Old/New Testament
Phiri la Yehova
4 Mʼmasiku otsiriza,
phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse.
Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko.
2 Mayiko ambiri adzabwera ndikunena kuti,
“Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova,
ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
3 Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri
ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
kapena kuphunziranso za nkhondo.
4 Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa
ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu,
ndipo palibe amene adzawachititse mantha,
pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula.
5 Mitundu yonse ya anthu
itha kutsatira milungu yawo;
ife tidzayenda mʼnjira za Yehova
Mulungu wathu mpaka muyaya.
Cholinga cha Yehova
6 “Tsiku limenelo, Yehova akuti,
“ndidzasonkhanitsa olumala;
ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa
ndiponso amene ndinawalanga.
7 Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala.
Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.
Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova
kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.
8 Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga,
iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni,
ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe;
ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”
9 Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula,
kodi ulibe mfumu?
Kodi phungu wako wawonongedwa,
kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?
10 Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,
ngati mayi pa nthawi yake yobereka,
pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda
ndi kugona kunja kwa mzindawo.
Udzapita ku Babuloni;
kumeneko udzapulumutsidwa,
kumeneko Yehova adzakuwombola
mʼmanja mwa adani ako.
11 Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu
yasonkhana kulimbana nawe.
Iwo akuti, “Tiyeni timudetse,
maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”
12 Koma iwo sakudziwa
maganizo a Yehova;
iwo sakuzindikira cholinga chake,
Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu.
13 “Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,
pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo;
ndidzakupatsa ziboda zamkuwa
ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.”
Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova,
chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.
Wolamulira Wochokera ku Betelehemu
5 Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo,
pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe.
Adzakantha ndi ndodo pa chibwano
cha wolamulira wa Israeli.
2 “Koma iwe Betelehemu Efurata,
ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda,
mwa iwe mudzatuluka
munthu amene adzalamulira Israeli,
amene chiyambi chake nʼchakalekale,
nʼchamasiku amakedzana.”
3 Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa
mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire.
Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera
kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.
4 Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zake
mwa mphamvu ya Yehova,
mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake.
Ndipo iwo adzakhala mu mtendere,
pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi.
5 Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo.
Chipulumutso ndi Chiwonongeko
Asiriya akadzalowa mʼdziko lathu
ndi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa,
tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri,
ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu.
6 Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga,
dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo.
Adzatipulumutsa kwa Asiriya
akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu
kudzatithira nkhondo.
7 Otsalira a Yakobo adzakhala
pakati pa mitundu yambiri ya anthu
ngati mame ochokera kwa Yehova,
ngati mvumbi pa udzu,
omwe sulamulidwa ndi munthu
kapena kudikira lamulo la anthu.
8 Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu,
mʼgulu la anthu a mitundu yambiri,
ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango.
Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa,
amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula,
ndipo palibe angathe kuzilanditsa.
9 Mudzagonjetsa adani anu,
ndipo adani anu onse adzawonongeka.
10 Yehova akuti,
“Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse
ndi kuphwasula magaleta anu.
11 Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu
ndi kugwetsa malinga anu onse.
12 Ndidzawononga ufiti wanu
ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula.
13 Ndidzawononga mafano anu osema
pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu;
simudzagwadiranso zinthu zopanga
ndi manja anu.
14 Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu,
ndipo ndidzawononga mizinda yanu.
15 Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiya
mitundu imene sinandimvere Ine.”
Mayi ndi Chinjoka
12 Chizindikiro chachikulu chinaoneka kuthambo; mayi atavala dzuwa, mapazi ake ataponda mwezi, pamutu pake pali chipewa chaufumu chokhala ndi nyenyezi khumi ndi ziwiri. 2 Mayiyo anali woyembekezera ndipo pa nthawi yake yochira analira mokuwa chifukwa cha ululu wakubala. 3 Kenaka ku thambo kunaonekanso chizindikiro china; chinjoka chachikulu kwambiri, chofiira chomwe chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi; pamutu uliwonse chitavala chipewa chaufumu. 4 Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye. 5 Mayiyo anabereka mwana wamwamuna amene adzalamulira anthu a mitundu ina yonse ndi ndodo yachitsulo. Ndipo mwanayo analandidwa ku dzanja la mayiyo ndi kupita naye kwa Mulungu ku mpando wake waufumu. 6 Mayiyo anathawira ku chipululu ku malo kumene Mulungu anamukonzera, kumene akasamalidweko masiku 1,260.
7 Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso. 8 Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako. 9 Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.
10 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti,
“Tsopano chipulumutso, mphamvu,
ufumu wa Mulungu wathu
ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera.
Pakuti woneneza abale athu uja,
amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku,
wagwetsedwa pansi.
11 Abale athuwo anamugonjetsa
ndi magazi a Mwana Wankhosa
ndiponso mawu a umboni wawo.
Iwo anadzipereka kwathunthu,
moti sanakonde miyoyo yawo.
12 Choncho, kondwerani, inu dziko lakumwamba
ndi onse okhala kumeneko!
Koma tsoka dziko lapansi ndi nyanja
chifukwa Mdierekezi wagwetsedwa kwa inu!
Iye wadzazidwa ndi ukali
chifukwa akudziwa kuti nthawi yake ndi yochepa.”
13 Pamene chinjokacho chinaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chinayamba kuthamangitsa mayi uja amene anali atabala mwana wamwamunayu. 14 Mayiyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athawire ku malo ake aja a ku chipululu. Kumeneko adzasamalidwako zaka zitatu ndi theka kuti chinjoka chija chisamupeze. 15 Kenaka chinjoka chija chinalavulira mayiyo madzi ambiri ngati mtsinje, kuti madziwo amukokolole. 16 Koma dziko lapansi linamuthandiza mayiyo. Nthaka inatsekuka ndi kumeza mtsinje uja unachokera mʼkamwa mwa chinjokacho. 17 Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.
18 Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.