Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 36-38

Zidzukulu za Esau

36 Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:

Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.

Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.

Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.

Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.

10 Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau:

Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.

11 Awa ndi mayina a ana a Elifazi:

Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.

12 Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.

13 Awa ndi ana a Reueli:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.

14 Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa:

Yeusi, Yolamu ndi Kora.

15 Nawa mafumu a zidzukulu za Esau:

Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa:

Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, 16 Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.

17 Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.

18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa:

Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.

19 Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.

20 Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 21 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.

22 Ana aamuna a Lotani anali awa:

Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.

23 Ana aamuna a Sobala anali awa:

Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

24 Ana aamuna a Zibeoni anali awa:

Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.

25 Ana a Ana anali:

Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.

26 Ana aamuna a Disoni anali awa:

Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.

27 Ana aamuna a Ezeri anali awa:

Bilihani, Zaavani ndi Akani.

28 Ana aamuna a Disani anali awa:

Uzi ndi Arani.

29 Mafumu a Ahori anali awa:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 30 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.

Mafumu a ku Edomu

31 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:

32 Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.

33 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.

34 Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.

35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.

36 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.

37 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.

38 Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.

39 Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.

40 Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa:

Timna, Aliva, Yeteti, 41 Oholibama, Ela, Pinoni, 42 Kenazi, Temani, Mibezari, 43 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo.

Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.

Maloto a Yosefe

37 Yakobo ankakhala mʼdziko la Kanaani kumene abambo ake ankakhala.

Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi:

Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake.

Tsono Israeli ankakonda Yosefe koposa ana ake ena onse, chifukwa anali mwana wobadwa muukalamba wake. Ndipo anamusokera mkanjo wa manja aatali. Pamene abale ake anaona kuti abambo awo ankakonda Yosefe kuposa aliyense wa iwo, anayamba kumuda Yosefe ndipo sankayankhula naye zamtendere.

Tsiku lina Yosefe analota maloto ndipo pamene anawuza abale ake za malotowo, iwo anawonjeza kumuda. Iye anawawuza kuti, “Tamvani maloto amene ndinalota: Ife timamanga mitolo ya tirigu ku munda ndipo mwadzidzidzi mtolo wanga unayimirira chilili, pamene mitolo yanu inazungulira mtolo wangawo nʼkumawugwadira.”

Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?” Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo.

Tsiku lina analotanso maloto ena, ndipo anafotokozera abale ake za malotowo. Iye anati, “Tamverani, ndinalotanso maloto ena. Ulendo uno dzuwa ndi mwezi pamodzi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zimandigwadira.”

10 Atawuza abambo ake ndi abale ake malotowa, abambo ake anamukalipira nati, “Ndi maloto anji umalotawa? Kodi uganiza kuti ine, amayi ako pamodzi ndi abale ako onsewa tingadzabwere kudzakugwandira iwe?” 11 Abale ake anamuchitira nsanje, koma abambo ake anasunga nkhaniyi mu mtima.

Yosefe Agulitsidwa ndi Abale Ake

12 Tsono abale ake anapita kukadyetsa ziweto za abambo awo ku Sekemu, 13 ndipo Israeli anati kwa Yosefe, “Tsono, ndikufuna kukutuma kwa abale ako.”

Iye anayankha nati, “Chabwino.”

14 Choncho anati kwa iye, “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino. Ukaonenso nkhosa ngati zili bwino. Kenaka ubwere udzandiwuze.” Choncho Israeli anatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni.

Yosefe atafika ku Sekemu, 15 munthu wina anamupeza akungozungulirazungulira mʼmunda ndipo anamufunsa, “Ukufunafuna chiyani?”

16 Iye anayankha, “Ndikufuna abale anga. Mungandiwuze kumene akudyetsa ziweto zawo?”

17 Munthuyo anayankha nati, “Anasamukako kuno. Ndinawamva akuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’ ”

Choncho Yosefe analondola abale ake ndipo anakawapeza ku Dotani. 18 Abale ake aja anamuonera patali. Ndipo asanafike nʼkomwe kumene kunali iwo kuja, anayamba kale kumupangira chiwembu choti amuphe.

