Old/New Testament
Dzombe, Moto ndi Chingwe Chowongolera Khoma
7 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. 2 Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
3 Kotero Yehova anakhululuka.
Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”
4 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko. 5 Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
6 Kotero Yehova anakhululuka.
Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”
7 Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma. 8 Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?”
Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.”
Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.
9 “Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa
ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja;
ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”
Amosi ndi Amaziya
10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo. 11 Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi:
“ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga,
ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo,
kutali ndi dziko lake.’ ”
12 Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa. 13 Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”
14 Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’ 16 Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti,
“ ‘Usanenere zotsutsa Israeli,
ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”
17 “Tsono zimene akunena Yehova ndi izi:
“ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu,
ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga.
Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa,
ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu.
Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,
kutali ndi dziko lake.’ ”
Dengu la Zipatso Zakupsa
8 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa. 2 Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?”
Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.”
Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.
3 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”
4 Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa
ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.
5 Mumanena kuti,
“Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti
kuti tigulitse zinthu?
Ndipo tsiku la Sabata litha liti
kuti tigulitse tirigu,
kuti tichepetse miyeso,
kukweza mitengo
kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
6 tigule osauka ndi ndalama zasiliva
ndi osowa powapatsa nsapato,
tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”
7 Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.
8 “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi,
ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni?
Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo;
lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata
ngati mtsinje wa ku Igupto.
9 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti,
“Ndidzadetsa dzuwa masana
ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.
10 Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni
ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro.
Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu
ndi kumeta mipala mitu yanu.
Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo,
ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
11 “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti,
“Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;
osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,
koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12 Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina.
Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa,
kufunafuna mawu a Yehova,
koma sadzawapeza.
13 “Tsiku limenelo
“anamwali okongola ndi anyamata amphamvu
adzakomoka ndi ludzu.
14 Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya,
kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’
kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’
Iwowo adzagwa
ndipo sadzadzukanso.”
Israeli Adzawonongedwa
9 Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati:
“Kantha mitu ya nsanamira
kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke.
Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse,
onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe,
palibe amene adzapulumuke.
2 Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa,
dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko.
Ngakhale atakwera kumwamba
Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko.
3 Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli,
Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira.
Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu,
ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
4 Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo,
ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko.
Ndidzawayangʼanitsitsa
kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”
5 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka,
onse amene amakhala mʼmenemo amalira.
Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo,
kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
6 Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba,
ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi,
Iye amene amayitana madzi a ku nyanja
ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi,
dzina lake ndiye Yehova.
7 “Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli
chimodzimodzi ndi Akusi?”
Akutero Yehova.
“Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto,
Afilisti ku Kafitori
ndi Aaramu ku Kiri?
8 “Taonani, maso a Ambuye Yehova
ali pa ufumu wochimwawu.
Ndidzawufafaniza
pa dziko lapansi.
Komabe sindidzawononga kotheratu
nyumba ya Yakobo,”
akutero Yehova.
9 “Pakuti ndidzalamula,
ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli
pakati pa mitundu yonse ya anthu
monga momwe amasefera ufa mʼsefa,
koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
10 Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga
adzaphedwa ndi lupanga,
onse amene amanena kuti,
‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
11 “Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa
nyumba ya Davide imene inagwa.
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,
ndi kuyimanganso
monga inalili poyamba,
12 kuti adzatengenso otsala a Edomu
ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,”
akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.
13 Yehova akunena kuti
“Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola
ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu.
Mapiri adzachucha vinyo watsopano
ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
14 Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli;
mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo.
Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake;
adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
15 Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo,
ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko
limene Ine ndawapatsa,”
akutero Yehova Mulungu wako.
Kutsekulidwa kwa Chimatiro Chachisanu ndi Chiwiri
8 Atatsekula chomatira chachisanu ndi chiwiri, kumwamba kunakhala chete mphindi makumi atatu.
2 Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri aja amene amayimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi awiri.
3 Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu. 4 Fungo la lubani pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima zinakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo. 5 Kenaka mngeloyo anatenga chofukizira nachidzaza ndi moto wochokera pa guwa lansembe ndi kuponya pa dziko lapansi ndipo nthawi yomweyo panachitika mabingu, phokoso, mphenzi ndi chivomerezi.
Malipenga
6 Angelo asanu ndi awiri anakonzekera kuyimba malipenga asanu ndi awiri.
7 Mngelo woyamba anayimba lipenga lake ndipo kunabwera matalala ndi moto wosakanizana ndi magazi ndipo unaponyedwa pa dziko lapansi. Gawo limodzi la magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi la magawo atatu a mitengo linapsa ndi gawo limodzi la magawo atatu a udzu wauwisi linapsanso.
8 Mngelo wachiwiri anayimba lipenga lake, ndipo chinthu china chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto, chinaponyedwa mʼnyanja. Gawo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka magazi. 9 Gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zonse zamoyo za mʼnyanja, linafa, ndipo gawo limodzi la sitima za pamadzi linawonongedwa.
10 Mngelo wachitatu anayimba lipenga lake, ndipo nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muni inachoka kumwamba nigwera pa gawo limodzi la magawo atatu a mitsinje ndi pa akasupe amadzi. 11 Dzina la nyenyeziyo ndi Chowawa. Gawo limodzi la magawo atatu a madzi anasanduka owawa ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha madzi owawawo.
12 Mngelo wachinayi anayimba lipenga lake, ndipo chimodzi cha zigawo zitatu za dzuwa, za mwezi ndi za nyenyezi zinamenyedwa kotero chimodzi mwa zitatu za zonsezi zinada. Panalibenso kuwala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
13 Ndinayangʼananso ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chimene chinkawuluka mlengalenga kwambiri chikuyankhula mofuwula kuti, “Tsoka, Tsoka! Tsoka lalikulu kwa anthu okhala mʼdziko lapansi, angelo otsala aja akangoyimba malipenga awo!”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.