Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Maliro 1-2

Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha,
    umene kale unali wodzaza ndi anthu!
Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu!
    Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye.
Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi,
    tsopano wasanduka kapolo.

Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse,
    misozi ili pa masaya pake.
Mwa abwenzi ake onse,
    palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza.
Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu;
    onse akhala adani ake.

Yuda watengedwa ku ukapolo,
    kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa.
Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina;
    ndipo alibe malo opumulira.
Onse omuthamangitsa iye amupitirira,
    ndipo alibe kwina kothawira.

Misewu yopita ku Ziyoni ikulira,
    chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake.
Zipata zake zonse zili pululu,
    ansembe akubuwula.
Anamwali ake akulira,
    ndipo ali mʼmasautso woopsa.

Adani ake asanduka mabwana ake;
    odana naye akupeza bwino.
Yehova wamubweretsera mavuto
    chifukwa cha machimo ake ambiri.
Ana ake atengedwa ukapolo
    pamaso pa mdani.

Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni
    wachokeratu.
Akalonga ake ali ngati mbawala
    zosowa msipu;
alibe mphamvu zothawira
    owathamangitsa.

Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake,
    Yerusalemu amakumbukira chuma chonse
    chimene mʼmasiku amakedzana chinali chake.
Anthu ake atagwidwa ndi adani ake,
    panalibe aliyense womuthandiza.
Adani ake ankamuyangʼana
    ndi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake.

Yerusalemu wachimwa kwambiri
    ndipo potero wakhala wodetsedwa.
Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza,
    chifukwa aona umaliseche wake.
Iye mwini akubuwula
    ndipo akubisa nkhope yake.

Uve wake umaonekera pa zovala zake;
    iye sanaganizire za tsogolo lake.
Nʼchifukwa chake kugwa kwake kunali kwakukulu;
    ndipo analibe womutonthoza.
“Inu Yehova, taonani masautso anga,
    pakuti mdani wapambana.”

10 Adani amulanda
    chuma chake chonse;
iye anaona mitundu ya anthu achikunja ikulowa mʼmalo ake opatulika,
    amene Inu Mulungu munawaletsa
    kulowa mu msonkhano wanu.

11 Anthu ake onse akubuwula
    pamene akufunafuna chakudya;
asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya
    kuti akhale ndi moyo.
“Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani,
    chifukwa ine ndanyozeka.”

12 “Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa?
    Yangʼanani ndipo muone.
Kodi pali mavuto ofanana ndi
    amene andigwerawa,
amene Ambuye anandibweretsera
    pa tsiku la ukali wake?

13 “Anatumiza moto kuchokera kumwamba,
    unalowa mpaka mʼmafupa anga.
Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga
    ndipo anandibweza.
Anandisiya wopanda chilichonse,
    wolefuka tsiku lonse.

14 “Wazindikira machimo anga onse
    ndipo ndi manja ake anawaluka pamodzi.
Machimowa afika pakhosi panga,
    ndipo Ambuye wandithetsa mphamvu.
Iye wandipereka
    kwa anthu amene sindingalimbane nawo.

15 “Ambuye wakana
    anthu anga onse amphamvu omwe ankakhala nane:
wasonkhanitsa gulu lankhondo kuti lilimbane nane,
    kuti litekedze anyamata anga;
mʼmalo ofinyira mphesa Ambuye wapondereza
    anamwali a Yuda.

16 “Chifukwa cha zimenezi ndikulira
    ndipo maso anga adzaza ndi misozi.
Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze,
    palibe aliyense wondilimbitsa mtima.
Ana anga ali okhaokha
    chifukwa mdani watigonjetsa.

17 “Ziyoni wakweza manja ake,
    koma palibe aliyense womutonthoza.
Yehova walamula kuti abale ake
    a Yakobo akhale adani ake;
Yerusalemu wasanduka
    chinthu chodetsedwa pakati pawo.

18 “Yehova ndi wolungama,
    koma ndine ndinawukira malamulo ake.
Imvani inu anthu a mitundu yonse;
    onani masautso anga.
Anyamata ndi anamwali anga
    agwidwa ukapolo.

19 “Ndinayitana abwenzi anga
    koma anandinyenga.
Ansembe ndi akuluakulu anga
    anafa mu mzinda
pamene ankafunafuna chakudya
    kuti akhale ndi moyo.

20 “Inu Yehova, onani mmene ine ndavutikira!
    Ndikuzunzika mʼkati mwanga,
ndipo mu mtima mwanga ndasautsidwa
    chifukwa ndakhala osamvera.
Mʼmisewu anthu akuphedwa,
    ndipo ku mudzi kuli imfa yokhayokha.

21 “Anthu amva kubuwula kwanga,
    koma palibe wonditonthoza.
Adani anga onse amva masautso anga;
    iwo akusangalala pa zimene Inu mwachita.
Lifikitseni tsiku limene munalonjeza lija
    kuti iwonso adzakhale ngati ine.

