Old/New Testament
34 Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,
2 “Imvani mawu anga, inu anthu anzeru;
tcherani khutu inu anthu ophunzira.
3 Pakuti khutu limayesa mawu
monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.
4 Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera;
tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.
5 “Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa,
koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
6 Ngakhale ndine wolungama mtima,
akundiyesa wabodza;
ngakhale ndine wosachimwa,
mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’
7 Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani,
amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?
8 Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa;
amayanjana ndi anthu oyipa mtima.
9 Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu
poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’
10 “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu.
Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe,
Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.
11 Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake;
Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.
12 Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa,
kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.
13 Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani?
Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?
14 Mulungu akanakhala ndi maganizo
oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,
15 zamoyo zonse zikanawonongekeratu
ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.
16 “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi;
mvetserani zimene ndikunena.
17 Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira?
Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?
18 Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’
ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’
19 Iye sakondera akalonga
ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka,
pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?
20 Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku;
anthu amachita mantha ndipo amamwalira;
munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.
21 “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu;
amaona mayendedwe ake onse.
22 Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani
kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.
23 Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu,
kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
24 Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu
ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.
25 Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo
amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.
26 Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo,
pamalo pamene aliyense akuwaona;
27 Chifukwa anasiya kumutsata
ndipo sasamaliranso njira zake zonse.
28 Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake,
kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.
29 Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa?
Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe?
Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,
30 kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza,
kuti asatchere anthu misampha.
31 “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti,
‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,
32 ndiphunzitseni zimene sindikuziona
ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’
33 Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira,
pamene inu mukukana kulapa?
Chisankho nʼchanu, osati changa;
tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
34 “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana,
anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
35 ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru;
mawu ake ndi opanda fundo.’
36 Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto
chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
37 Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira;
amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu,
ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”
35 Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,
2 “Kodi mukuganiza kuti mukukhoza?
Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’
3 Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani,
ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’
4 “Ine ndikufuna ndikuyankheni inu
pamodzi ndi abwenzi anu omwe.
5 Yangʼanani kumwamba ndipo muone
mitambo imene ili kutali ndi inuyo.
6 Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani?
Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?
7 Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani?
Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?
8 Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo,
ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.
9 “Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa;
akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.
10 Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga,
amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,
11 amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi
ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’
12 Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye
chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.
13 Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake;
Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.
14 Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti
Iye saona zimene zikuchitika.
Iye adzaweruza molungama ngati
inu mutamudikira
15 ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango,
zoyipa zambiri zimene anthu amachita,
16 abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake,
mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”
Msonkhano wa ku Yerusalemu
15 Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.” 2 Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi. 3 Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse. 4 Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.
5 Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.”
6 Atumwi ndi akulu ampingo anasonkhana kuti akambirane za nkhaniyi. 7 Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira. 8 Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro. 10 Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza? 11 Osatero! Ife tikukhulupirira kuti tinapulumutsidwa mwachisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, monga iwonso anachitira.”
12 Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo. 13 Iwo atatha kuyankhula, Yakobo anayankhula nati: “Abale, tandimverani. 14 Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake. 15 Mawu a aneneri akuvomereza zimenezi, monga kwalembedwa kuti,
16 “ ‘Zitatha izi Ine ndidzabwerera
ndipo ndidzamanganso nyumba ya Davide imene inagwa.
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,
ndi kuyimanganso,
17 kuti anthu otsalawo afunefune Ambuye,
ndi anthu onse a mitundu ina amene atchedwa ndi dzina langa,
akutero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi
18 zinaululidwa kuyambira kalekale.’
19 “Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu. 20 Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi. 21 Pakuti malamulo a Mose akhala akulalikidwa mu mzinda uliwonse, kuyambira kalekale ndipo amawerengedwa mʼMasunagoge tsiku la Sabata.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.