Old/New Testament
Nyimbo Yodandaulira Turo
27 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo. 3 Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti,
“Iwe Turo, umanena kuti,
‘Ndine wokongola kwambiri.’
4 Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja;
amisiri ako anakukongoletsa kwambiri.
5 Anakupanga ndi matabwa
a payini ochokera ku Seniri;
anatenga mikungudza ya ku Lebanoni
kupangira mlongoti wako.
6 Ndi mitengo ya thundu ya ku Basani
anapanga zopalasira zako;
ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu.
Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu.
7 Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako,
ndipo inakhala ngati mbendera.
Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepo
zochokera ku zilumba za Elisa.
8 Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako.
Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa.
9 Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako,
ngati okonza zibowo zako.
Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa ake
ankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.
10 “Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Puti
anali asilikali mʼgulu lako la nkhondo.
Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako,
kubweretsa kwa iwe ulemerero.
11 Anthu a ku Arivadi ndi Heleki
ankalondera mbali zonse za mpanda wako;
anthu a ku Gamadi
anali mu nsanja zako,
Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse.
Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.
12 “Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
13 “Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
14 “Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.
15 “Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.
16 “Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
17 “Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
18 “Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari. 19 Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.
20 “Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.
21 “Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
22 “Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
23 “Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda. 24 Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
25 “Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali
zonyamula malonda ako.
Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi
yodzaza ndi katundu wolemera.
26 Anthu opalasa ako amakupititsa
pa nyanja yozama.
Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyola
pakati pa nyanja.
27 Chuma chako, katundu wako, malonda ako,
okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi,
anthu ako amalonda ndi asilikali ako onse
ndiponso aliyense amene ali mʼmenemo
adzamira mʼnyanja
tsiku limene udzawonongeka.
28 Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezeka
chifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo.
29 Onse amene amapalasa sitima zapamadzi,
adzatuluka mʼsitima zawo;
oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadzi
adzayimirira mʼmbali mwa nyanja.
30 Iwo akufuwula,
kukulira iwe kwambiri;
akudzithira fumbi kumutu,
ndi kudzigubuduza pa phulusa.
31 Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe
ndipo akuvala ziguduli.
Akukulira iweyo
ndi mitima yowawa kwambiri.
32 Akuyimba nyimbo
yokudandaulira nʼkumati:
‘Ndani anawonongedwapo ngati Turo
pakati pa nyanja?’
33 Pamene malonda ako ankawoloka nyanja
unakhutitsa mitundu yambiri ya anthu.
Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chako
komanso ndi malonda ako.
34 Koma tsopano wathyokera mʼnyanja,
pansi penipeni pa nyanja.
Katundu wako ndi onse amene anali nawe
amira pamodzi nawe.
35 Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanja
aopsedwa ndi zimene zakuchitikira.
Mafumu awo akuchita mantha
ndipo nkhope zangoti khululu.
36 Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola.
Watha mochititsa mantha
ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”
Mawu Odzudzula Mfumu ya Turo
28 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza
umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu;
ndimakhala pa mpando wa mulungu
pakati pa nyanja.’
Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu,
ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
3 Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli.
Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
4 Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako
unadzipezera chuma
ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva
mʼnyumba zosungira chuma chako.
5 Ndi nzeru zako zochitira malonda
unachulukitsa chuma chako
ndipo wayamba kunyada
chifukwa cha chuma chakocho.
6 “ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Popeza umadziganizira
kuti ndiwe mulungu,
7 Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza,
kuti adzalimbane nawe.
Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako,
ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
8 Iwo adzakuponyera ku dzenje
ndipo udzafa imfa yoopsa
mʼnyanja yozama.
9 Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’
pamaso pa iwo amene akukupha?
Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu,
mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
10 Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe
mʼmanja mwa anthu achilendo.
Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’ ”
11 Yehova anandiyankhula kuti: 12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni,
wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
13 Iwe unkakhala ngati mu Edeni,
munda wa Mulungu.
Miyala yokongola ya mitundu yonse:
rubi, topazi ndi dayimondi,
kirisoliti, onikisi, yasipa,
safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako.
Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide.
Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
14 Ndinayika kerubi kuti azikulondera.
Unkakhala pa phiri langa lopatulika,
ndipo unkayendayenda
pakati pa miyala ya moto.
15 Makhalidwe ako anali abwino
kuyambira pamene unalengedwa
mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
16 Unatanganidwa ndi zamalonda.
Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu
ndi kumachimwa.
Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.
Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa
kukuchotsa ku miyala yamoto.
17 Unkadzikuza mu mtima mwako
chifukwa cha kukongola kwako,
ndipo unayipitsa nzeru zako
chifukwa chofuna kutchuka.
Kotero Ine ndinakugwetsa pansi
kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
18 Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.
Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.
Choncho ndinabutsa moto pakati pako,
ndipo unakupsereza,
ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi
pamaso pa anthu onse amene amakuona.
19 Anthu onse amitundu amene ankakudziwa
akuchita mantha chifukwa cha iwe.
Watheratu mochititsa mantha
ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”
Za Chilango cha Sidoni
20 Yehova anandiyankhula nati: 21 “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti, 22 ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,
ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.
Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova
ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti
ndine woyera pakati pako.
23 Ndidzatumiza mliri pa iwe
ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.
Anthu ophedwa ndi lupanga
adzagwa mbali zonse.
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
24 “ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25 “ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. 26 Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”
Za Chilango cha Igupto
29 Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. 3 Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,
iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.
Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;
ndinadzipangira ndekha.’
4 Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako
ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo
pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
5 Ndidzakutaya ku chipululu,
iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.
Udzagwera pamtetete kuthengo
popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya
cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.
6 Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. 7 Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.
8 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. 9 Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10 nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11 Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12 Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.
13 “ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14 Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15 Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16 Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”
Mphotho ya Nebukadinezara
17 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20 Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.
21 “Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Akazi ndi Amuna
3 Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu 2 pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu. 3 Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. 4 Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu. 5 Pakuti umo ndi mmene akazi oyera mtima akale amene anali ndi chiyembekezo pa Mulungu anadzikongoletsera. Iwo ankagonjera amuna awo, 6 monga Sara, amene anamvera Abrahamu namutcha iye mbuye wake. Akazi inu ndinu ana ake ngati muchita zoyenera, ndipo musaope choopsa chilichonse.
7 Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.
Kumva Zowawa Chifukwa cha Chilungamo
8 Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa. 9 Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso. 10 Pakuti,
“Iye amene angakonde moyo
ndi kuona masiku abwino,
aletse lilime lake kuyankhula zoyipa,
ndiponso milomo yake kunena mabodza.
11 Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino.
Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza.
12 Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama
ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo.
Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”
13 Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino? 14 Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.” 15 Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho. 16 Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho. 17 Nʼkwabwino ngati ndi chifuniro cha Mulungu kumva zowawa chifukwa chochita zabwino kusiyana ndi kumva zowawa chifukwa chochita zoyipa. 18 Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu. 19 Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende, 20 ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi. 21 Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu, 22 amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.