Old/New Testament
Chiweruzo cha Israeli
5 “Ansembe inu, imvani izi!
Inu Aisraeli, tcherani khutu!
Inu nyumba yaufumu, mvetserani!
Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu:
Inu munali ngati msampha ku Mizipa,
munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
2 Owukira azama mʼmoyo wakupha,
Ine ndidzawalanga onsewo.
3 Ndimadziwa zonse za Efereimu;
Aisraeli ndi osabisika kwa Ine.
Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere;
Israeli wadziyipitsa.
4 “Ntchito zawo siziwalola
kubwerera kwa Mulungu wawo.
Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere;
Iwo sadziwa Yehova.
5 Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa;
Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo;
Yudanso anagwa nawo pamodzi.
6 Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo
kukapereka nsembe kwa Yehova,
iwo sadzamupeza;
Iye wawachokera.
7 Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova;
amabereka ana amʼchigololo
ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano
chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.
8 “Womba lipenga mu Gibeya,
liza mbetete mu Rama.
Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni;
iwe Benjamini tsogolera.
9 Efereimu adzasanduka bwinja
pa tsiku la chilango.
Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi
pakati pa mafuko a Israeli.
10 Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu
amene amasuntha miyala ya mʼmalire.
Ndidzawakhutulira ukali wanga
ngati madzi a chigumula.
11 Efereimu waponderezedwa,
akulangidwa chifukwa chotsatira
mafano.
12 Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu,
ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.
13 “Efereimu ataona nthenda yake,
ndi Yuda ataona zilonda zake,
pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya,
ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza.
Koma mfumuyo singathe kukuchizani,
singathe kuchiritsa mabala anu.
14 Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu.
Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda.
Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo;
ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
15 Ndipo ndidzabwerera ku malo anga
mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo.
Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga;
mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”
Kusalapa kwa Israeli
6 “Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova.
Iye watikhadzula,
koma adzatichiritsa.
Iye wativulaza,
koma adzamanga mabala athu.
2 Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa;
pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa
kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3 Tiyeni timudziwe Yehova,
tiyeni tilimbike kumudziwa Iye.
Adzabwera kwa ife mosakayikira konse
ngati kutuluka kwa dzuwa;
adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe,
ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
4 Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani?
Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda?
Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa,
ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
5 Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga,
ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga;
chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
6 Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe,
ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
7 Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa,
iwo sanakhulupirike kwa Ine.
8 Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa,
okhala ndi zizindikiro za kuphana.
9 Monga momwe mbala zimadikirira anthu,
magulu a ansembe amachitanso motero;
iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu,
kupalamula milandu yochititsa manyazi.
10 Ndaona chinthu choopsa kwambiri
mʼnyumba ya Israeli.
Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere,
ndipo Israeli wadzidetsa.
11 “Kunenanso za iwe Yuda,
udzakolola chilango.
“Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”
7 Pamene ndichiritsa Israeli,
machimo a Efereimu amaonekera poyera
ndiponso milandu ya Samariya sibisika.
Iwo amachita zachinyengo,
mbala zimathyola nyumba,
achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
2 Koma sazindikira kuti Ine
ndimakumbukira zoyipa zawo zonse.
Azunguliridwa ndi zolakwa zawo;
ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.
3 “Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo,
akalonga amasekerera mabodza awo.
4 Onsewa ndi anthu azigololo,
otentha ngati moto wa mu uvuni,
umene wophika buledi sasonkhezera
kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu
akalonga amaledzera ndi vinyo,
ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
6 Mitima yawo ili ngati uvuni;
amayandikira Mulungu mwachiwembu.
Ukali wawo umanyeka usiku wonse,
mmawa umayaka ngati malawi a moto.
7 Onsewa ndi otentha ngati uvuni,
amapha olamulira awo.
Mafumu awo onse amagwa,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.
8 “Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena;
Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
9 Alendo atha mphamvu zake,
koma iye sakuzindikira.
Tsitsi lake layamba imvi
koma iye sakudziwa.
10 Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa,
koma pa zonsezi
iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake
kapena kumufunafuna.
11 “Efereimu ali ngati nkhunda
yopusa yopanda nzeru.
Amayitana Igupto
namapita ku Asiriya.
12 Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga;
ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.
Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi
ndidzawakola.
13 Tsoka kwa iwo,
chifukwa andisiya Ine!
Chiwonongeko kwa iwo,
chifukwa andiwukira!
Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa
koma amayankhula za Ine monama.
14 Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima,
koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo.
Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano,
koma amandifulatira.
15 Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa,
koma amandikonzera chiwembu.
16 Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba;
ali ngati uta woonongeka.
Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga
chifukwa cha mawu awo achipongwe.
Motero iwo adzasekedwa
mʼdziko la Igupto.
Israeli Akolola Kamvuluvulu
8 “Ika lipenga pakamwa pako.
Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova
chifukwa anthu aphwanya pangano langa
ndiponso agalukira lamulo langa.
2 Israeli akulirira kwa Ine kuti,
‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’
3 Koma Israeli wakana zabwino;
mdani adzamuthamangitsa.
4 Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga.
Amasankha akalonga popanda chilolezo changa.
Amadzipangira mafano
asiliva ndi agolide
koma adzawonongeka nawo.
5 Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!
Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.
Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
6 Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!
Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;
si Mulungu amene anamupanga.
Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,
mwana wangʼombe wa ku Samariya.
7 “Aisraeli amadzala mphepo
ndipo amakolola kamvuluvulu.
Tirigu alibe ngala;
sadzabala chakudya.
Akanabala chakudya
alendo akanadya chakudyacho.
8 Israeli wamezedwa,
tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina
ngati chinthu cha chabechabe.
9 Pakuti iwo anapita ku Asiriya
ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha.
Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
10 Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu,
Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.
Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa
ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.
11 “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo,
maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.
12 Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga,
koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.
13 Amapereka nsembe za nyama kwa Ine
ndipo iwo amadya nyamayo,
koma Yehova sakondwera nazo.
Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo
ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:
iwowo adzabwerera ku Igupto.
14 Israeli wayiwala Mlengi wake
ndipo wamanga nyumba zaufumu;
Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.
Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,
moto umene udzatenthe malinga awo.”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Efeso
2 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 2 Ine ndimadziwa zochita zako, ntchito yako yowawa ndi kupirira kwako. Ine ndimadziwa kuti sungalekerere anthu oyipa amene amadzitcha atumwi pamene sichoncho, unawayesa, ndipo unawapeza kuti ndi abodza. 3 Iwe wapirira ndipo wakumana ndi zovuta chifukwa cha dzina langa, ndipo sunatope.
4 Komabe ndili ndi chotsutsana nawe: Wataya chikondi chako chapoyamba. 5 Kumbukirani kuti munagwa kuchokera patali. Lapa ndikuchita zinthu zimene unkachita poyamba. Ngati sulapa ndidzabwera ndikukuchotsera choyikapo nyale chako pamalo pake. 6 Komabe chokomera chako ndi chakuti umadana ndi zochita za Anikolai, zimene Inenso ndimadana nazo.
7 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Simurna
8 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Simurna kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi Woyamba ndi Wotsiriza, amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo. 9 Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. 10 Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
11 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Pergamo
12 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Pergamo kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse. 13 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.
14 Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo. 15 Chimodzimodzinso inuyo muli ndi ena amene amatsatira ziphunzitso za Anikolai. 16 Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.
17 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’ ”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Tiyatira
18 “Lembera mngelo wampingo wa ku Tiyatira kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa Mwana wa Mulungu, amene maso ake ali ngati moto woyaka ndi mapazi ake ngati chitsulo chonyezimira. 19 Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zanu, chikondi chanu ndi chikhulupiriro chanu, kutumikira kwanu ndi kupirira kwanu. Ndikudziwa tsopano kuti ntchito zanu ndi zabwino kuposa zoyamba zija.
20 Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano. 21 Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna. 22 Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo. 23 Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.
24 Tsopano ndikunena kwa enanu a ku Tiyatira, kwa inu amene simunatsate chiphunzitso cha mkaziyo ndipo simunaphunzire zimene iwo amati ndi ‘zinsinsi zonama’ za Satana. Kwa inu mawu anga ndi akuti sindikuwunjikirani malamulo ena. 25 Inu mungogwiritsa zimene munaphunzira basi, mpaka Ine ndidzabwere.
26 Amene adzapambana ndi kuchita chifuniro changa mpaka kumapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu. 27 Adzayilamulira ndi ndodo yachitsulo ndipo nadzayiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi omwe ndinalandira kwa Atate anga. 28 Ine ndidzamupatsanso nthanda, nyenyezi yowala mʼmamawa ija. 29 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.