22 “Lolani kuti ntchito zawo zoyipa zifike pamaso panu;
    muwalange
ngati mmene mwandilangira ine
    chifukwa cha machimo anga onse.
Ndikubuwula kwambiri
    ndipo mtima wanga walefuka.”

Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni
    ndi mtambo wa mkwiyo wake!
Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli
    kuchoka kumwamba.
Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso
    popondapo mapazi ake.

Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo;
mu mkwiyo wake anagwetsa
    malinga a mwana wamkazi wa Yuda.
Anagwetsa pansi mochititsa manyazi
    maufumu ndi akalonga ake.

Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola
    nyanga iliyonse ya Israeli.
Anabweza dzanja lake lamanja
    pamene mdani anamuyandikira.
Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa
    umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.

Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani;
    wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani,
ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira.
Ukali wake ukuyaka ngati moto
    pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.

Ambuye ali ngati mdani;
    wawonongeratu Israeli;
wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu
    ndipo wawononga malinga ake.
Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira
    kwa mwana wamkazi wa Yuda.

Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda;
    wawononga malo ake a msonkhano.
Yehova wayiwalitsa Ziyoni
    maphwando ake oyikika ndi masabata ake.
Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza
    mfumu ndi wansembe.

Ambuye wakana guwa lake la nsembe
    ndipo wasiya malo ake opatulika.
Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu
    kwa mdani wake;
adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova
    ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.

Yehova anatsimikiza kugwetsa
    makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni.
Anawayesa ndi chingwe
    ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa.
Analiritsa malinga ndi makoma;
    onse anawonongeka pamodzi.

Zipata za Yerusalemu zalowa pansi;
    wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake.
Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
    palibenso lamulo,
ndipo aneneri ake sakupeza
    masomphenya kuchokera kwa Yehova.

10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni
    akhala chete pansi;
awaza fumbi pa mitu yawo
    ndipo avala ziguduli.
Anamwali a Yerusalemu
    aweramitsa mitu yawo pansi.

11 Maso anga atopa ndi kulira,
    ndazunzika mʼmoyo mwanga,
mtima wanga wadzaza ndi chisoni
    chifukwa anthu anga akuwonongeka,
chifukwa ana ndi makanda akukomoka
    mʼmisewu ya mu mzinda.

12 Anawo akufunsa amayi awo kuti,
    “Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?”
pamene akukomoka ngati anthu olasidwa
    mʼmisewu ya mʼmizinda,
pamene miyoyo yawo ikufowoka
    mʼmanja mwa amayi awo.

13 Ndinganene chiyani za iwe?
    Ndingakufanizire ndi chiyani,
    iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?
Kodi ndingakufanizire ndi yani
    kuti ndikutonthoze,
    iwe namwali wa Ziyoni?
Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja,
    kodi ndani angakuchiritse?

14 Masomphenya a aneneri ako
    anali abodza ndi achabechabe.
Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo
    poyika poyera mphulupulu zako.
Mauthenga amene anakupatsa
    anali achabechabe ndi osocheretsa.

15 Onse oyenda mʼnjira yako
    akukuwombera mʼmanja;
akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola
    iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu:
“Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa
    wokongola kotheratu,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”

16 Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza;
iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo,
    ndipo akuti, “Tamumeza.
Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera;
    tili ndi moyo kuti tilione.”

17 Yehova wachita chimene anakonzeratu;
    wakwaniritsa mawu ake,
    amene anatsimikiza kale lomwe.
Wakuwononga mopanda chifundo,
    walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako,
    wakweza mphamvu za adani ako.

18 Mitima ya anthu
    ikufuwulira Ambuye.
Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni,
    misozi yako itsike ngati mtsinje
    usana ndi usiku;
usadzipatse wekha mpumulo,
    maso ako asaleke kukhetsa misozi.

19 Dzuka, fuwula usiku,
    pamene alonda ayamba kulondera;
khuthula mtima wako ngati madzi
    pamaso pa Ambuye.
Kweza manja ako kwa Iye
    chifukwa cha miyoyo ya ana ako,
amene akukomoka ndi njala
    mʼmisewu yonse ya mu mzinda.

20 Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani:
    kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi?
Kodi amayi adye ana awo,
    amene amawasamalira?
Kodi ansembe ndi aneneri awaphere
    mʼmalo opatulika a Ambuye?

21 Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi
    pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda;
anyamata anga ndi anamwali anga
    aphedwa ndi lupanga.
Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu;
    mwawapha mopanda chifundo.

22 Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando,
    chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse.
Pa tsiku limene Yehova wakwiya
    palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo;
mdani wanga wawononga
    onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.

Ahebri 10:1-18

Yesu Nsembe ya Anthu Onse

10 Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza. Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,

“Simunafune nsembe kapena zopereka,
    koma thupi munandikonzera.
Simunakondwere nazo nsembe zopsereza
    ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,
    Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”

Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.

11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.

15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,

16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo
    atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,
    ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”

17 Ndipo akutinso:

“Sindidzakumbukiranso konse
    machimo awo ndi zolakwa zawo.”

18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.