Old/New Testament
Mlandu wa Yehova ndi Israeli
6 Tamverani zimene Yehova akunena:
“Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri;
zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.
2 Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri;
tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi.
Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake;
Iye akutsutsa Aisraeli.
3 “Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani?
Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.
4 Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto
ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo.
Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni,
pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
5 Anthu anga, kumbukirani
zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani
ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha.
Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala,
kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”
6 Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova
ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba?
Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza,
ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?
7 Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000,
kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta?
Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga?
Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
8 Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino.
Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe?
Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo
ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Kulakwa kwa Israeli ndi Chilango chake
9 Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda
ndi nzeru kuopa dzina lanu.
“Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa.
10 Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala
chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo,
ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?
11 Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo,
ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake?
12 Anthu ake olemera amachita zachiwawa;
anthu ake ndi abodza
ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.
13 Choncho, ndayamba kukuwonongani,
kukusakazani chifukwa cha machimo anu.
14 Mudzadya, koma simudzakhuta;
mudzakhalabe ndi njala.
Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika,
chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga.
15 Mudzadzala, koma simudzakolola.
Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito.
Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.
16 Inu mwatsatira malangizo a Omuri
ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu,
ndi khalidwe lawo lonse.
Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe
ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu;
mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”
Chipsinjo cha Israeli
7 Tsoka ine!
Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe,
pa nthawi yokolola mphesa;
palibe phava lamphesa loti nʼkudya,
palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.
2 Anthu opembedza atha mʼdziko;
palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala.
Anthu onse akubisalirana kuti aphane;
aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka.
3 Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa;
wolamulira amafuna mphatso,
woweruza amalandira ziphuphu,
anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna,
onse amagwirizana zochita.
4 Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga,
munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga.
Tsiku limene alonda ako ananena lafika,
tsiku limene Mulungu akukuchezera.
Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo.
5 Usadalire mnansi;
usakhulupirire bwenzi.
Usamale zoyankhula zako
ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.
6 Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake,
mwana wamkazi akuwukira amayi ake,
mtengwa akukangana ndi apongozi ake,
adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.
7 Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo,
ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga;
Mulungu wanga adzamvetsera.
Kuuka kwa Israeli
8 Iwe mdani wanga, usandiseke!
Ngakhale ndagwa, ndidzauka.
Ngakhale ndikukhala mu mdima,
Yehova ndiye kuwunika kwanga.
9 Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova,
chifukwa ndinamuchimwira,
mpaka ataweruza mlandu wanga
ndi kukhazikitsa chilungamo changa.
Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika;
ndidzaona chilungamo chake.
10 Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi
nadzagwidwa ndi manyazi,
iye amene anandifunsa kuti,
“Ali kuti Yehova Mulungu wako?”
Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga;
ngakhale tsopano adzaponderezedwa
ngati matope mʼmisewu.
11 Idzafika nthawi yomanganso makoma anu,
nthawi yokulitsanso malire anu.
12 Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu
kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto,
ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate
ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso
kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
13 Dziko lapansi lidzasanduka chipululu
chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.
Pemphero ndi Matamando
14 Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza,
nkhosa zimene ndi cholowa chanu,
zimene zili zokha mʼnkhalango,
mʼdziko la chonde.
Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi
monga masiku akale.
15 “Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga,
ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.”
16 Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi,
ngakhale ali ndi mphamvu zotani.
Adzagwira pakamwa pawo
ndipo makutu awo adzagontha.
17 Adzabwira fumbi ngati njoka,
ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi.
Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo;
mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu
ndipo adzachita nanu mantha.
18 Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
19 Inu mudzatichitiranso chifundo;
mudzapondereza pansi machimo athu
ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
20 Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo,
ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu,
monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu
masiku amakedzana.
Chirombo Chotuluka Mʼnyanja
13 Ndipo ndinaona chirombo chikutuluka mʼnyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri. Pa nyanga iliyonse chinavala chipewa chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu. 2 Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu. 3 Umodzi wa mitu wa chirombocho unkaoneka ngati uli ndi bala losati nʼkupola, koma nʼkuti balalo litapola. Dziko lonse linadabwa ndipo linatsatira chirombocho. 4 Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
5 Chirombo chija chinaloledwa kuyankhula mawu onyada ndi achipongwe kwa Mulungu. Chinapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. 6 Ndipo chinayamba kuyankhula mawu achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo okhalamo ndi onse amene amakhala kumwamba. 7 Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse. 8 Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja.
9 Iye amene ali ndi makutu, amve.
10 “Woyenera kupita ku ukapolo,
adzapita ku ukapolo.
Woyenera kufa ndi lupanga,
adzafa ndi lupanga.”
Pamenepa kwa anthu a Mulungu pakufunika kupirira ndi kukhulupirika.
Chirombo Chotuluka Mʼnthaka
11 Kenaka ndinaona chirombo china chikutuluka mʼnthaka. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wankhosa koma kuyankhula kwake ngati chinjoka. 12 Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola. 13 Ndipo chinachita zizindikiro zazikulu zodabwitsa, mpaka kumagwetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba anthu akuona. 14 Chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita mʼmalo mwa chirombo choyamba chija, chimene bala lake linapola, chinanyenga anthu okhala pa dziko lapansi. Chinalamula anthu kuti apange fano mopereka ulemu kwa chirombo chimene chinavulazidwa ndi lupanga, koma nʼkukhalabe ndi moyo. 15 Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo. 16 Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. 17 Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake.
18 Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.