Old/New Testament
Za Kulangidwa kwa Igupto
30 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.
“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,
‘Kalanga, tsiku lafika!’
3 Pakuti tsiku layandikira,
tsiku la Yehova lili pafupi,
tsiku la mitambo yakuda,
tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
4 Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto
ndipo mavuto adzafika pa Kusi.
Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,
chuma chake chidzatengedwa
ndipo maziko ake adzagumuka.
5 Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.
6 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:
“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa
ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.
Adzaphedwa ndi lupanga
kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”
ndikutero Ine Ambuye Yehova.
7 “ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja
kupambana mabwinja ena onse opasuka,
ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka
kupambana mizinda ina yonse.
8 Nditatha kutentha Igupto
ndi kupha onse omuthandiza,
pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
9 “ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
10 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni
kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
11 Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja
adzabwera kudzawononga dzikolo.
Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto
ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
12 Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo
ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.
Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo
pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.
Ine Yehova ndayankhula.
13 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndidzawononga mafano
ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.
Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,
ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
14 Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,
ndi kutentha mzinda wa Zowani.
Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
linga lolimba la Igupto,
ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
Peluziumu adzazunzika ndi ululu.
Malinga a Thebesi adzagumuka,
ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
adzaphedwa ndi lupanga
ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
pamene ndidzathyola goli la Igupto;
motero kunyada kwake kudzatha.
Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,
ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Farao Watha Mphamvu
20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. 22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. 23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. 26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Mkungudza mu Lebanoni
31 Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,
“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
3 Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,
wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.
Unali wautali,
msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
4 Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,
akasupe ozama ankawutalikitsa.
Mitsinje yake inkayenda
mozungulira malo amene unaliwo
ndipo ngalande zake zinkafika
ku mitengo yonse ya mʼmunda.
5 Choncho unatalika kwambiri
kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.
Nthambi zake zinachuluka
ndi kutalika kwambiri,
chifukwa inkalandira madzi ambiri.
6 Mbalame zonse zamlengalenga
zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.
Nyama zakuthengo zonse
zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.
Mitundu yotchuka ya anthu
inkakhala mu mthunzi wake.
7 Unali wokongola kwambiri,
wa nthambi zake zotambalala,
chifukwa mizu yake inazama pansi
kumene kunali madzi ochuluka.
8 Mʼmunda wa Mulungu munalibe
mkungudza wofanana nawo,
kapena mitengo ya payini
ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.
Munalibenso mtengo wa mkuyu
nthambi zofanafana ndi zake.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse
wofanana ndi iwo kukongola kwake.
9 Ine ndinawupanga wokongola
wa nthambi zochuluka.
Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa
Mulungu inawuchitira nsanje.
10 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake, 11 ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake. 12 Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya. 13 Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake. 14 Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
15 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. 16 Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. 17 Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.
18 “ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.
“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Nyimbo ya Maliro a Farao
32 Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,
“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.
Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.
Umakhuvula mʼmitsinje yako,
kuvundula madzi ndi mapazi ako
ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.
3 “Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,
ndidzakuponyera khoka langa
ndi kukugwira mu ukonde wanga.
4 Ndidzakuponya ku mtunda
ndi kukutayira pansi.
Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,
ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
5 Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri
ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.
6 Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,
mpaka kumapiri komwe,
ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.
7 Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba
ndikudetsa nyenyezi zake.
Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,
ndipo mwezi sudzawala.
8 Zowala zonse zamumlengalenga
ndidzazizimitsa;
ndidzachititsa mdima pa dziko lako,
akutero Ambuye Yehova.
9 Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri
pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
ku mayiko amene iwe sunawadziwe.
10 Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,
ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe
pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.
Pa nthawi ya kugwa kwako,
aliyense wa iwo adzanjenjemera
moyo wake wonse.
11 “ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,
“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni
lidzabwera kudzalimbana nawe.
12 Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe
ndi lupanga la anthu amphamvu,
anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Adzathetsa kunyada kwa Igupto,
ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
13 Ndidzawononga ziweto zake zonse
zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.
Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu
kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
14 Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake
ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,
akutero Ambuye Yehova.
15 Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;
ndikadzawononga dziko lonse
ndi kukantha onse okhala kumeneko,
adzadziwa kuti ndine Yehova.’
16 “Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”
17 Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa. 19 Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’ 20 Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo. 21 Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’
22 “Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo. 23 Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.
24 “Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. 25 Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.
26 “Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. 27 Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.
28 “Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.
29 “Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.
30 “Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.
31 “Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 32 Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Moyo Watsopano
4 Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. 2 Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. 3 Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. 4 Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. 5 Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. 6 Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.
7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. 8 Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. 9 Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. 10 Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu. 11 Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni.
Kumva Zowawa Chifukwa cha Chikhristu
12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu. 15 Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, 16 koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo. 17 Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani? 18 Monga Malemba akuti,
“Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke,
nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”
19 Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.