Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 24-26

Mʼphika Wophikira

24 Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino. Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Ikani mʼphika pa moto,
    ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi.
Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama,
    nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba.
Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri.
    Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri.
Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo.
    Madzi awire.
    Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’

“ ‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi,
    tsoka kwa mʼphika wadzimbiri;
    dzimbiri lake losachoka!
Mutulutsemo nthuli imodzimodzi
    osasankhulapo.

“ ‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo.
    Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala.
Sanawakhutulire pa dothi
    kuopa kuti fumbi lingawafotsere.
Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalala
    kuti asafotseredwe ndi fumbi
    chifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi!
    Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni.
10 Choncho wonjeza nkhuni
    ndipo muyatse moto.
Phikani nyamayo bwinobwino,
    muthiremo zokometsera,
    mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo.
11 Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwo
    mpaka utenthe kuchita kuti psuu
kuti zonyansa zake zisungunuke
    ndi kuti dzimbiri lake lichoke.
12 Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa.
    Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchoka
    ngakhale ndi moto womwe.

13 “ ‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe.

14 “ ‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Imfa ya Mkazi wa Ezekieli

15 Yehova anandiyankhula kuti: 16 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi. 17 Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.”

18 Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira.

19 Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?”

20 Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti, 21 ‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga. 22 Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa. 23 Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu. 24 Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’

25 “Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi. 26 Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo. 27 Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Za Chilango cha Aamoni

25 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira anthu a ku Amoni ndipo unenere mowadzudzula. Awawuze kuti, ‘Inu anthu a ku Amoni, imvani zimene Ambuye Yehova akunena. Iye akuti: Inu munanena mawu onyoza pamene Nyumba yanga yopatulika inkayipitsidwa. Munanyozanso dziko la Israeli pamene linaguga ndiponso anthu a ku Yuda pamene anatengedwa ukapolo. Nʼchifukwa chake Ine ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu akummawa ngati cholowa chawo. Iwo adzamanga misasa yawo ndi kukhoma matenti awo pakati panu. Adzadya zipatso zanu ndi kumwa mkaka wanu. Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira ndi mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu munawomba mʼmanja ndi kumalumphalumpha. Munkakondwa mu mtima mwanu pamene munkanyoza dziko la Israeli. Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’ ”

Za Chilango cha Mowabu

“Ambuye Yehova akuti, ‘Anthu a ku Mowabu ndi a ku Seiri ananena kuti anthu a ku Yuda ali ngati mayiko ena onse.’ Nʼchifukwa chake ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, kuyambira ku mizinda yake ya kumalire; mizinda yokongola ya Beti-Yesimoti, Baala-Meoni ndi Kiriataimu. 10 Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni mʼmanja mwa anthu akummawa kotero kuti Aamoni adzayiwalikiratu pakati pa anthu a mitundu ina. 11 Ndidzawalangadi Amowabuwo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Za Chilango cha Edomu

12 “Ambuye Yehova akuti, ‘Pakuti Edomu analipsira Ayuda, ndiye kuti analakwa kwambiri pochita zimenezi. 13 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kulanga Edomu ndi kupha anthu ake ndiponso nyama zawo. Ndidzawonongeratu Edomu ndipo adzaphedwa ndi lupanga kuchokera ku Temani mpaka ku Dedani. 14 Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraeli. Adzalanga anthu a ku Edomu molingana ndi mkwiyo ndi ukali wanga. Choncho adzaona kulipsira kwanga akutero Ambuye Yehova.’ ”

Za Chilango cha Filisitiya

15 “Ambuye Yehova akuti, ‘Afilisti analanga anthu anga mwankhanza ndi kuwalipsira. 16 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kukantha Afilistiwo. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga iwo amene amakhala mʼmbali mwa nyanja. 17 Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Za Chilango cha Turo

26 Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja. Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala. Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe. Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. 10 Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa. 11 Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa. 12 Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja. 13 Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. 14 Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.

15 “Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako. 16 Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera. 17 Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:

“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,
    wodzaza ndi anthu a ku nyanja!
Unali wamphamvu pa nyanja,
    iwe ndi nzika zako;
unkaopseza anthu onse amene
    ankakhala kumeneko.
18 Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera
    chifukwa cha kugwa kwako;
okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu
    chifukwa cha kugwa kwako.’

19 “Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize. 20 Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo. 21 Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”

1 Petro 2

Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse. Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu, pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino.

Mwala wa Moyo ndi Anthu Osankhidwa

Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti,

“Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni,
    wosankhika ndi wamtengowapatali.
Amene akhulupirira Iye
    sadzachititsidwa manyazi.”

Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira,

“Mwala umene amisiri anawukana
    wasanduka mwala wa maziko,

ndi

“Mwala wopunthwitsa anthu
    ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.”

Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.

Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa. 10 Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.

11 Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu. 12 Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.

Kugonjera Olamulira

13 Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu, 14 kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino. 15 Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa. 16 Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu. 17 Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu.

Akapolo

18 Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza. 19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo. 20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu. 21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.

22 “Iye sanachite tchimo
    kapena kunena bodza.”

23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama. 24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa. 25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.