Old/New Testament
Yehova Adzudzula Opembedza Mafano
14 Tsiku lina ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kwa ine ndipo anakhala pansi pamaso panga. 2 Ndipo Yehova anandipatsa uthenga uwu nati, 3 “Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse? 4 Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake. 5 Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’
6 “Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa!
7 “ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha. 8 Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
9 “ ‘Ndipo ngati mneneri anyengedwa nanenera, Ine Yehova ndiye ndamunyenga mneneri ameneyo, ndipo ndidzatambasula dzanja langa kumukantha ndi kumuwononga pakati pa anthu anga Aisraeli. 10 Iwo adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Chilango cha wodzafunsira nzeru kwa mneneri chidzafanana ndi chilango cha mneneriyo. 11 Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chilango Chosathawika
12 Yehova anayankhula nane kuti, 13 “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 14 Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
15 “Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo. 16 Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’
17 “Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 18 Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’
19 “Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 20 Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.
21 “Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe! 22 Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu. 23 Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”
Yerusalemu, Mtengo Wamphesa Wosabereka
15 Yehova anayankhulanso nane kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji mtengo wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi ina iliyonse. 3 Mtengo umene uja nʼkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chikhomo chokolekapo zinthu zawo? 4 Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse? 5 Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?
6 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mtengo wamphesa ndidzawuponya mʼmoto monga ndimachitira ndi mitengo ina ya ku nkhalango. Momwemonso ndidzachita ndi anthu a ku Yerusalemu. 7 Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 8 Ine ndidzasandutsa dziko kukhala chipululu chifukwa anthu akhala osakhulupirika, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa
2 Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. 2 Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. 3 Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” 4 kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?
5 Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? 6 Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? 7 Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?
8 Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. 9 Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. 10 Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse. 11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.
12 Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu, 13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.
Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino
14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? 15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. 16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? 17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
18 Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.”
Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino. 19 Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.
20 Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa? 21 Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? 22 Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino. 23 Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. 24 Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi.
25 Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina? 26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.