Old/New Testament
Abrahamu ndi Mfumu Abimeleki
20 Abrahamu anachokako kumeneko napita ku Negevi ndipo anakakhala ku dziko la Gerari, limene lili pakati pa mzinda wa Kadesi ndi mzinda wa Suri. Anakhala ku Gerari kwa kanthawi, 2 ndipo Abrahamu ankawawuza za Sara kuti, “Iyeyu ndi mlongo wanga.” Choncho Abimeleki, mfumu wa ku Gerari anamutenga Sara uja.
3 Koma usiku, Mulungu anafika kwa Abimeleki kutulo nati, “Ufatu iwe chifukwa cha mkazi amene watengayu popeza ndi wokwatiwa.”
4 Nthawi imeneyi nʼkuti Abimeleki asanamukhudze mkaziyo, kotero kuti anati, “Ambuye, kodi mudzawonongadi mtundu wolungama? 5 Kodi Abrahamu sanandiwuze kuti iyeyu ndi mlongo wake? Ndiponso mkaziyu ankanena kuti Abrahamu ndi mlongo wake. Choncho ine pochita izi, ndinkachita moona mtima ndiponso mopanda chinyengo.”
6 Tsono kumaloto komweko Mulungu anati kwa iye, “Inde ndikudziwa kuti wachita izi moona mtima, ndipo Ine sindinafune kuti undichimwire. Nʼchifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze. 7 Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.”
8 Mmamawa mwake Abimeleki anayitanitsa akuluakulu ake onse, ndipo atawafotokozera zimene zinachitika, iwo aja anachita mantha kwambiri. 9 Kenaka Abimeleki anayitana Abrahamu ndipo anati, “Kodi wachita chiyani? Ndakulakwira chiyani kuti undibweretsere ine pamodzi ndi anthu anga chilango chachikulu chotere? Wandichitira zinthu zimene sizinayenera kuchitika.” 10 Ndipo Abrahamu anafunsa Abimeleki kuti, “Chifukwa chiyani wachita zimenezi?”
11 Abrahamu anayankha nati, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibiretu munthu woopa Mulungu. Ndiye ndimati mwina adzandipha chifukwa cha mkazi wanga. 12 Komabe kunena zoona, iyeyu ndi mlongo wangadi, mwana wamkazi wa abambo anga ngakhale kuti si ife a mayi mmodzi. Tsono akhoza kukhala mkazi wanga. 13 Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, ‘Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’ ”
14 Tsono Abimeleki anapereka nkhosa, ngʼombe ndi antchito aamuna ndi aakazi kwa Abrahamu. Ndipo anamubwezeranso Abrahamu Sara, mkazi wake. 15 Tsono Abimeleki anati kwa Abrahamu, “Dziko langa ndi limene ukulionali; ukhale paliponse pamene ufuna.”
16 Ndipo kwa Sara, iye anati, “Ndikumupatsa mlongo wakoyu makilogalamu khumi ndi awiri a siliva kutsimikiza kuti iwe ndi wosalakwa pamaso pa onse amene ali ndi iwe; ulibedi mlandu.”
17 Tsono Abrahamu anapemphera kwa Mulungu ndipo Mulunguyo anachiritsa Abimeleki, mkazi wake pamodzi ndi adzakazi ake kuti athenso kubereka ana. 18 Paja Yehova nʼkuti atatseka akazi onse a mʼbanja la Abimeleki kuti asabereke ana chifukwa cha Sara, mkazi wa Abrahamu.
Kubadwa kwa Isake
21 Yehova anakomera mtima Sara monga ananenera, ndipo Yehovayo anachita monga momwe analonjezera. 2 Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza. 3 Abrahamu anapereka dzina loti Isake kwa mwana wamwamuna amene Sara anamuberekera. 4 Isake atakwanitsa masiku asanu ndi atatu, Abrahamu anamuchita mdulidwe monga Mulungu anamulamulira. 5 Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa.
6 Sara anati, “Mulungu wandibweretsera mseko, ndipo aliyense amene adzamva zimenezi adzaseka nane pamodzi.” 7 Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.”
Kuchotsedwa kwa Hagara ndi Ismaeli
8 Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu. 9 Koma Sara anaona kuti mwana wamwamuna amene Hagara Mwigupto anamuberekera Abrahamu amamuseka, 10 ndipo anati kwa Abrahamu, “Muchotse mdzakazi ndi mwana wake wamwamunayu, pakuti mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wanga Isake.”
11 Nkhaniyi inamumvetsa chisoni kwambiri Abrahamu chifukwa imakhudza mwana wake. 12 Koma Mulungu anamuwuza Abrahamu kuti, “Usamve chisoni motero ndi mnyamatayu ndi mdzakazi wakoyu. Mvetsera chilichonse chomwe Sara akukuwuza, chifukwa zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 13 Mwana wa mdzakazi wakoyu ndidzamusandutsa mtundu wa anthu chifukwa ndi mwana wako.”
