Old/New Testament
3 Ine ndine munthu amene ndaona masautso
ndi ndodo ya ukali wake.
2 Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa
mu mdima osati mʼkuwala;
3 zoonadi anandikantha ndi dzanja lake
mobwerezabwereza tsiku lonse.
4 Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga,
ndipo waphwanya mafupa anga.
5 Wandizinga ndi kundizungulira
ndi zowawa ndi zolemetsa.
6 Wandikhazika mu mdima
ngati amene anafa kale.
7 Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe,
wandimanga ndi maunyolo.
8 Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo,
amakana pemphero langa.
9 Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema;
ndipo wakhotetsa tinjira tanga.
10 Wandidikirira ngati chimbalangondo,
wandibisalira ngati mkango.
11 Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba,
ndipo wandisiya wopanda thandizo.
12 Wakoka uta wake
ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.
13 Walasa mtima wanga
ndi mivi ya mʼphodo mwake.
14 Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse;
amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.
15 Wandidyetsa zowawa
ndipo wandimwetsa ndulu.
16 Wathyola mano anga ndi miyala;
wandiviviniza mʼfumbi;
17 Wandichotsera mtendere;
ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.
18 Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka
ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”
19 Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala,
zili ngati zowawa ndi ndulu.
20 Ine ndikuzikumbukira bwino izi,
ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.
21 Komabe ndimakumbukira zimenezi,
nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.
22 Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,
ndi chifundo chake ndi chosatha.
23 Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;
kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
24 Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse;
motero ndimamuyembekezera.”
25 Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,
kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;
26 nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha
Yehova modekha.
27 Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli
pamene ali wamngʼono.
28 Akhale chete pa yekha,
chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.
29 Abise nkhope yake mʼfumbi
mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.
30 Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye,
ndipo amuchititse manyazi.
31 Chifukwa Ambuye satayiratu
anthu nthawi zonse.
32 Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo,
chifukwa chikondi chake ndi chosatha.
33 Pakuti sabweretsa masautso mwadala,
kapena zowawa kwa ana a anthu.
34 Kuphwanya ndi phazi
a mʼndende onse a mʼdziko,
35 kukaniza munthu ufulu wake
pamaso pa Wammwambamwamba,
36 kumana munthu chiweruzo cholungama—
kodi Ambuye saona zonsezi?
37 Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika
ngati Ambuye sanavomereze?
38 Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka
mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?
39 Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula
akalangidwa chifukwa cha machimo ake?
40 Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu,
ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.
41 Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu
kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:
42 “Ife tachimwa ndi kuwukira
ndipo inu simunakhululuke.
43 “Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo
mwatitha mopanda chifundo.
44 Mwadzikuta mu mtambo
kotero mapemphero athu sakukufikani.
45 Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala
pakati pa mitundu ya anthu.
46 “Adani anthu atitsekulira pakamwa.
47 Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje,
tapasuka ndi kuwonongedwa.”
48 Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe
chifukwa anthu anga akuwonongedwa.
49 Misozi idzatsika kosalekeza,
ndipo sidzasiya,
50 mpaka Yehova ayangʼane pansi
kuchokera kumwamba ndi kuona.
51 Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi
chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.
52 Akundisaka ngati mbalame,
amene anali adani anga, popanda chifukwa.
53 Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje
ndi kundiponya miyala;
54 madzi anamiza mutu wanga
ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.
55 Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova,
kuchokera mʼdzenje lozama.
56 Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere
kulira kwanga kopempha thandizo.”
57 Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani,
ndipo munati, “Usaope.”
58 Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga;
munapulumutsa moyo wanga.
59 Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira.
Mundiweruzire ndinu!
60 Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo,
chiwembu chawo chonse pa ine.
61 Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo,
chiwembu chawo chonse pa ine,
62 manongʼonongʼo a adani anga
ondiwukira ine tsiku lonse.
63 Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira,
akundinyoza mu nyimbo zawo.
64 Inu Yehova, muwabwezere chowayenera,
chifukwa cha zimene manja awo achita.
