Old/New Testament
Mndandanda wa Mitundu ya Anthu
10 Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
Banja la Yafeti
2 Ana aamuna a Yafeti anali:
Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
3 Ana aamuna a Gomeri anali:
Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
4 Ana aamuna a Yavani anali:
Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. 5 (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
Banja la Hamu
6 Ana aamuna a Hamu anali:
Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
7 Ana aamuna a Kusi anali:
Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka.
Ana aamuna a Raama anali:
Seba ndi Dedani.
8 Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi. 9 Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.” 10 Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. 11 Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala, 12 ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
13 Igupto ndiye kholo la
Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 14 Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
15 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,
Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; 16 Ayebusi, Aamori, Agirigasi; 17 Ahivi, Aariki, Asini, 18 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse, 19 mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20 Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
Banja la Semu
21 Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
22 Ana aamuna a Semu anali:
Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
23 Ana aamuna a Aramu anali:
Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
24 Aripakisadi anabereka Sela,
ndipo Selayo anabereka Eberi.
25 A Eberi anabereka ana aamuna awiri:
Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
26 Yokitani anabereka
Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 27 Hadoramu, Uzali, Dikila, 28 Obali, Abimaeli, Seba, 29 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
30 Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
32 Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.
Nsanja ya Babeli
11 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi. 2 Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
3 Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. 4 Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
5 Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. 6 Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. 7 Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”
8 Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. 9 Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
Mibado Kuyambira pa Semu Mpaka Abramu
10 Nayi mibado yochokera kwa Semu.
Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
12 Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. 13 Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
14 Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. 15 Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
16 Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. 17 Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
18 Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
20 Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21 Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
22 Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
24 Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. 25 Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
26 Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
Mibado Yochokera mwa Tera
27 Nayi mibado yochokera mwa Tera.
Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. 28 Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. 29 Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. 30 Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
31 Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
32 Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.
Mulungu Ayitana Abramu
12 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.
2 “Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu
ndipo ndidzakudalitsa;
ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti
udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
3 Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,
ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;
ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi
adzadalitsika kudzera mwa iwe.”
4 Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. 5 Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.
6 Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo. 7 Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.
8 Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. 9 Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi.
Abramu ku Igupto
10 Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri. 11 Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri. 12 Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. 13 Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.”
14 Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. 15 Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao. 16 Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.
17 Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. 18 Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? 19 Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20 Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.
Yesu Ayesedwa Mʼchipululu
4 Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. 2 Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala. 3 Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”
5 Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. 6 Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa:
“ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe,
ndipo adzakunyamula ndi manja awo
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”
7 Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”
8 Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. 9 Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”
10 Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
11 Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.
Yesu Ayamba Kulalikira
12 Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya. 13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali; 14 pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
15 “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,
njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani,
Galileya wa anthu a mitundu ina,
16 anthu okhala mu mdima
awona kuwala kwakukulu;
ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa
kuwunika kwawafikira.”
17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi. 19 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.
Yesu Achiritsa Odwala
23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu. 24 Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa. 25 Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.