Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mika 1-3

Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.

Tamverani, inu anthu a mitundu yonse,
    mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo,
pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani,
    Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.

Chiweruzo cha Samariya ndi Yerusalemu

Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake;
    Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.
Mapiri akusungunuka pansi pake,
    ndipo zigwa zikugawikana
ngati phula pa moto,
    ngati madzi ochokera mʼphiri.
Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo,
    chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli.
Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani?
    Kodi si Samariya?
Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati?
    Kodi si Yerusalemu?

“Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja,
    malo odzalamo mphesa.
Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa
    ndipo ndidzafukula maziko ake.
Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya;
    mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto;
    ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake.
Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere,
    mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”

Kulira ndi Kumva Chisoni

Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni;
    ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche.
Ndidzafuwula ngati nkhandwe
    ndi kulira ngati kadzidzi.
Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika;
    chafika ku Yuda.
Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga,
    mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.
10 Musanene zimenezi ku Gati;
    musalire nʼkomwe.
Mugubuduzike mu fumbi
    ku Beti-Leafura.
11 Inu anthu okhala ku Safiro,
    muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi.
Iwo amene akukhala ku Zanaani
    sadzatuluka.
Beti-Ezeli akulira mwachisoni;
    chitetezo chake chakuchokerani.
12 Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu,
    akuyembekezera thandizo,
chifukwa Yehova wabweretsa tsoka,
    lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
13 Inu anthu okhala ku Lakisi
    mangani akavalo ku magaleta.
Inu amene munayamba kuchimwitsa
    mwana wamkazi wa Ziyoni,
pakuti zolakwa za Israeli
    zinapezeka pakati panu.
14 Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana
    ndi a ku Moreseti Gati.
Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama
    kwa mafumu a Israeli.
15 Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu
    okhala mu Maresa.
Ulemerero wa Israeli udzafika
    ku Adulamu.
16 Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira
    ana anu amene mumawakonda;
mudzichititse dazi ngati dembo,
    pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.

Zokonzekera za Munthu ndi Zokonzekera za Mulungu

Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu,
    kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo!
Kukacha mmawa amakachitadi
    chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.
Amasirira minda ndi kuyilanda,
    amasirira nyumba ndi kuzilanda.
Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo,
    munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.

Nʼchifukwa chake Yehova akuti,

“Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa,
    tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha.
Inu simudzayendanso monyada,
    pakuti idzakhala nthawi ya masautso.
Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe;
    adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro:
‘Tawonongeka kotheratu;
    dziko la anthu anga lagawidwa.
Iye wandilanda!
    Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”

Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova
    kuti agawe dziko pochita maere.

Aneneri Onyenga

Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere!
    Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi;
    ife sitidzachititsidwa manyazi.”
Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena:
    “Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya?
    Kodi Iye amachita zinthu zotere?”

“Kodi mawu ake sabweretsa zabwino
    kwa amene amayenda molungama?
Posachedwapa anthu anga andiwukira
    ngati mdani.
Mumawavula mkanjo wamtengowapatali
    anthu amene amadutsa mosaopa kanthu,
    monga anthu amene akubwera ku nkhondo.
Mumatulutsa akazi a anthu anga
    mʼnyumba zawo zabwino.
Mumalanda ana awo madalitso anga
    kosatha.
10 Nyamukani, chokani!
    Pakuti ano si malo anu opumulirapo,
chifukwa ayipitsidwa,
    awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso.
11 Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti,
    ‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri,
    woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’

Alonjeza Chipulumutso

12 “Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse;
    ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli.
Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola,
    ngati ziweto pa msipu wake;
    malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.
13 Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo;
    iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka.
Mfumu yawo idzawatsogolera,
    Yehova adzakhala patsogolo pawo.”

Atsogoleri ndi Aneneri Adzudzulidwa

Ndipo ine ndinati,

“Tamverani, inu atsogoleri a Yakobo,
    inu olamulira nyumba ya Israeli.
Kodi sindinu oyenera kudziwa kuweruza molungama,
    inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa;
inu amene mumasenda khungu la anthu anga,
    ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo;
inu amene mumadya anthu anga,
    mumasenda khungu lawo
    ndi kuphwanya mafupa awo;
inu amene mumawadula nthulinthuli
    ngati nyama yokaphika?”

Pamenepo adzalira kwa Yehova,
    koma Iye sadzawayankha.
Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake
    chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.

Yehova akuti,

“Aneneri amene
    amasocheretsa anthu anga,
ngati munthu wina awapatsa chakudya
    amamufunira ‘mtendere;’
ngati munthu wina sawapatsa zakudya
    amamulosera zoyipa.
Nʼchifukwa chake kudzakuderani,
    simudzaonanso masomphenya,
mdima udzakugwerani ndipo simudzawombezanso.
    Dzuwa lidzawalowera aneneriwo, ndipo mdima udzawagwera.
Alosi adzachita manyazi
    ndipo owombeza mawula adzanyazitsidwa.
Onse adzaphimba nkhope zawo
    chifukwa Mulungu sakuwayankha.”

Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu,
    ndi Mzimu wa Yehova,
    ndi kulungama, ndi kulimba mtima,
kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo,
    kwa Israeli za tchimo lake.
Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo,
    inu olamulira nyumba ya Israeli,
inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama;
    ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola;
10 inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi,
    ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu.
11 Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze,
    ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire,
    ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama.
Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti,
    “Kodi Yehova sali pakati pathu?
    Palibe tsoka limene lidzatigwere.”
12 Choncho chifukwa cha inu,
    Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
    ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.

Chivumbulutso 11

Mboni Ziwiri

11 Ndinapatsidwa bango longa ndodo yoyezera ndipo ndinawuzidwa kuti, “Pita, kayeze Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukawerenge anthu opembedza mʼNyumbamo. Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42. Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.” Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi. Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo. Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune.

Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako. Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira. 10 Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi.

11 Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu. 12 Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona.

13 Nthawi yomweyo panachitika chivomerezi choopsa mwakuti chigawo chimodzi cha magawo khumi a mzinda chinagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho, ndipo opulumukawo anachita mantha kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wakumwamba.

14 Tsoka lachiwiri lapita; koma tsoka lachitatu likubwera posachedwapa.

Lipenga Lachisanu ndi Chiwiri

15 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati,

“Ufumu wa dziko lapansi uli
    mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja,
    ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

16 Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu 17 Iwo anati,

“Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
    amene mulipo ndipo munalipo,
chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu,
    ndipo mwayamba kulamulira.
18 A mitundu ina anapsa mtima;
    koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo.
Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa,
    yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri,
anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu,
    wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe.
Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”

19 Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.