14 Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba.
15 Madzi atatha mʼbotolo muja, anamuyika mnyamatayo pansi pa zitsamba. 16 Kenaka Hagara anachoka nakakhala pansi cha pakatalipo, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi, popeza mʼmaganizo mwake amati, “Sindingaonerere mwanayu akufa.” Ndipo anakhala pansi cha poteropo nʼkumalira.
17 Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo. 18 Munyamule mnyamatayo ndipo umugwire dzanja pakuti ndidzamupanga kukhala mtundu waukulu.”
19 Kenaka Mulungu anatsekula maso a Hagara ndipo anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita nadzaza botolo lija ndi madzi ndi kumupatsa mnyamatayo kuti amwe.
20 Mulungu anali ndi mnyamatayo pamene ankakula. Anakhala ku chipululu nakhala katswiri wolasa uta. 21 Akukhala ku chipululu cha Parani, mayi ake anamupezera mkazi wochokera ku Igupto.
Pangano la ku Beeriseba
22 Pa nthawiyo, Abimeleki ndi Fikolo wamkulu wankhondo wake anati kwa Abrahamu, “Mulungu ali nawe pa chilichonse umachita. 23 Tsopano undilumbirire ine pano pamaso pa Mulungu kuti sudzachita mwa chinyengo ndi ine kapena ana anga kapena zidzukulu zanga. Undionetse ine pamodzi ndi dziko limene ukukhalamo ngati mlendo, kukoma mtima kokhala ngati kumene ndinakuonetsa ine.”
24 Abrahamu anati, “Ine ndikulumbira.”
25 Kenaka Abrahamu anadandaula kwa Abimeleki pa za chitsime chimene antchito a Abimeleki analanda. 26 Koma Abimeleki anati, “Ine sindikudziwa amene anachita zimenezi. Iwe sunandiwuze, ndipo ndazimva lero zimenezi.”
27 Choncho Abrahamu anabweretsa nkhosa ndi ngʼombe nazipereka kwa Abimeleki, ndipo anthu awiriwo anachita pangano. 28 Abrahamu anapatulako ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri kuchoka pagulu la nkhosa zina, 29 ndipo Abimeleki anafunsa Abrahamu, “Kodi tanthauzo lake la ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri amene wawapatula pawokhawa nʼchiyani?”
30 Iye anayankha kuti, “Landirani ana ankhosa aakazi kuchokera mʼdzanja langa ngati umboni kuti ndinakumba chitsime ichi.”
31 Kotero malo amenewo anatchedwa Beeriseba, chifukwa anthu awiriwo analumbirirapo malumbiro.
32 Atatha kuchita pangano pa Beeriseba, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wankhondo wake anabwerera ku dziko la Afilisti. 33 Abrahamu anadzala mtengo wa bwemba ku Beeriseba, ndipo anapemphera pamenepo mʼdzina la Yehova, Mulungu Wamuyaya. 34 Ndipo Abrahamu anakhala mʼdziko la Afilisti kwa nthawi yayitali.
Kuyesedwa kwa Abrahamu
22 Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!”
Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
2 Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.”
3 Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu. 4 Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. 5 Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.”
6 Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, 7 Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?”
Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.”
Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?”
8 Abrahamu anayankha, “Mwana wanga, Mulungu adzipezera yekha mwana wankhosa wa nsembe yopsereza.” Ndipo awiriwo anapitiriza ulendo.
9 Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja. 10 Kenaka Abrahamu anatambasula dzanja lake natenga mpeni kuti aphe mwana wake. 11 Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!”
Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
12 Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
13 Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. 14 Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.”
15 Mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba kachiwiri 16 ndipo anati, “Ndikulumbira mwa Ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi, wosandikaniza mwana wako mmodzi yekhayu, 17 ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo, 18 ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi idzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.”
19 Kenaka Abrahamu anabwerera kumene anasiya antchito ake kuja nanyamukira nawo pamodzi kupita ku Beeriseba. Ndipo Abrahamu anakhala ku Beeriseba.
Ana Aamuna a Nahori
20 Patapita nthawi, Abrahamu anamva kuti, “Milika nayenso anaberekera Nahori, mʼbale wake ana. 21 Woyamba anali Huzi ndipo kenaka mʼbale wake Buzi. Anaberekanso Kemueli, amene anali abambo ake a Aramu. 22 Ana ena ndi Kesede Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betueli.” 23 Betueli anabereka Rebeka. Milika anaberekera Nahori, mʼbale wake wa Abrahamu, ana aamuna asanu ndi atatu amenewa. 24 Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.
Za Chuma cha Kumwamba
19 “Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20 Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.
Diso Nyale ya Thupi
22 “Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala. 23 Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji!
24 “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.
Musade Nkhawa
25 “Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? 26 Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? 27 Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?
28 “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. 29 Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa. 30 Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa! 31 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ 32 Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. 33 Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu. 34 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.