Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Estere 6-8

Mordekai Apatsidwa Ulemu

Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.

Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?”

Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.”

Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera.

Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.”

“Mulowetseni,” Mfumu inalamulira.

Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?”

Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ”

10 Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.”

11 Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!”

12 Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. 13 Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira.

Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” 14 Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza.

Hamani Aphedwa

Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”

Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”

Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”

Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”

Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi. Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake.

Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo.

Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?”

Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani. Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.”

Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” 10 Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika.

Lamulo la Mfumu Lothandiza Ayuda

Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani.

Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake.

Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?”

Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.”

Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. 10 Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu.

11 Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. 12 Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. 13 Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo.

14 Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa.

15 Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. 16 Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. 17 Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.

Machitidwe a Atumwi 6

Asankha Atumiki Asanu ndi Awiri

Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira. Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”

Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya. Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja.

Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira.

Ayuda Agwira Stefano

Stefano, munthu wodzazidwa ndi chisomo cha Mulungu ndi mphamvu anachita zodabwitsa ndiponso zizindikiro zazikulu pakati pa anthu. Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano. 10 Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.

11 Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.”

12 Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu. 13 Iwo anabweretsa mboni zonama zimene zinati, “Munthu uyu akupitirirabe kuyankhula mawu onyoza malo oyera ndi malamulo. 14 Pakuti tinamumva akunena kuti Yesu uja wa ku Nazareti adzawononga malo ano ndiponso kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”

15 Onse amene anakhala pansi Mʼbwalo Lalikulu anamuyangʼanitsitsa Stefano, ndipo anaona kuti nkhope yake ikuwala ngati ya mngelo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.