Old/New Testament
Chiweruzo pa Adani a Israeli
Ulosi
9 Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki
ndi mzinda wa Damasiko
pakuti maso a anthu ndiponso mafuko onse a Israeli
ali pa Yehova—
2 ndiponso mzinda wa Hamati, umene ukuchita malire ndi dzikoli,
komanso pa Turo ndi Sidoni, ngakhale kuti iwo ndi anzeru kwambiri.
3 Ndipo Turo anadzimangira linga;
wadziwunjikira siliva ngati fumbi,
ndi golide ngati zinyalala za mʼmisewu.
4 Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho
ndi kuwononga mphamvu zake mʼnyanja,
ndipo adzapserera ndi moto.
5 Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha;
Gaza adzanjenjemera ndi ululu,
chimodzimodzinso Ekroni, chifukwa chiyembekezo chake chidzatheratu.
Mfumu ya ku Gaza idzaphedwa
ndipo Asikeloni adzakhala opanda anthu.
6 Mu Asidodi mudzakhala mlendo,
ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisti.
7 Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo,
chakudya choletsedwa mʼmano mwawo.
Amene atsala adzakhala anthu a Mulungu wathu,
adzasanduka atsogoleri mu Yuda,
ndipo Ekroni adzakhala ngati Ayebusi.
8 Koma Ine ndidzalondera Nyumba yanga
ndi kuyiteteza kwa ankhondo osakaza.
Palibenso mdani amene adzagonjetse anthu anga,
pakuti tsopano ndikuwayangʼanira.
Kubwera kwa Mfumu ya Ziyoni
9 Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!
Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu!
Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,
yolungama ndi yogonjetsa adani,
yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu,
pa mwana wamphongo wa bulu.
10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu
ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu,
ndipo uta wankhondo udzathyoka.
Mfumuyo idzabweretsa mtendere pakati pa mitundu ya anthu.
Ulamuliro wake udzayambira ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina,
ndipo kuchokera ku Mtsinje (Yufurate) mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
11 Tsono kunena za iwe, chifukwa cha magazi a pangano lako ndi Ine,
ndidzamasula amʼndende ako, ndidzawatulutsa mʼdzenje lopanda madzi.
12 Bwererani ku malo anu otetezedwa, inu amʼndende achiyembekezo;
ngakhale tsopano ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino mowirikiza.
13 Ndidzakoka Yuda monga ndimakokera uta wanga,
ndipo Efereimu ndiye muvi wake.
Ndidzadzutsa ana ako iwe Ziyoni,
kulimbana ndi ana ako iwe Grisi,
ndipo ndidzakusandutsa iwe lupanga la munthu wankhondo.
Kuoneka kwa Yehova
14 Pamenepo Yehova adzaonekera kwa anthu ake;
mivi yake idzangʼanima ngati chingʼaningʼani.
Ambuye Yehova adzaliza lipenga;
ndipo adzayenda mu mkuntho wochokera kummwera,
15 ndipo Yehova Wamphamvuzonse adzawateteza.
Iwo adzawononga
ndipo adzagonjetsa ndi miyala ya legeni.
Adzamwa magazi ndi kubangula ngati amwa vinyo;
magazi adzayenderera ngati a mʼmbale yowazira magazi
pa ngodya za guwa lansembe.
16 Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa
pakuti anthu ake ali ngati nkhosa.
Adzanyezimira mʼdziko lake
ngati miyala yokongola pa chipewa chaufumu.
17 Taonani chikoka ndi kukongola kwawo!
Tirigu adzasangalatsa anyamata,
ndi vinyo watsopano anamwali.
Yehova Adzasamalira Yuda
10 Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira;
ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula.
Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu,
ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.
2 Mafano amayankhula zachinyengo,
owombeza mawula amaona masomphenya abodza;
amafotokoza maloto onama,
amapereka chitonthozo chopandapake.
Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika
chifukwa chosowa mʼbusa.
3 “Ine ndawakwiyira kwambiri abusa,
ndipo ndidzalanga atsogoleri;
pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira
nkhosa zake, nyumba ya Yuda,
ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.
4 Mu Yuda mudzachokera mwala wapangodya,
mudzachokera chikhomo cha tenti,
mudzachokera uta wankhondo,
mudzachokera mtsogoleri aliyense.
5 Onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo
zoponda mʼmatope a mʼmisewu nthawi yankhondo.
