Old/New Testament
Ezekieli Akhala Mlonda
33 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda. 3 Tsono iyeyo amati akaona nkhondo ikubwera amaliza lipenga kuti achenjeze anthuwo. 4 Wina aliyense akamva lipenga koma osasamala, mdani uja akabwera nʼkumupha, ndiye kuti wadziphetsa yekha. 5 Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire. Ndiye kuti wadziphetsa yekha. Akanasamala kuchenjeza kwa mlonda akanapulumuka. 6 Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’
7 “Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Choncho imva mawu amene ndikuyankhula ndipo uwachenjeze. 8 Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 9 Koma ngati uchenjeza munthu woyipa kuti aleke njira zake, ndipo iye osatero, adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma iwe udzapulumutsa moyo wako.
10 “Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ ” 11 Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?
12 “Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’ 13 Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake. 14 Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, 15 monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. 16 Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu.
17 “Komabe anthu a mtundu wako akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, koma makhalidwe awo ndiwo ali osalungama. 18 Ngati munthu wolungama atembenuka ndi kuleka ntchito zake zolungama ndi kuyamba kuchita zoyipa, adzafa nazo. 19 Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo. 20 Koma Inu Aisraeli, mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, inu Aisraeli, Ine ndidzaweruza aliyense wa inu potsata ntchito zake.”
Mbiri ya Kuwonongeka kwa Yerusalemu
21 Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!” 22 Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula.
23 Ndipo Yehova anandiyankhula kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’ 25 Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli? 26 Mumadalira lupanga lanu, mumachita zinthu zonyansa, ndipo aliyense wa inu amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi inu nʼkulandira dzikoli?’
27 “Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri. 28 Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako. 29 Ndikadzasandutsa dzikolo chipululu chifukwa cha zonyansa zimene ankachita, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndine Yehova.’
30 “Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’ 31 Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo. 32 Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito.
33 “Koma zonsezi zikadzachitika, ndipo zidzachitika ndithu, pamenepo adzadziwa kuti mneneri anali pakati pawo.”
Abusa a Israeli
34 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa? 3 Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo. 4 Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza. 5 Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo. 6 Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.
7 “ ‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 8 Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga. 9 Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 10 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.
11 “ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. 12 Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima. 13 Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu. 14 Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli. 15 Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16 Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
17 “ ‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna. 18 Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu? 19 Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu?
20 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda. 21 Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali, 22 tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. 23 Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo. 24 Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula.
25 “ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo. 26 Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso. 27 Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo. 28 Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze. 29 Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso. 30 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 31 Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’ ”
Akulu Ampingo ndi Anyamata mu Mpingo
5 Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. 2 Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. 3 Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. 4 Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
5 Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,
“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”
6 Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. 7 Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
8 Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. 9 Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
10 Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. 11 Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni.
Mawu Otsiriza
12 Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu. 13 Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni. 14 Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.