19 Iwo anawuzana nati, “Uyo akubwera apo wamaloto uja. 20 Tsono tiyeni timuphe ndi kuponya thupi lake mu chimodzi mwa zitsime izi ndipo tidzati anadyedwa ndi nyama zakuthengo zolusa. Tsono timuonera zomwe ziti zichitike ndi maloto ake aja.”

21 Koma Rubeni atamva izi, anapulumutsa Yosefe. Iye anati kwa abale ake, “Ayi, tisamuphe, 22 tisakhetse magazi. Tiyeni timuponye mʼchitsime ku chipululu konkuno. Koma tisamuvulaze nʼkomwe. Rubeni ananena zonsezi kuti apulumutse Yosefe ndi kuti pambuyo pake akamupereke kwa abambo awo.”

23 Choncho Yosefe atafika kwa abale ake, iwo anamuvula mkanjo wake wamanja aatali uja umene anavala 24 ndipo anamutenga namuponya mʼchitsime chopanda madzi komanso mopanda chilichonse.

25 Atakhala pansi kuti adye chakudya, anatukula maso naona gulu la Aismaeli akubwera kuchokera ku Giliyadi. Ngamira zawo zinanyamula zonunkhiritsa bwino zakudya zamitundumitundu, ndipo zimenezi ankapita nazo ku Igupto.

26 Yuda anafunsa abale ake nati, “Kodi tidzapindula chiyani tikapha mʼbale wathuyu ndi kuphimbitsa magazi ake? 27 Bwanji timugulitse kwa Aismaeliwa, koma ife tisamuchite kanthu kalikonse. Ameneyu ndi mʼbale wathu thupi limodzi ndi ife.” Abale ake anavomereza zimenezi.

28 Amalonda ena a ku Midiyani ankadutsa pomwepo. Tsono abale ake a Yosefe anamutulutsa Yosefe uja mu chitsime chija ndipo anamugulitsa kwa Aismaeli aja pamtengo wa masekeli makumi awiri. Choncho anapita naye Yosefe ku Igupto.

29 Rubeni atabwerera ku chitsime kuja anapeza kuti Yosefe mulibe mʼchitsimemo. Pamenepo iye anangʼamba zovala zake 30 nabwerera kwa abale ake nati, “Mnyamata uja mulibemo! Nanga ndilowere kuti ine tsopano?”

31 Tsono anapha kamwana ka mbuzi, natenga mkanjo wa Yosefe ndi kuwunyika mʼmagazi ake. 32 Iwo anatenga mkanjo uja nabwerera nawo kwa abambo awo nati, “Ife tapeza mkanjowu. Tawuyangʼanitsitsani muone ngati uli wa mwana wanu.”

33 Iye anawuzindikira ndipo anati, “Ndi mkanjo wa mwana wanga umenewu! Nyama yakuthengo yolusa yamudya. Mosakayika, mwana wanga Yosefe wakhadzulidwa.”

34 Pamenepo Yakobo anangʼamba zovala zake, navala chisaka mʼchiwuno mwake. Iye analira maliro a mwana wake masiku ambiri. 35 Ngakhale kuti ana ake onse aamuna ndi aakazi anasonkhana kudzamutonthoza, iye anakana kutonthozedwa. Iye anati, “Ayi. Ndidzalira mpaka ndidzapite kwa mwana wanga ku manda.” Choncho Israeli anapitirirabe kulira mwana wake.

36 Amidiyani aja anagulitsa Yosefe kwa Potifara, mmodzi mwa nduna za Farao ku Igupto. Potifarayu anali mkulu wa asilikali olonda nyumba ya Farao.

