 20 Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu.

Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo 21 koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe. 22 Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo. 23 Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.

Yosefe Amasulira Maloto a Amʼndende Anzake

40 Patapita nthawi, woperekera zakumwa ndi wopanga buledi a ku nyumba kwa mfumu ya ku Igupto analakwira mbuye wawoyo. Farao anapsa mtima ndi akuluakulu awiriwa, ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo. Mkulu wa alonda aja anawapereka mʼmanja mwa Yosefe, ndipo iye anawasamalira.

Iwo anakhala mʼndendemo kwa kanthawi. Usiku wina, aliyense wa anthu awiriwa, wopereka zakumwa pamodzi ndi wopanga buledi wa ku nyumba ya mfumu ya ku Igupto aja, amene ankasungidwa mʼndende, analota maloto. Malotowo anali ndi tanthauzo lake.

Mmawa wake, Yosefe atabwera, anaona kuti nkhope zawo zinali zakugwa. Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?”

Iwo anayankha, “Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo.”

Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, “Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu.”

Choncho mkulu wa operekera zakumwa uja anamuwuza Yosefe maloto ake. Anati, “Mʼmaloto anga ndinaona mtengo wa mpesa, 10 unali ndi nthambi zitatu. Mpesawo utangophukira, unachita maluwa ndipo maphava ake anabereka mphesa zakupsa. 11 Chikho cha Farao chinali mʼmanja mwanga, ndipo ndinatenga mphesa, kupsinyira mu chikho cha Farao ndi kuchipereka mʼmanja mwake.”

12 Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. 13 Pakangopita masiku atatu, Farao adzakutulutsa muno. Udzaperekera zakumwa kwa Farao monga momwe umachitira poyamba. 14 Koma zako zikakuyendera bwino, udzandikumbukire ndi kundikomera mtima. Chonde ukandipepesere kwa Farao kuti anditulutse muno. 15 Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”

16 Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi. 17 Mu nsengwa yapamwamba munali zakudya zamitundumitundu za Farao, koma mbalame zimadya zakudyazo.”

18 Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. 19 Pakangotha masiku atatu Farao adzakutulutsa muno koma adzakupachika. Ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”

20 Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. 21 Tsono Farao anamubwezera mkulu wa operekera zakumwa uja pa udindo wake, kotero kuti anayamba kuperekeranso zakumwa kwa Farao, 22 koma mkulu wa ophika buledi anamupachika, mofanana ndi mmene Yosefe anatanthauzira maloto.

23 Koma mkulu wa operekera zakumwa uja sanamukumbukire Yosefe ndipo anamuyiwaliratu.

Mateyu 11

Otumidwa ndi Yohane Mʼbatizi

11 Ndipo Yesu atamaliza kulangiza ophunzira ake khumi ndi awiri aja, anachoka kumeneko kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira ku mizinda ya ku Galileya.

Yohane ali mʼndende anamva zimene Khristu ankachita, ndipo anatumiza ophunzira ake kukamufunsa Iye. Anamufunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankanena kuti mudzabwerayu kapena tidikire wina?”

Yesu anayankha kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwamva ndi kuona. Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. Odala ndi munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

Pamene ophunzira a Yohane ankachoka, Yesu anayamba kuyankhula kwa gulu la anthu za Yohane kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kuti mukaone chiyani? Kodi bango logwedezeka ndi mphepo? Nanga munkapita kukaona chiyani, munthu wovala zokongola? Ayi, wovala zokongola amakhala mʼnyumba za mafumu. Nanga munkapita kukaona chiyani? Mneneri kodi? Inde ndikuwuzani kuti munkakaona woposa mneneri. 10 Uyu ndi amene malemba akunena za iye kuti,

“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu
    amene adzakonza njira yanu.

11 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pakati pa obadwa ndi mkazi sipanaoneke wina aliyense wamkulu woposa Yohane Mʼbatizi; komatu amene ndi wamngʼono kwambiri mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu koposa iye. 12 Kuyambira masiku a Yohane Mʼbatizi mpaka tsopano, ufumu wakumwamba ndi wolimbirana ndipo anthu amphamvu okha ndi amene akuwulanda. 13 Pakuti aneneri onse ndi malamulo ananenera kufikira nthawi ya Yohane. 14 Ndipo ngati inu mufuna kulandira izi, iyeyu ndi Eliya amene ankanena kuti adzabwera uja. 15 Iye amene ali ndi makutu amve.

16 “Kodi mʼbado uwu ndingawufanizire ndi chiyani? Uli ngati ana opezeka mʼmisika amene akuyitana anzawo nʼkumati:

17 “ ‘Tinakuyimbirani zitoliro,
    koma inu simunavine;
ife tinayimba nyimbo zamaliro,
    koma inu simunalire.’

18 Pakuti Yohane sanabwerere kudya kapena kumwa koma iwo ankanena kuti, ‘Iye anali ndi chiwanda.’ 19 Mwana wa Munthu anabwera ndi kumadya ndi kumwa koma iwo akuti, ‘Munthu wadyera, woledzera, bwenzi la amisonkho ndi bwenzi la ochimwa.’ Koma nzeru imatsimikizika kuti ndi yolondola mwa ntchito zake.”

Tsoka la Mizinda Itatu Yosatembenuka mtima

20 Pamenepo Yesu anayamba kudzudzula mizinda imene zodabwitsa zake zambiri zinachitikamo, chifukwa chakuti sinatembenuke mtima. 21 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 22 Koma ndikuwuzani inu kuti pa tsiku lachiweruzo mlandu wa Turo ndi Sidoni udzachepako kusiyana ndi wanu. 23 Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero. 24 Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu.”

Goli la Khristu

25 Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono. 26 Inde, Atate, ichi chinali chokukomerani Inu.

27 “Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.

28 “Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. 29 Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30 Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.