Chifukwa Yehova adzakhala nawo,
adzachita nkhondo ndi kugonjetsa okwera pa akavalo.
6 “Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda
ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe.
Ndidzawabwezeretsa
chifukwa ndawamvera chisoni.
Adzakhala ngati kuti
sindinawakane,
chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo
ndipo ndidzawayankha.
7 Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvu
adzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo.
Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala;
mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.
8 Ndidzaliza mluzu
ndi kuwasonkhanitsa pamodzi.
Ndithu ndawawombola;
adzachulukana ngati poyamba paja.
9 Ndinawamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu,
koma ku mayiko akutaliwo adzandikumbukira.
Iwo pamodzi ndi ana awo adzapulumuka,
ndipo adzabwerera.
10 Ndidzawabweretsa kuchokera ku Igupto
ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya.
Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni,
mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.
11 Adzawoloka nyanja ya masautso;
nyanja yokokoma idzagonja
ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa.
Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha
ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.
12 Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehova
ndipo adzayenda mʼdzina lake,”
akutero Yehova.
11 Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni,
kuti moto unyeketse mikungudza yako!
2 Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa;
mtengo wamphamvu wawonongeka!
Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani;
nkhalango yowirira yadulidwa!
3 Imvani kulira mwachisoni kwa abusa;
msipu wawo wobiriwira wawonongeka!
Imvani kubangula kwa mikango;
nkhalango yowirira ya ku Yorodani yawonongeka!
Abusa Awiri
4 Yehova Mulungu wanga akuti, “Dyetsa nkhosa zimene zikukaphedwa. 5 Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo. 6 Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”
7 Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo. 8 Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu.
Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo. 9 Ndinawuza gulu la nkhosalo kuti, “Sindidzakhalanso mʼbusa wanu. Imene ikufa, ife, ndipo imene ikuwonongeka, iwonongeke, zimene zatsala zizidyana.”
10 Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu. 11 Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.
12 Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
13 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.
14 Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.
15 Pamenepo Yehova anayankhula nane kuti, “Tenganso zida za mʼbusa wopusa. 16 Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.
17 “Tsoka kwa mʼbusa wopandapake,
amene amasiya nkhosa!
Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja!
Mkono wake ufote kotheratu,
diso lake lamanja lisaonenso.”
Kuphedwa kwa Adani a Yerusalemu
Ulosi
12 Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti, 2 “Taonani, ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala chakumwa choledzeretsa chimene chidzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomuzungulira. Yuda adzazingidwa pamodzinso ndi Yerusalemu. 3 Pa tsiku limenelo, pamene mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi idzasonkhana kulimbana naye, ndidzasandutsa Yerusalemu thanthwe losatheka kusunthidwa ndi mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kumusuntha adzadzipweteka. 4 Pa tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamuchititsa mantha kuti asokonezeke, ndipo wokwerapo wake ndidzamuchititsa misala,” akutero Yehova. “Ndidzayangʼanira nyumba ya Yuda koma ndidzachititsa khungu akavalo onse a anthu a mitundu ina. 5 Pamenepo atsogoleri a Yuda adzayankhula mʼmitima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu ndi amphamvu, chifukwa Yehova Wamphamvuzonse ndiye Mulungu wawo.’
6 “Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake.
7 “Yehova adzapulumutsa malo okhala Yuda poyamba, kuti ulemu wa nyumba ya Davide ndi wa anthu okhala mu Yerusalemu usapambane ulemu wa Yuda. 8 Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera. 9 Pa tsiku limenelo ndidzawononga mitundu yonse yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu.
Kulirira amene Anamulasa
10 “Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa. 11 Pa tsiku limenelo mudzakhala kulira kwakukulu mu Yerusalemu, monga kulira kwa ku Hadadi-Rimoni ku chigwa cha Megido. 12 Dziko lidzalira kwambiri, fuko lililonse pa lokha, akazi awo pa okhanso: fuko la Davide pamodzi ndi akazi awo, fuko la Natani pamodzi ndi akazi awo, 13 nyumba ya Levi pamodzi ndi akazi awo, fuko la Simei pamodzi ndi akazi awo, 14 ndiponso mafuko onse pamodzi ndi akazi awo.
Zaka 1,000
20 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. 2 Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000. 3 Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe.
4 Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000. 5 (Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba. 6 Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.
Kugonjetsedwa kwa Satana
7 Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ku ndende yake 8 ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 9 Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa. 10 Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya.
Chiweruzo Chotsiriza
11 Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. 12 Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. 13 Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. 14 Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. 15 Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.