Yuda ndi Tamara

38 Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake napita kukakhala ndi munthu wina wa ku Adulamu wotchedwa Hira. Kumeneko, Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanaani wotchedwa Suwa. Anamukwatira nagona naye malo amodzi. Iye anatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna amene anamutcha Eri. Anatenganso pathupi nabala mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Onani. Anaberekanso mwana wina wamwamuna ndipo anamutcha Sela. Ameneyu anabadwa Yuda ali ku Kezibi.

Yuda anamupezera mkazi mwana wake woyamba uja Eri, ndipo dzina la mkaziyo linali Tamara. Koma ntchito zoyipa za Eri, mwana wachisamba wa Yuda zinayipira Yehova. Choncho Mulungu anamulanga ndi imfa.

Pamenepo Yuda anati kwa Onani, “Kwatira mkazi wamasiye wa mʼbale wako. Ulowe chokolo kuti mʼbale wako akhale ndi mwana.” Koma Onani anadziwa kuti mwanayo sadzakhala wake. Choncho nthawi zonse pamene amagona naye mkaziyo, ankatayira umuna pansi kuti asamuberekere mwana mʼbale wake. 10 Zimene ankachitazi zinayipira Yehova. Choncho anamulanganso ndi imfa.

11 Kenaka Yuda anati kwa mpongozi wake Tamara, “Bwererani ku nyumba ya abambo anu ndi kukhala kumeneko ngati wamasiye mpaka mwana wanga Sela atakula.” Ananena izi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso ngati abale ake aja. Choncho Tamara anapita kukakhala ku nyumba ya abambo ake.

12 Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo.

13 Tamara atamva kuti apongozi ake akupita ku Timna kukameta nkhosa, 14 iye anavula zovala zake za umasiye, nadziphimba nkhope ndi nsalu kuti asadziwike, ndipo anakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu popita ku Timna. Tamara anachita izi chifukwa anaona kuti ngakhale Selayo anali atakula tsopano, iye sanaperekedwe kuti amulowe chokolo.

15 Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope. 16 Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake.

Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?”

17 Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.”

Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?”

18 Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?”

Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi. 19 Kenaka Tamara anachoka, navula nsalu anadziphimba nayo ija, navalanso zovala zake za umasiye zija.

20 Tsono Yuda anatuma bwenzi lake Mwadulamu uja ndi kamwana kambuzi kaja kuti akapereke kwa mkazi wadama uja, ndi kuti akatero amubwezere chikole chake chija. Koma atafika sanamupezepo. 21 Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?”

Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.”

22 Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ”

23 Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.”

24 Patapita miyezi itatu, Yuda anawuzidwa kuti, “Mpongozi wanu Tamara anachita zadama, ndipo zotsatira zake nʼzakuti ali ndi pathupi.”

Yuda anati, “Kamutulutseni ndipo mukamutenthe kuti afe!”

25 Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?”

26 Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso.

27 Pamene Tamara nthawi inamukwanira yoti abeleke, mʼmimbamo munali mapasa. 28 Pamene ankabereka, mmodzi wa iwo anatulutsa dzanja lake. Choncho mzamba anatenga kawulusi kofiira nakamangirira pa mkono pa mwanayo nati, “Uyu ndiye anayamba kubadwa.” 29 Koma pamene anabweza mkonowo, mʼbale wake anabadwa ndipo mzamba anati, “Wachita kudziphotcholera wekha njira chonchi!” Ndipo anamutcha Perezi. 30 Pambuyo pake mʼbale wake amene anali ndi ulusi wofiira pa mkono wake uja anabadwa ndipo anapatsidwa dzina lakuti Zera.

Mateyu 10:21-42

21 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23 Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.

24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake. 25 Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!

26 “Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika. 27 Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga. 28 Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena. 29 Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. 30 Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. 31 Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.

32 “Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. 33 Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.

34 “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. 35 Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa

“ ‘Munthu ndi abambo ake,
    mwana wamkazi ndi amayi ake,
mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake,
36     adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’

37 “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. 38 Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. 39 Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.

40 “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41 Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42 Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.