Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 40-41

Malo Atsopano a Nyumba ya Mulungu

40 Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu. Mʼmasomphenyawo Yehova ananditenga ndi kupita nane ku dziko la Israeli ndipo anandiyika pa phiri lalitali kwambiri, moti ndinaona ngati mzinda. Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera. Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”

Chipata Chakummawa

Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.

Anapita ku chipata chakummawa. Anakwera pa makwerero a nyumbayo, nayeza chiwundo choyamba cha chipatacho; kutalika kwake kunali mamita atatu. Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.

Ndipo iye anayeza khonde la chipata ndipo chinali cha mamita atatu. Anayeza khonde ndipo linali mamita anayi. Mphuthu zake zinali mita imodzi kuchindikira kwake. Khonde lamʼkati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.

10 Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana. 11 Kenaka anayeza chipata cholowera; mulifupi mwake munali mamita asanu ndipo mulitali mwake munali mamita asanu ndi limodzi ndi theka. 12 Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu. 13 Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka. 14 Anayezanso khonde lamʼkati ndipo linali la mamita makumi atatu. Ndipo mozungulira khondelo munali bwalo. Muyesowu sukuphatikiza khonde loyangʼanana ndi bwalo. 15 Kuchokera pa chipata cholowera mpaka ku mapeto a khonde la chipata, kutalika kwake kunali mamita 27. 16 Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.

Bwalo la Kunja

17 Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo. 18 Utali wa mulifupi mwa msewuwo unkayenda mamita 27 kufanana ndi utali wa chipata cholowera. Uwu unali msewu wa mʼmunsi. 19 Tsono, anayeza kutalika kwa bwalo kuyambira chipata cholowera choyamba mpaka polowera pa chipata chakunja cha bwalo la mʼkati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipata Chakumpoto

20 Kenaka munthuyo anayeza mulitali ndi mulifupi mwa chipata chimene chimayangʼana kumpoto, chotulukira kunja. 21 Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 22 Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde. 23 Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipata Chakummwera

24 Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija. 25 Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13. 26 Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma. 27 Bwalo lamʼkati linalinso ndi chipata kummwera. Munthuyo analiyeza kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Zipata Zolowera ku Bwalo la Mʼkati

28 Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija. 29 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake zinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi munali mamita 13. 30 (Khonde lililonse la makonde atatu a zipata zolowera bwalo lamʼkati aja linali la mamita ozungulira mʼbwalo lamʼkati anali mamita 13 mulitali mwake, mamita awiri ndi theka mulifupi mwake). 31 Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

32 Kenaka munthuyo anapita nane ku bwalo la mʼkati mbali ya kummawa, ndipo anayeza chipata cholowera; chinali chofanana ndi zinzake zina zija. 33 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 34 Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

35 Kenaka anapita nane ku chipata chakumpoto ndipo anachiyeza. Chinali chofanana ndi zina zija. 36 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 37 Khonde lake limayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu zake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

Zipinda Zokonzeramo Nsembe

38 Panali chipinda ndipo khomo lake linali pafupi ndi khonde la chipata cholowera chamʼkati. Mʼchipinda mʼmenemo ankatsukira nyama ya nsembe yopsereza. 39 Pa khonde la chipatacho panali matebulo awiri, lina kuno lina uko. Ankapherapo nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula. 40 Panali matebulo anayi, awiri a iwo anali kunja kwa khoma la khonde pafupi ndi makwerero olowera pa chipata chakumpoto ndi awiri enawo anali mbali inayo ya makwerero. 41 Choncho ku mbali imodzi ya chipata kunali matebulo anayi, ndiponso ku mbali inayo kunali matebulo anayi. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pa matebulopo ankapherapo nyama za nsembe zopsereza. 42 Matebulo anayiwa anali a miyala yosema. Lililonse mulitali mwake linali la masentimita 75, mulifupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita makumi asanu. Pa matebulopo amayikapo zipangizo zophera nsembe zopsereza ndi nsembe zina. 43 Choncho pa matebulopo ankayikapo nyama za nsembe zopsereza. Mbedza zitatu zazitali ngati chikhatho amazikoleka pa makoma pozungulira ponse.

Zipinda za Ansembe

44 Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto. 45 Munthuyo anandiwuza kuti, “Chipinda chimene chikuyangʼana kummwera ndi cha ansembe amene amayangʼanira Nyumba ya Mulungu, 46 ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”

47 Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.

Nyumba ya Mulungu

48 Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse. 49 Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.

41 Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake. Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.

Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu. Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”

Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake. Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu. Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.

Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu. Khoma lakunja la zipindazo linali la mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho 10 ndi zipinda za Nyumba ya Mulungu panali bwalo limeneli la mamita khumi kupingasa kwake kuzungulira Nyumba yonse ya Mulungu. 11 Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.

12 Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.

13 Ndipo munthuyo anayeza Nyumba ya Mulungu ndipo mulitali mwake inali mamita makumi asanu. Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu. 14 Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakummawa kwa bwalolo mulifupi mwake munali mamita makumi asanu.

15 Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo, 16 mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa), 17 pamwamba pa khomo lolowera ku malo opatulika amʼkati komanso kuzungulira makoma onse kunja ndi mʼkati, 18 anajambulapo zithunzi za kerubi mmodzi atakhala pakati pa kanjedza muwiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri: 19 imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse. 20 Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.

21 Mphuthu za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu kutalika kwake mbali zonse kunali kofanana. Ndipo kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu china chooneka ngati 22 guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.” 23 Chipinda chachikulu chija chinali ndi zitseko ziwiri. Malo opatulika aja analinso ndi zitseko ziwiri. 24 Chitseko chilichonse chinali ndi zigawo ziwiri zopatukana. 25 Ndipo pa zitsekopo anajambulipo zithunzi za akerubi ndi kanjedza monga zomwe anajambulapo pa makoma. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lamʼkati. 26 Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.

2 Petro 3

Kubwera kwa Ambuye

Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera. Ndikufuna kuti mukumbukire mawu amene anayankhulidwa kale ndi aneneri oyera mtima ndiponso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu analipereka kudzera mwa atumwi.

Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa. Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.” Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi. Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa. Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.

Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

10 Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.

11 Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu 12 pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. 13 Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

14 Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. 15 Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. 16 Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.

17 Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. 18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.