65 Phimbani mitima yawo,
ndipo matemberero anu akhale pa iwo!
66 Muwalondole mwaukali ndipo
muwawonongeretu pa dziko lapansi.
4 Haa! Golide wathimbirira,
golide wosalala wasinthikiratu!
Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulika
pamphambano ponse pa mzinda.
2 Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali
amene kale anali ngati golide,
tsopano ali ngati miphika ya dothi,
ntchito ya owumba mbiya!
3 Ngakhale nkhandwe zimapereka bere
kuyamwitsa ana ake,
koma anthu anga asanduka ankhanza
ngati nthiwatiwa mʼchipululu.
4 Lilime la mwana lakangamira kukhosi
chifukwa cha ludzu,
ana akupempha chakudya,
koma palibe amene akuwapatsa.
5 Iwo amene kale ankadya zonona
akupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda.
Iwo amene kale ankavala zokongola
tsopano akugona pa phulusa.
6 Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu
kuposa anthu a ku Sodomu,
amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa
popanda owathandiza.
7 Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana
ndi oyera kuposa mkaka.
Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi,
maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.
8 Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye;
palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda.
Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo;
lawuma gwaa ngati nkhuni.
9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa
amene anafa ndi njala;
chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda
iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.
10 Amayi achifundo afika
pophika ana awo enieni,
ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu
anga anali kuwonongeka.
11 Yehova wakwaniritsa ukali wake;
wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa.
Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni
kuti uwononge maziko ake.
12 Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,
kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,
kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowa
pa zipata za Yerusalemu.
13 Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake
ndi mphulupulu za ansembe ake,
amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.
14 Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda
ngati anthu osaona.
Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi
palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
15 Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”
“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”
Akamathawa ndi kumangoyendayenda,
pakati pa anthu a mitundu yonse amati,
“Asakhalenso ndi ife.”
16 Yehova mwini wake wawabalalitsa;
Iye sakuwalabadiranso.
Ansembe sakulandira ulemu,
akuluakulu sakuwachitira chifundo.
17 Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,
chithandizo chosabwera nʼkomwe,
kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtundu
wa anthu umene sukanatipulumutsa.
18 Anthu ankalondola mapazi athu,
choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda.
Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka,
chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.
19 Otilondola akuthamanga kwambiri
kuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;
anatithamangitsa mpaka ku mapiri
ndi kutibisalira mʼchipululu.
20 Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,
anakodwa mʼmisampha yawo.
Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake
pakati pa mitundu ya anthu.
21 Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.
Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.
Koma iwenso chikho chidzakupeza;
udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;
Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.
Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,
ndi kuyika poyera mphulupulu zako.
5 Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira;
yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.
2 Apereka cholowa chathu kwa obwera,
nyumba zathu kwa alendo.
3 Takhala amasiye ndi wopanda abambo,
amayi athu ali ngati akazi amasiye.
4 Tiyenera kugula madzi amene timamwa,
nkhuni zathunso nʼzogula.
5 Otilondola atigwira pakhosi;
tafowoka ndipo sakutilola kupumula.
6 Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya
kuti tipeze chakudya.
7 Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale,
koma chilango chawo chili pa ife.
8 Akapolo akutilamulira,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.
9 Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe
chifukwa cha lupanga mʼchipululu.
10 Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo,
chifukwa cha kuwawa kwa njala.
11 Amayi agwiriridwa mu Ziyoni,
ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.
12 Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo,
akuluakulu sakuwalemekeza.
13 Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu;
anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.
14 Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda;
achinyamata aleka nyimbo zawo.
15 Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu;
kuvina kwathu kwasanduka maliro.
16 Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu.
Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!
17 Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi,
chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,
18 pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja,
nkhandwe zikungoyendayendapo.
19 Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya;
mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.
20 Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse?
Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?
21 Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere;
mukonzenso masiku athu akhale monga akale,
22 pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu,
ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.
Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro
19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.
35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,
Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,
Ine sindidzakondwera naye.
39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.