Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 47-48

Mtsinje Wotuluka Mʼnyumba ya Mulungu

47 Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.

Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”

Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. 10 Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. 11 Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. 12 Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”

Malire a Dziko

13 Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri. 14 Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu.

15 “Malire a dzikolo adzakhala motere:

Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi, 16 Berota ndi Sibraimu (mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati mpaka kukafika ku Hazeri Hatikoni mzinda umene uli mʼmalire mwa Haurani. 17 Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto.

18 Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa.

19 Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera.

20 Mbali ya kumadzulo, malire adzakhala Nyanja Yayikulu mpaka pa malo oyangʼanana ndi Lebo Hamati. Awa adzakhala malire akumadzulo.”

21 “Mugawane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israeli. 22 Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli. 23 Mu fuko lililonse kumene mlendoyo akukhala mumupatse cholowa chake.” Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

Magawidwe ka Dziko

48 “Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.

“Aseri adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Dani kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Nafutali adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Aseri kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Manase adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Nafutali kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Efereimu adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Manase kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Rubeni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Efereimu kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Yuda adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Rubeni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.

“Chigawo chapadera chimene mudzachipereke kwa Yehova mulitali mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. 10 Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. 11 Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera. 12 Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.

13 “Moyandikana ndi chigawo cha ansembe, Alevi adzakhala ndi dera lawo lotalika makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Kutalika kwake konse kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. 14 Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ichi ndi chigawo chabwino kwambiri ndipo chisapatsidwe kwa anthu ena, chifukwa ndi chopatulikira Yehova.

15 “Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati. 16 Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250. 17 Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125. 18 Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda. 19 Anthu ogwira ntchito mu mzinda amene adzalime mʼmundamo adzachokera ku mafuko onse a Israeli. 20 Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.

21 “Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu. 22 Choncho chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zidzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo kwa dziko la Benjamini.

23 “Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: Benjamini adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo.

24 “Simeoni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Benjamini kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

25 “Isakara adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Simeoni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

26 “Zebuloni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Isakara kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

27 “Gadi adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Zebuloni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

28 “Malire a Gadi a mbali yakummwera ku Negevi adzayenda kuchokera ku Tamara mpaka ku dziwe la Meriba Kadesi komanso kuchokera ku Mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.

29 “Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.

Zipata za Mzinda

30 “Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250, 31 kudzakhale zipata zitatu izi: cha Rubeni, cha Yuda ndi cha Levi.

32 “Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani.

33 “Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.

34 “Mbali ya kumadzulo, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250 kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Gadi, chipata cha Aseri ndi chipata cha Nafutali.

35 “Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000.

“Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala:

Yehova Ali Pano.”

1 Yohane 3

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo. Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.

Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama. Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi. Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. 10 Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.

Kukondana Wina ndi Mnzake

11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. 17 Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? 18 Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi. 19 Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu, 20 nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.

21 Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu. 22 Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa. 23 Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira. 24 Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.