Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Hagai 1-2

Za Kumanga Nyumba ya Yehova

Chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Yehova anapatsa mneneri Hagai uthenga wopita kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, ndiponso kwa mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki:

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu awa amanena kuti, ‘Nthawi sinafike yoti nʼkumanga Nyumba ya Yehova.’ ”

Tsono Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti, “Kodi ino ndi nthawi yoti inuyo muzikhala mʼnyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ikanali bwinja?”

Tsono zimene Yehova Wamphamvuzonse akunena ndi izi, “Ganizirani bwino njira zanu. Mwadzala zambiri, koma mwakolola zochepa. Mumadya, koma simukhuta. Mumamwa, koma ludzu lanu silitha. Mumavala, koma simumva kutentha. Mumalandira malipiro, koma ndalama zanu zimatha ngati mwaziyika mʼthumba lobowoka.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ganizirani bwino njira zanu. Pitani ku mapiri ndipo mukatenge matabwa oti mudzamangire Nyumba yanga, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiramo ulemu,” akutero Yehova. “Mumayembekezera zambiri, koma taonani mwapeza pangʼono pokha. Zimene munazibweretsa ku nyumba, Ine ndinazimwaza. Nʼchifukwa chiyani?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Chifukwa Nyumba yanga ikanali bwinja, pamene aliyense wa inu watanganidwa kumanga nyumba yake. 10 Choncho, chifukwa cha inu, mitambo yaleka kugwetsa mvula ndipo dziko lapansi laleka kutulutsa zomera. 11 Ndabweretsa chilala pa minda ndi pa mapiri, chilala chawumitsa tirigu, mphesa, mafuta a olivi ndi chilichonse chimene chimamera pa nthaka, pa anthu ndi pa ngʼombe, ndi pa ntchito zonse za manja anu.”

12 Pamenepo Zerubabeli mwana wa Sealatieli, mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndi anthu onse otsala anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi uthenga wa Hagai, chifukwa anatumidwa ndi Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthuwo anaopa Yehova.

13 Tsono Hagai, mthenga wa Yehova, anapereka kwa anthuwo uthenga uwu wa Yehova: “Ine ndili nanu,” akutero Yehova. 14 Kotero Yehova anakhudza mtima wa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, mtima wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso mitima ya anthu onse otsala. Iwo anabwera ndi kuyamba ntchito yomanga Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wawo, 15 pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo.

Ulemerero wa Nyumba Yatsopano ya Yehova

Pa tsiku la 21 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Yehova anayankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti: “Yankhula kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa anthu onse otsala. Afunse kuti, ‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu? Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Izi ndi zimene ndinapangana nanu pamene munkatuluka ku Igupto. Ndipo Mzimu wanga uli pakati panu. Musachite mantha.’

“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakapita nthawi pangʼono ndidzagwedezanso thambo ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda. Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ulemerero wa nyumba iyi udzaposa ulemerero wa nyumba yoyamba ija,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo pamalo pano ndidzakhazikitsapo mtendere,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Madalitso kwa Anthu Oyipitsidwa

10 Chaka chachiwiri cha Dariyo, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti: 11 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Funsa ansembe za zimene lamulo likunena: 12 Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’ ”

Ansembe anayankha kuti, “Ayi.”

13 Pamenepo Hagai anati, “Ngati munthu amene anayipitsidwa pokhudza mtembo akhudza chimodzi cha zinthu zimenezi, kodi chinthucho chimayipitsidwa?”

Ansembe anayankha kuti, “Inde, chimayipitsidwa.”

14 Pamenepo Hagai anati, “ ‘Ndi mmene zilili ndi anthu awa ndi dziko ili pamaso panga,’ akutero Yehova. ‘Chilichonse amachita ndiponso chilichonse chimene amapereka nʼchodetsedwa.

15 “ ‘Tsopano muganizire zimenezi kuyambira lero mpaka mʼtsogolo. Ganizirani momwe zinthu zinalili asanayambe kumanga nyumba ya Yehova. 16 Pamene munthu ankayembekezera miyeso ya tirigu makumi awiri ankangopeza khumi yokha. Munthu akapita kuti akatunge miyeso makumi asanu ya vinyo mu mtsuko, ankangopeza miyeso makumi awiri yokha. 17 Ndinawononga ntchito yonse ya manja anu ndi chinsikwi, chiwawu ndi matalala, komabe inu simunatembenukire kwa Ine,’ akutero Yehova 18 ‘Kuyambira lero tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi mpaka mʼtsogolo, chonde ganizirani bwino tsiku limene munayika maziko a nyumba ya Yehova. Ganizirani bwino. 19 Kodi mʼnkhokwe mwatsala mbewu? Mpaka lero, mpesa ndi mtengo wa mkuyu, makangadza ndi mtengo wa olivi sizinabereke zipatso.

“ ‘Kuyambira lero mpaka mʼtsogolo ndidzakudalitsani.’ ”

Zerubabeli Mphete Yolamulira ya Yehova

20 Yehova anayankhula ndi Hagai kachiwiri, pa tsiku la 24 la mwezi kuti: 21 “Uza Zerubabeli, bwanamkubwa wa Yuda, kuti ndidzagwedeza thambo ndi dziko lapansi. 22 Ndidzagwetsa mipando yaufumu ndi kuwononga mphamvu za maufumu achilendo. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake; akavalo ndi okwerapo ake adzagwa, aliyense adzaphedwa ndi lupanga la mʼbale wake.

23 “ ‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Chivumbulutso 17

Mkazi Wachiwerewere

17 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”

Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa:

BABULONI WAMKULU

MAYI WA AKAZI ADAMA

NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.

Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu.

Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri. Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.

“Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri. 10 Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa. 11 Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.

12 “Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi. 13 Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho. 14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”

15 Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo. 16 Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto. 17 Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. 18 Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.