Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 11-13

Chiweruzo pa Atsogoleri a Israeli

11 Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo. Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo. Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’ ”

Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’ Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo.

“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo. Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye. Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni. 10 Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 11 Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. 12 Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’ ”

13 Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”

14 Yehova anayankhula nane kuti, 15 “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”

Mulungu Alonjeza za Kubwerera kwa Israeli

16 “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’

17 “Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.

18 “Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. 19 Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. 20 Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 21 Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

22 Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 23 Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. 24 Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.

Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. 25 Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.

Chifaniziro cha Otengedwa Ukapolo

12 Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira.

“Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu. Utulutse katundu wako wopita naye ku ukapolo nthawi ya masana iwo akuona. Ndipo nthawi ya madzulo, iwo akuona, uchoke monga ngati ukupita ku ukapolo. Iwo akuona, ubowole pa khoma ndipo utulutsirepo katundu wako. Usenze katundu wako pa phewa iwo akuona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi, pakuti ndakusandutsa iwe chizindikiro chochenjeza Aisraeli.”

Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona.

Mmawa mwake Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu aupandu a Israeli sanakufunse kuti ukuchita chiyani?

10 “Uwawuze kuti, ‘zimene ndikunena Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndi izi: Uthengawu ndi wonena za kalonga wa ku Yerusalemu pamodzi ndi banja lonse la Israeli amene akukhala kumeneko.’ 11 Uwawuze kuti, ‘Ndiwe chizindikiro chowachenjeza.’

“Zidzakuchitikirani monga momwe zakuchitikira iwemu. Iwo adzatengedwa kupita ku ukapolo.”

12 “Kalonga wawo adzatenga katundu wake nʼchisisira nʼkunyamuka. Adzatulukira pa bowo limene anthu anabowola pa khoma. Adzaphimba nkhope yake kuti asaone kumene akupita. 13 Ndidzayala ukonde wanga pa iye ndi kumukola mu msampha wanga. Ndidzabwera naye ku Babuloni, dziko la Akaldeya, koma sadzaliona dzikolo, ndipo adzafera kumeneko. 14 Ine ndidzabalalitsa kumbali zonse zinayi onse okhala naye pafupi, ndiwo omuthandiza ake pamodzi ndi ankhondo ake. Ndidzawalondola ndi lupanga losolola.

15 “Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira ku mayiko ena. 16 Koma ndidzasiyako ena pangʼono amene adzapulumuke ku lupanga, njala ndi mliri, kuti akafotokoze ntchito zawo zonse zonyansa pakati pa anthu achilendo kumene akupitako. Pamenepo adzadziwa kuti ndine Yehova.”

17 Pambuyo pake Yehova anandiyankhulanso nati, 18 “Iwe mwana wa munthu, uzinjenjemera ukamadya chakudya chako, ndipo uzinthunthumira ndi mantha ukamamwa madzi ako. 19 Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo. 20 Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

21 Yehova anayankhulanso nane kuti, 22 “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’ 23 Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi. 24 Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli. 25 Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

26 Yehova anandiyankhula nati: 27 “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’

28 “Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

Mawu Odzudzula Aneneri Onyenga

13 Yehova anayankhulanso nane kuti, “Iwe mwana wa munthu unenere modzudzula aneneri a Israeli amene akunenera za kukhosi kwawo. Uwawuze iwowa kuti, ‘Imvani mawu a Yehova!’ Ambuye Yehova akuti, ‘Tsoka kwa aneneri opusa amene amangonenera zopeka ngakhale kuti sanaone kanthu konse!’ Iwe Israeli, aneneri ako ali ngati nkhandwe pa mabwinja. Simunakwere khoma kuti mukakonze mʼmene munagumuka, kuti Aisraeli adziteteze kolimba pa nkhondo pa tsiku la Yehova. Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi. Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe.

“Tsono Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndikukutsutsani chifukwa cha zoyankhula zanu zonama ndi masomphenya anu abodzawo. Ndikutero Ine Yehova. Ndidzalanga aneneri amene amanenera zabodza za zinthu zimene amati anaziona mʼmasomphenya. Sadzakhala nawo mʼbwalo la anthu anga ndipo mayina awo sadzalembedwa mu kawundula wa nzika za Israeli. Sadzalowa nawo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

10 “Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza, 11 choncho ufotokozere amene alipaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzagwa mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzawomba mphepo yamkuntho. 12 Pamene khomalo lagwa, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza yemwe munapaka uja ali kuti?’

13 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Mwa ukali ndidzakunthitsa mphepo ya mkuntho. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu ndili ndi ukali ndipo ndidzavumbwitsa mvula yamphamvu ndi mkwiyo mpaka khomalo litawonongeka kotheratu. 14 Ndidzagwetsa khoma limene munalipaka njerezalo. Ndidzaligumuliratu mpaka pansi kotero kuti maziko ake adzaoneka. Khomalo likadzagwa, inu mudzawonongekamo; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 15 Kotero ndidzagwiritsa ntchito mkwiyo wanga pa khomali ndi pa amene analipaka njereza. Pambuyo pake ndidzakuwuzani kuti, ‘Khoma lagwa pamodzi ndi amene analipaka njereza. 16 Agwanso aneneri a Yerusalemu amene ankalosa za Yerusalemu nʼkumati anaona mʼmasomphenya za mtendere wa Yerusalemu pamene mtendere kunalibe konse, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.’

17 “Tsono iwe mwana wa munthu, yankhulapo pa nkhani za akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwo amanenera zopeka za mʼmutu mwawo. Tsono adzudzule. 18 Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu? 19 Ponamiza anthu anga amene amamva za mabodza anu, inu mwapha anthu amene sanayenera kufa ndipo mwasiya ndi moyo amene sanayenera kukhala ndi moyo.

20 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame. 21 Ndidzangʼamba nsalu zanu za matsengazo ndi kupulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu, ndipo simudzakhalanso ndi mphamvu yowakolera. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 22 Popeza kuti munatayitsa mtima anthu olungama ngakhale sindinafune kuti ataye mtima; ndipo munalimbitsa anthu oyipa kuti asaleka machimo awo motero sakutha kupulumutsa moyo wawo, 23 choncho inu simudzaonanso masomphenya abodza kapena kuwombeza. Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu. Ndipo pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Yakobo 1

Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu,

kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana.

Landirani moni.

Masautso ndi Mayesero

Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.

Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. 10 Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. 11 Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.

12 Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

13 Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15 Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.

16 Musanyengedwe abale anga okondedwa. 17 Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. 18 Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.

Kumva ndi Kuchita

19 Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. 20 Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. 21 Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.

22 Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. 23 Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. 24 Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. 25 Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.

26 Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. 27 Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.